Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 7/15 tsamba 25-29
  • “Kuweruza mwa Kufufuza”—Kodi Nchiphunzitso cha Baibulo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Kuweruza mwa Kufufuza”—Kodi Nchiphunzitso cha Baibulo?
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Iko Nchiyani?
  • Mawu Akukanika Kugwirizana
  • Kodi Mavesi Enawo Amavumbulanji?
  • Mayankho Odabwitsa
  • Kodi Buku la Ahebri Lingathandize?
  • Mavuto ndi Kukanika Kuwathetsa
  • Yehova Alonjeza Danieli Mphotho Yodabwitsa
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Buku la Danieli ndi Inu
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Kuzindikira Alambiri Oona M’nthaŵi ya Chimaliziro
    Samalani Ulosi wa Danieli!
  • Alimbikitsidwa ndi Mthenga Wochokera kwa Mulungu
    Samalani Ulosi wa Danieli!
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 7/15 tsamba 25-29

“Kuweruza mwa Kufufuza”​—Kodi Nchiphunzitso cha Baibulo?

OCTOBER 22, 1844, linali tsiku limene anthu 50,000 anali kudikira mwachidwi pa Gombe Lakummaŵa la United States. Mtsogoleri wa tchalitchi chawo, William Miller, anali atawauza kuti Yesu Kristu adzabwera tsiku limenelo. Otchedwa Amila amenewo, anayembekezera m’malo awo osonkhanira osiyanasiyana mpaka usiku. Mpaka kunacha mbe, koma Ambuyeyo osafika iyayi. Ataona kuti asokeretsedwa, anabwerera kwawo ndiyeno pambuyo pake tsikulo analitcha “Kugwiritsa Mwala Kwakukulu.”

Komabe, kugwiritsidwa mwalako kunasanduka chiyembekezo. Mkazi wina wotchedwa Ellen Harmon anauza kagulu ka Amila ena, nawachititsa kukhulupirira kuti Mulungu anamvumbulira mwa masomphenya kuti iwo anali ataŵerengera nthaŵi molondola. Anakhulupirira kuti patsiku limenelo zazikulu zinali zitachitika​—Kristu anali ataloŵa ‘m’malo opatulikitsa a kachisi wakumwamba.’

Patapita zaka zoposa khumi, mlaliki wa Adventist, James White (yemwe anakwatira Ellen Harmon) anapeka mawu ofotokoza ntchito ya Kristu kuyambira October 1844. M’magazini yakuti Review and Herald ya January 29, 1857, White anati Yesu anali atayamba “kuweruza mwa kufufuza.” Ndipo chimenechi chakhala chiphunzitso chachikulu cha anthu ngati mamiliyoni asanu ndi aŵiri amene amadzitcha a Seventh-Day Adventist.

Komabe, akatswiri ena olemekezeka azamaphunziro m’Tchalitchi cha Seventh-Day Adventist (SDA) akhala akukayikira ngati “kuweruza mwa kufufuza” chilidi chiphunzitso cha Baibulo. Kodi nchifukwa ninji akuchikayikira? Inuyo mukanakhala wa Seventh-Day Adventist, funso limeneli likanakukhudzani. Komabe, choyamba, kodi “kuweruza mwa kufufuza” nchiyani?

Kodi Iko Nchiyani?

Lemba limene amadalira lochirikiza chiphunzitso chimenechi ndilo Danieli 8:14. Limati: “Nati kwa ine, Mpaka masiku zikwi ziŵiri mphambu mazana atatu usana ndi usiku; pamenepo malo opatulika “adzayeretsedwa.” (King James Version) Chifukwa cha mawu akuti ‘pamenepo malo opatulika adzayeretsedwa,’ anthu ambiri a Adventist amagwirizanitsa vesi limeneli ndi Levitiko chaputala 16. Limafotokoza za mkulu wa ansembe wachiyuda poyeretsa malo opatulika pa Tsiku Lotetezera. Amagwirizanitsanso mawu a Danieli ndi Ahebri chaputala 9, amene amanena kuti Yesu ndiye Mkulu wa Ansembe Wamkulu kumwamba. Katswiri wina wachipembedzo cha SDA anati kalingaliridwe kameneka kazikidwa pa njira yopeza “malemba ochirikiza chiphunzitso.” Munthu amapeza “mawu ena onga malo opatulika pa Dan. 8:14, mawu amodzimodzi pa Lev. 16, mawu amodzimodzinso pa Aheb. 7, 8, 9,” ndiyeno amaganiza “kuti malembawo akunena chinthu chimodzi.”

A Adventist amati: Ansembe a Israyeli wakale tsiku ndi tsiku anali kutumikira m’chipinda cha m’kachisi chotchedwa Malo Opatulika, ndipo machimo anali kukhululukidwa. Pa Tsiku Lotetezera, mkulu wa ansembe chaka ndi chaka anali kutumikira m’Malo Opatulikitsa (chipinda chamkatikati mwa kachisi) ndipo machimo a anthu anali kufafanizidwa. Ndiye amaganiza kuti utumiki waunsembe wa Kristu kumwamba uli ndi mbali ziŵiri. Yoyamba inayamba pamene anakwera kumwamba m’zaka za zana loyamba, nkutha mu 1844, ndipo unachititsa machimo kukhululukidwa. Yachiŵiri, kapena “mbali yoweruza,” inayamba pa October 22, 1844, ndipo idakapitirizabe, ndipo nayonso idzafafaniza machimo. Kodi zimenezo zimachitika motani?

Kuyambira mu 1844, akuti Yesu akufufuza m’mabuku a moyo wa anthu odzitcha okhulupirira (kuyamba ndi akufa, kenako amoyo) kuti aone ngati akuyenerera moyo wosatha. Akuti kupenda kumeneku ndiko “kuweruza mwa kufufuza.” Anthuwo ataweruzidwa choncho, machimo a aja amene apambana mayeso adzafafanizidwa m’mabuku. Ellen White akufotokoza kuti, koma amene akulephera, ‘maina awo amafafanizidwa m’buku la moyo.’ Chotero, “mtsogolo mwa onsewo mudzakhala mutadziŵika kuti ndi moyo kapena imfa.” Pamenepo, ndiye kuti malo opatulika a kumwamba ayeretsedwa ndipo Danieli 8:14 adzakhala atakwaniritsidwa. A Seventh-Day Adventist amaphunzitsa zimenezo. Koma chofalitsa china cha SDA chotchedwa Adventist Review chikuvomereza kuti: “Mawu akuti kuweruza mwa kufufuza sakupezeka m’Baibulo.”

Mawu Akukanika Kugwirizana

Chiphunzitso chimenechi chawavutitsa maganizo a Adventist ena. Womvetsera wina anati, “mbiri ikusonyeza kuti atsogoleri athu okhulupirika amavutika maganizo kwambiri akamasinkhasinkha chiphunzitso chathu cha mwambo ponena za kuweruza mwa kufufuza.” Akuwonjezera kuti, m’zaka zaposachedwapa, kuvutika maganizoko kunasanduka kukayikira, pamene akatswiri a zamaphunziro anayamba “kukayikira mizati yambiri yotichirikiza nthaŵi zonse tikamafotokoza malo opatulika.” Tsopano tiyeni tipende mizati iŵiri yokha.

Mzati woyamba: Amagwirizanitsa Danieli chaputala 8 ndi Levitiko chaputala 16. Mfundo imeneyi imafooketsedwa ndi mavuto aŵiri aakulu​—mawu ndi nkhani yake. Choyamba, talingalirani mawuwo. A Adventist amakhulupirira kuti ‘malo opatulika oyeretsedwa’ pa Danieli chaputala 8 ndiwo enieni ophiphiritsidwa ndi ‘malo opatulika oyeretsedwa’ pa Levitiko chaputala 16. Poyamba, ganizo limeneli linaoneka lomveka, mpaka pamene otembenuza nkhani anadziŵa kuti liwu lakuti “adzayeretsedwa” mu King James Version ndilo kutembenuza molakwa verebu lachihebri lakuti tsa·dhaqʹ (lotanthauza “kukhala olungama”) lomwe lili pa Danieli 8:14. Profesala wa zaumulungu, Anthony A. Hoekema akuti: “Nzachisoni kuti liwulo analitembenuza kuti adzayeretsedwa, pakuti verebu lachihebri limene nthaŵi zonse amalitembenuza kuti adzayeretsedwa, [ta·herʹ] pano silinatchulidwe iyayi.”a Linatchulidwa pa Levitiko chaputala 16 pamene King James Version amatembenuza liwu lakuti ta·herʹ kuti “kuyeretsa” ndi “kukhala woyera.” (Levitiko 16:19, 30) Choncho, Dr. Hoekema molondola anati: “Ngati Danieli anafuna kutanthauza mtundu wakuyeretsa kumene kunali kuchitidwa pa Tsiku Lotetezera, bwenzi atagwiritsira ntchito taheer [ta·herʹ] m’malo mwa tsadaq [tsa·dhaqʹ].” Komabe, liwu lakuti tsa·dhaqʹ silikupezeka mu Levitiko, ndipo liwu lakuti ta·herʹ silikupezekanso mu Danieli. Mawu akukanika kugwirizana.

Kodi Mavesi Enawo Amavumbulanji?

Tsopano talingalirani mawu a m’mavesi enawo. A Adventist amakhulupirira kuti Danieli 8:14 langokhala “vesi lodziimira palokha,” losagwirizana ndi mavesi otsatizana nalo. Koma kodi mumaona kuti zilidi choncho pamene mukuŵerenga Danieli 8:9-14 m’bokosi lakuti “Danieli 8:14 mogwirizana ndi mavesi ena?” Vesi 9 Likunena za woukira, nyanga yaing’ono. Mavesi 10-12 akuvumbula kuti woukira ameneyu adzaukira malo opatulika. Vesi 13 likufunsa kuti, ‘Kodi [kuukira, NW], kumeneku kudzakhala mpaka liti?’ Ndipo vesi 14 likuyankha kuti: “Mpaka masiku zikwi ziŵiri mphambu mazana atatu usana ndi usiku; pamenepo malo opatulika adzayesedwa olungama.” Mwachionekere, vesi 13 likufunsa funso limene likuyankhidwa pa vesi 14. Wazaumulungu Desmond Ford akuti: “Kulekanitsa Danieli 8:14 ndi mfuu imeneyi [“Mpaka liti?” vesi 13] kudzatisiya tilibiretu maziko alionse.”b

Kodi nchifukwa ninji a Adventist amalekanitsa vesi 14 ndi mavesi ena otsatizana nalo? Kuti apeŵe lingaliro lochititsa manyazi. Mavesi enawo akulongosola kuti nyanga yaing’onoyo ndiyo inaipsa malo opatulika otchulidwa pa vesi 14. Komabe, chiphunzitso cha “kuweruza mwa kufufuza” chimati ntchito za Kristu ndizo zinaipsa malo opatulikawo. Akuti kumalo opatulika a kumwamba nkumene iyeyo amasamutsira machimo a anthu okhulupirira. Nanga bwanji ngati a Adventist angakhulupirire zonse ziŵiri chiphunzitsocho ndi mawu a mavesi enawo? Dr. Raymond F. Cottrell, wa Seventh-Day Adventist yemwe alinso mkonzi wa SDA Bible Commentary, analemba kuti: “Kudzinyenga tokha kuti a SDA amamasulira Danieli 8:14 mogwirizana ndi mawu a m’mavesi enawo ndiye kuti tikutanthauza kuti nyangayo ndi Kristu.” Dr. Cottrell akuvomereza moona mtima kuti: “Sitingakhulupirire zonse ziŵiri, mawu a m’mavesi enawo ndi njira imene a Adventist amawamasulirira.” Kuti agwiritsitse pa “kuweruza mwa kufufuza,” ndiye kuti Tchalitchi cha Adventist chiyenera kusankha chinthu chimodzi​—kaya kukhulupirira chiphunzitsocho, kapena kukhulupirira mawu otsatizana ndi Danieli 8:14. Mwachisoni, anakhulupirira chiphunzitsocho ndi kukana mawu a m’mavesi enawo. Dr. Cottrell akuti, nzosadabwitsa kuti ophunzira Baibulo aluso amaimba mlandu a Adventist chifukwa “amapatsa malemba tanthauzo” limene malembawo “sakutanthauza”!

Mu 1967, Dr. Cottrell anatenga m’buku la Danieli phunziro lasukulu yasabata nkulitumiza kumatchalitchi onse a SDA padziko lonse lapansi. Linaphunzitsa kuti Danieli 8:14 akugwirizana ndi mawu a m’mavesi ena ndi kuti akamati ‘kuyeretsa’ sakutanthauza okhulupirira. Ndiponso phunzirolo silinatchule chilichonse ponena za “kuweruza mwa kufufuza.”

Mayankho Odabwitsa

Kodi a Adventist akudziŵa bwino zakuti mzati umenewu siwolimba kwenikweni koti nkuchirikiza nawo chiphunzitso cha “kuweruza mwa kufufuza”? Dr. Cottrell anafunsa a Adventist okwana 27, atsogoleri pa zaumulungu, kuti, ‘Kodi mungandiuze zifukwa zotani zokhudza mawu zimene mumagwirizanitsira Danieli chaputala 8 ndi Levitiko chaputala 16?’ Mmene anayankhira mwadziŵa?

“Anthu 27 onsewo anavomereza kuti analibe zifukwa zokhudza mawu kapena nkhani yake potanthauzira Danieli 8:14 kuti akuphiphiritsira tsiku lotetezera ndi kuweruza mwa kufufuza.” Anawafunsanso kuti, ‘Kodi muli nazo zifukwa zina zogwirizanitsira malembawo?’ Ochuluka mwa akatswiri achipembedzo cha Adventist anati analibenso zifukwa zina, asanu anayankha kuti anagwirizanitsa malembawo chifukwa chakuti Ellen White ndiye anayamba, ndipo aŵiri anati chiphunzitso chawocho chinazikidwa pa “ngozi yamwaŵi” potembenuza Baibulo. Wazaumulungu Ford akuti: “Zimene akatswiri a akatswiri athu akunena zikutanthauza kuti njira yathu yophunzitsira Dan. 8:14 njosamveka.”

Kodi Buku la Ahebri Lingathandize?

Mzati wachiŵiri: Amagwirizanitsanso Danieli 8:14 ndi Ahebri chaputala 9. “M’mabuku athu onse oyamba tinagwiritsira ntchito kwambiri Aheb. 9 pofotokoza Danieli 8:14,” akutero wazaumulungu Ford. Tinayamba kuwagwirizanitsa pambuyo ‘Pogwiritsidwa Mwala’ mu 1844. Pofunafuna chitsogozo, Mmila wotchedwa Hiram Edson anaponya Baibulo lake pathebulo kuti litseguke. Mwadziŵa zimene zinachitika? Linangotseguka lokha pa Ahebri machaputala 8 ndi 9. Ford akuti: “Palibe zina zoposa zimenezo zimene zingampangitse wa Adventist kunena kuti zimenezi nzoyenera kwenikweni ndipo nchizindikiro chosonyeza kuti a Adventist ali olondola ponena kuti machaputala ameneŵa ndiwo akufotokoza bwino phiphiritso ndi tanthauzo la 1844 ndi Dan. 8:14!”

“Mawu amenewo akutanthauza zambiri kwa a Seventh-Day Adventist,” anawonjezera choncho Dr. Ford m’buku lake lakuti Daniel 8:14, The Day of Atonement, and the Investigative Judgment. “Pa Aheb. 9 . . . ndi pokha pamene tingapeze mafotokozedwe omveka bwino a tanthauzo la . . . chiphunzitso cha malo opatulika chimene chili chofunika kwambiri kwa ife.” Inde, Ahebri chaputala 9 ndicho chaputala cha “m’Chipangano Chatsopano” chofotokoza tanthauzo la ulosi pa Levitiko chaputala 16. Komanso a Adventist amati Danieli 8:14 ndilo vesi la “m’Chipangano Chakale” limene limafotokoza zimenezo. Ngati mawu onsewo ali oona, ndiye kuti Ahebri chaputala 9 ndi Danieli chaputala 8 ayenera kugwirizananso.

Desmond Ford akuti: “Zinthu zina zimangodziŵika msanga poŵerenga Aheb. 9. Sakutchulapo buku la Danieli, ndipo ngakhale mpang’ono pomwe sakutchulapo Dan. 8:14. . . . Chaputala chonsecho chikulongosola Levitiko 16.” Iye akuti: “Chiphunzitso chathu cha malo opatulika sichimapezeka m’buku lokhali m’Chipangano Chatsopano limene likulongosola tanthauzo la mautumiki a pamalo opatulika. Alembi otchuka a Adventist padziko lonse akuzidziŵa bwino zimenezo.” Chotero, mzati wachiŵiriwo nawonso siwolimba kwenikweni kuti uchirikize chiphunzitso chosamvekacho.

Komabe, lingaliro limenelo si lachilendo. Dr. Cottrell akuti, kwa zaka zambiri, “akatswiri a Baibulo m’tchalitchi alidziŵa bwino vuto limene timakumana nalo pomafotokoza tanthauzo la Danieli 8:14 ndi Ahebri 9.” Zaka 80 zapitazo, wa Seventh-Day Adventist wina womveka, E. J. Waggoner analemba kuti: “Chiphunzitso cha Adventist chonena za malo opatulika, ndi ‘Kuweruza mwa Kufufuza’ . . . , kwenikweni kwangokhala kukana chitetezo cha machimo.” (Confession of Faith) Zoposa zaka 30 zapitazo, mavuto amenewo anaakambitsirana pa Msonkhano Waukulu, wa atsogoleri a Tchalitchi cha SDA.

Mavuto ndi Kukanika Kuwathetsa

Pa Msonkhano Waukuluwo anasankha “Komiti Yoona za Mavuto a Buku la Danieli.” Inayenera kulemba lipoti lonena za mmene angathetsere mavuto okhudza Danieli 8:14. Komiti ya anthu 14 imeneyo inalifufuza vutolo zaka zisanu koma inalephera kupeza yankho limodzi limene onse anagwirizana nalo. Mu 1980, mmodzi wa komitiyo Cottrell anati ambiri m’komitiyo anaganiza kuti njira imene a Adventist “angatanthauzire nayo mokhutiritsa” Danieli 8:14 ndiyo mwa kuloŵetsamo malingaliro ena angapo ongoganizira ndi kuti za mavutozo “angoziiŵala.” Anawonjezera kuti: “Kumbukirani kuti dzina la komitiyo linali Komiti Yoona za Mavuto a Buku la Danieli, komano ambiri anali kunena kuti tingoiŵala za mavutowo ndipo tisanene chilichonse za iwo.” Zimenezo zikanangokhala ngati “tavomereza kuti talephera kuyankha.” Chotero oŵerengeka anakana kugwirizana ndi maganizo a aunyinji, ndipo sanalembe lipoti lililonse. Mavuto a chiphunzitso anakhalabe choncho osathetsedwa.

Ponena za kulephera kumeneku, Dr. Cottrell akuti: “Nkhani ya Danieli 8:14 ilipobe chifukwa nthaŵi yonseyi sitinafune kulimba mtima ndi kuvomereza kuti ikutivuta kulongosola. Nkhani imeneyi sidzatha iyayi malinga ngati tizinamizirabe kuti palibe vuto, malinga ngati tizikhulupirirabe zinthu zimene sitidziŵa, kaya aliyense payekha kapena tonse pamodzi.”​—Spectrum, magazini yofalitsidwa ndi Association of Adventist Forums.

Dr. Cottrell akulangiza a Adventist kuti “apende mosamalitsa maganizo awo ndi njira zofotokozera nkhani zimene timatanthauzira Chiadventizimu​—Lemba losayenera kunyalanyazidwa.” Tikulimbikitsa a Adventist kupenda chiphunzitso cha “kuweruza mwa kufufuza” kuti aone ngati mizati yake yazikidwadi m’Baibulo kapena yangozikidwa pamchenga wa mwambo.c Mtumwi Paulo analangiza mwanzeru kuti: “Yesani zonse; sungani chokomacho.”​—1 Atesalonika 5:21.

[Mawu a M’munsi]

a Wilson’s Old Testament Word Studies limatanthauzira tsadaq (kapena, tsa·dhaqʹ) kuti “kukhala wolungama, kulungamitsidwa,” ndipo taheer (kapena, ta·herʹ) kuti “kukhala woyera, kuwala, ndi kunyezimira; kuyeretsedwa, kukhala wosaipsidwa kapena kudetsedwa.”

b Dr. Ford anali profesala wa chipembedzo pakoleji yoyendetsedwa ndi tchalitchi ya Pacific Union College ku U.S.A. Mu 1980 atsogoleri a SDA anampatsa tchuti cha miyezi isanu ndi umodzi kuti akaphunzire za chiphunzitsocho, koma iwo anakana zimene anapezazo. Iye anazifalitsa m’buku lakuti Daniel 8:14, the Day of Atonement, and the Investigative Judgment.

c Kuti mumve mafotokozedwe omveka a Danieli chaputala 8, onani masamba 188-219 m’buku lachingelezi lakuti “Your Will Be Done on Earth,” lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

[Bokosi patsamba 27]

Danieli 8:14 Mogwirizana ndi Mavesi Ena

DANIELI 8:9 ‘Ndipo mu imodzi ya izi munaphuka nyanga yaing’ono, imene inakula kwakukulu ndithu, kuloza kumwela, ndi kummaŵa, ndi ku dziko lokometsetsa. 10 Nikula, kufikira khamu la kuthambo; ndi zina za khamulo ndi za nyenyezi inazigwetsa pansi, nizipondereza. 11 Inde inadzikulitsa kufikira kwa kalonga wa khamulo, nimchotsera nsembe yopsereza yachikhalire; ndi pokhala malo ake opatulika panagwetsedwa. 12 Ndipo khamulo linaperekedwa kwa iyo, pamodzi ndi nsembe yopsereza yachikhalire mwa kulakwa kwake, nigwetsa pansi choonadi, nichita chifuniro chake, nikuzika.

‘13 Pamenepo ndinamva wina woyera alikunena; ndi wina woyera anati kwa iye uja wanenayo, Masomphenya a nsembe yopsereza yachikhalire, ndi cholakwa chakupululutsa cha kupereka malo opatulika ndi khamulo ziponderezedwe, adzakhala mpaka liti? 14 Nati kwa ine, Mpaka masiku zikwi ziŵiri mphambu mazana atatu usana ndi usiku; pamenepo malo opatulika adzayesedwa olungama.’​—Revised Nyanja (Union) Version.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena