Kodi Pali Mabuku Ena a Uthenga Wabwino Amene Amafotokoza Nkhani za Yesu Zimene M’Baibulo Mulibe?
“BUKU limeneli ndi lofunika kwambiri ndipo anthu ambiri adabwa akaliwerenga.” “Zimene bukuli likunena zikusiyana ndi zimene anthu akhala akukhulupirira pa nkhani ya mpingo wakale wachikhristu.” Mawu amenewa ananena ndi akatswiri ena amaphunziro posangalala ndi kupezeka kwa buku limene ena amati ndi Uthenga Wabwino wa Yudasi (lili pamwambali). Anthu amaganiza kuti bukuli linasowa kwa zaka zoposa 1,600.
Masiku ano anthu ambiri akuchita chidwi ndi mabuku ngati amenewa omwe ena amati ali m’gulu la Mauthenga Abwino. Anthu ena amati mabukuwa amafotokoza zinthu zikuluzikulu zimene Yesu anachita ndiponso kuphunzitsa. Iwo amati zinthu zimenezi zakhala zisakudziwika kwa nthawi yaitali. Koma kodi ena mwa mabuku amenewa ndi ati? Kodi n’zoona kuti mabukuwa angatithandize kudziwa zoona zenizeni zokhudza Yesu komanso Chikhristu zimene sitingazipeze m’Baibulo?
Kusiyana kwa Mabuku Amenewa ndi Mauthenga Abwino Ovomerezeka
Pakati pa zaka za 41 ndi 98 C.E., Mateyu, Maliko, Luka ndi Yohane analemba mabuku ofotokoza za “mzere wa makolo a Yesu Khristu,” kapena kuti mbiri ya Yesu. (Mateyu 1:1) Nkhani zimenezi zimatchedwanso kuti “uthenga wabwino” wonena za Yesu Khristu.—Maliko 1:1.
Ngakhale kuti panali mbiri ina yokhudza Yesu imene anthu ena analemba kapena imene inkangofotokozedwa mwapakamwa, mabuku anayi a Uthenga Wabwino okhawa ndi amene ankaonedwa kuti ndi ouziridwa ndi Mulungu komanso oyenera kukhala mbali ya Baibulo. Mabukuwa amatithandiza kudziwa mbiri ‘yodalirika’ yokhudza moyo wa Yesu ali padziko lapansi pano komanso zimene anaphunzitsa. (Luka 1:1-4; Machitidwe 1:1, 2; 2 Timoteyo 3:16, 17) Mauthenga Abwino anayi amenewa amapezeka mu mndandanda uliwonse wamakedzana wa Malemba Achigiriki. Choncho palibe zifukwa zokayikirira kuti mabuku amenewa ndi olondola ndiponso ndi mbali ya Mawu ouziridwa a Mulungu.
Koma patapita nthawi, panayamba kupezeka mabuku ena amene anthu ankanena kuti alinso m’gulu la Mauthenga Abwino.a
Chakumapeto kwa zaka za m’ma 100, Irenaeus wa ku Lyon analemba kuti anthu ampatuko omwe anachoka m’Chikhristu anali ndi “mabuku achinyengo ambiri owonjezera pa mabuku a m’Baibulo” ndipo mabukuwa anaphatikizapo amene amati ali m’gulu la Mauthenga Abwino omwe “anthu ampatukowa analemba okha n’cholinga chofuna kusokoneza maganizo a anthu opusa.” N’chifukwa chake mabuku amenewa ankaonedwa kuti sanali abwino kuwawerenga komanso kukhala nawo.
Komabe ansembe ndi anthu ena okopera mabuku amene anakhalako zaka za m’ma 500 mpaka m’ma 1500 anapitiriza kukopera ndi kusunga mabuku amenewa. M’zaka za m’ma 1800, anthu ambiri anayamba kuchita chidwi ndi mabukuwa ndipo anthu anatulukira mabuku ambiri owonjezera pa mabuku amene ali m’Baibulo, kuphatikizapo mabuku amene ena amati ndi Mauthenga Abwino. Panopa pali mabuku ambiri oterewa amene anamasuliridwa mu zinenero zikuluzikulu za masiku ano.
Nkhani Zokhudza Yesu Zimene Mabukuwa Amafotokoza N’zokayikitsa Kwambiri
Nthawi zambiri, mabuku amene amati ali m’gulu la Mauthenga Abwinowa amafotokoza kwambiri za anthu amene satchulidwa kawirikawiri kapenanso amene satchulidwa n’komwe m’Mauthenga Abwino ovomerezeka. Nthawi zina amanena za nkhani zokhudza Yesu ali mwana zimene palibe umboni woti zinachitikadi. Tiyeni tione zina mwa nkhani zoterezi:
◼ Buku limene amati ndi Uthenga Wabwino wa Yakobo, lomwe limatchedwanso kuti “Kubadwa kwa Mariya,” limafotokoza za kubadwa kwa Mariya, ubwana wake komanso ukwati wake ndi Yosefe. Chifukwa cha nkhani zimene zili m’bukuli m’pake kuti anthu amalitchula kuti ndi buku la nthano zauzimu. Bukuli limalimbikitsa maganizo akuti Mariya anakhalabe namwali ndipo limachita kuonekeratu kuti cholinga chake ndi kufuna kuti anthu azilambira Mariya.—Mateyu 1:24, 25; 13:55, 56.
◼ Buku limene amati ndi Uthenga Wabwino wa Tomasi limafotokoza kwambiri zimene Yesu ankachita ali ndi zaka zapakati pa 5 ndi 12. Limanena kuti iye ali mwana ankachita zozizwitsa. (Onani Yohane 2:11.) Nkhani zimenezi zimasonyeza kuti Yesu anali mwana wosamvera, wosachedwa kukwiya komanso wovuta, yemwe ankagwiritsa ntchito mphamvu zake zotha kuchita zozizwitsa pobwezera zimene aphunzitsi, anthu oyandikana nawo nyumba komanso ana ena ankamuchitira. Nkhanizi zimati Yesu ankagwiritsa ntchito mphamvu zakezo kuchititsa khungu anthu, kuwalumalitsa kapenanso kuwapha kumene.
◼ Mabuku ena amene amati ali m’gulu la Mauthenga Abwino ali ndi nkhani zokhudza mlandu wa Yesu, imfa yake komanso kuukitsidwa kwake. Lina mwa mabuku oterewa ndi limene amati ndi Uthenga Wabwino wa Petulo. Mabuku enanso ngati limene amati Machitidwe a Pilato, lomwe ndi mbali ya buku lomwe amati ndi Uthenga Wabwino wa Nikodemo, amanena za anthu amene ankakhudzidwa ndi nkhani za mlandu wa Yesu, imfa yake komanso kuukitsidwa kwake. Nkhani zimenezi ndi zosadalirika chifukwa zimanena za zinthu zoti sizinachitikedi komanso zimatchula anthu oti sanakhaleko. Buku limene amati ndi Uthenga Wabwino wa Petulo limafotokoza nkhani mosonyeza ngati Pontiyo Pilato sanalakwe ndipo limafotokoza nkhani ya kuuka kwa Yesu m’njira yoti izioneka ngati sinachitikedi.
Mabuku Amene Ena Amati Ali M’gulu la Mauthenga Abwino Analembedwa ndi Anthu Opandukira Chikhristu
Mu December 1945 alimi a pafupi ndi mudzi wotchedwa Nag Hammadi, womwe uli kumpoto kwa dziko la Egypt, anapeza magumbwa okwana 13 amene anali ndi nkhani 52. Anthu amaganiza kuti zinthu zimenezi, zomwe ndi za m’zaka za m’ma 300, zinalembedwa ndi kagulu kena kampatuko ka anthu achipembedzo komanso akatswiri a nzeru za anthu. Polemba zinthu zimenezi iwo anaphatikiza mfundo zongoganiza okha, ziphunzitso zachikunja, nzeru za Agiriki, mfundo zachipembedzo chachiyuda komanso mfundo zachikhristu. Chifukwa cha zimenezi, anthu amenewa ankasokoneza anthu ena amene ankati ndi Akhristu.—1 Timoteyo 6:20, 21.
Mabuku amene amati ndi Uthenga Wabwino wa Tomasi, Uthenga Wabwino wa Filipo komanso Uthenga Wabwino Wachoonadi, amene ali m’gulu la zinthu zimene zinapezeka ku Nag Hammadi, amafotokoza mfundo za gulu la anthu ampatuko aja ngati kuti zinalankhulidwa ndi Yesu. Buku lina limene linalembedwa ndi anthu ampatukowa ndi buku lomwe langotulukiridwa kumene limene amati ndi Uthenga Wabwino wa Yudasi. Bukuli limakometsera moyo wa Yudasi ndipo limasonyeza ngati kuti iye yekha ndi amene ankamudziwa bwino Yesu. Mabukuwa amafotokoza kuti Yesu “anali mphunzitsi komanso munthu amene ankaululira anthu nzeru ndi chidziwitso, koma osati mpulumutsi amene anafa chifukwa cha machimo a anthu.” Koma Mauthenga Abwino ouziridwa amene ali m’Baibulo amanena kuti Yesu anafa monga nsembe ya machimo a anthu. (Mateyu 20:28; 26:28; 1 Yohane 2:1, 2) Apa n’zoonekeratu kuti cholinga cha mabuku a uthenga wabwino a anthu ampatuko n’kulepheretsa anthu kukhulupirira Baibulo.—Machitidwe 20:30.
Kudalirika kwa Mabuku a Uthenga Wabwino Amene Ali M’Baibulo
Tikaona bwinobwino mabuku amene anthu ena amati ali m’gulu la mauthenga abwino, timaona kuti mabukuwa ndi abodza. Mukawayerekezera ndi zimene zili m’Mauthenga Abwino ovomerezeka, mabukuwa amachita kuonekeratu kuti sanauziridwe ndi Mulungu. (2 Timoteyo 1:13) Popeza mabukuwa analembedwa ndi anthu amene sankamudziwa Yesu komanso atumwi ake, sangafotokoze choonadi chonena za Yesu komanso Chikhristu. M’malomwake, nkhani zimene zili m’mabukuwa n’zopeka ndipo sizingathandize munthu kudziwa Yesu komanso ziphunzitso zake.—1 Timoteyo 4:1, 2.
Koma mosiyana ndi anthu amene analemba mabuku amenewa, Mateyu ndi Yohane anali m’gulu la atumwi 12 a Yesu. Maliko anali mnzake wa mtumwi Petulo pomwe Luka anali mnzake wapamtima wa mtumwi Paulo. Iwo analemba mabuku awo a Uthenga Wabwino mouziridwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. (2 Timoteyo 3:14-17) Choncho, Mauthenga Abwino anayi ovomerezeka ali ndi zonse zimene zingamuthandize munthu kukhulupirira kuti Yesu ndi Khristu, Mwana wa Mulungu.—Yohane 20:31.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu amene amagwiritsa ntchito ponena za mabuku owonjezera a m’Baibulo (apocryphal) anachokera ku mawu achigiriki amene amatanthauza “kubisa.” Poyamba mawu amenewa ankanena za nkhani zimene zinkaphunzitsidwa pasukulu ina koma ankazibisa kuti amene saphunzira pasukulupo asazidziwe. Koma m’kupita kwa nthawi, mawuwa anayambanso kugwiritsidwa ntchito ponena za mabuku omwe sanaphatikizidwe m’gulu la mabuku ovomerezeka a m’Baibulo.
[Mawu a Chithunzi patsamba 18]
Kenneth Garrett/National Geographic Image Collection