Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/95 tsamba 1
  • Khalidwe Lachikristu ku Sukulu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Khalidwe Lachikristu ku Sukulu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
  • Nkhani Yofanana
  • Achichepere Achikristu Khalani Olimba M’chikhulupiriro
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Kodi Chikhulupiriro Chanu Chidzakhala Cholimba?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Kodi Mumakhulupiriradi Uthenga Wabwino?
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kodi Yehova Amatithandiza Bwanji Kupirira?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1995
km 8/95 tsamba 1

Khalidwe Lachikristu ku Sukulu

1 Ngati muli Mkristu wachinyamata amene akali pasukulu, mufunikira chikhulupiriro cholimba kuti musunge umphumphu wanu. Mumakhala pakati pa mayanjano oipa ndi pa mikhalidwe imene ingayese chikhulupiriro chanu. Kuli kofunika kuti mugwiritsire ntchito uphungu wa Petro wakuchititsa ‘mayendedwe anu mwa amitundu kukhalabe okoma, kuti, . . . akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino.’ (1 Pet. 2:12) Mufunikira kulimba mtima ndi kutsimikiza kuti mulimbane ndi zovuta zimenezi.

2 Kusukulu ndi kumalo ena, mumakumana ndi mabwenzi okusonkhezerani kugonana popanda ukwati, kutukwana, kusuta fodya, ndi anamgoneka. Tsiku lililonse, mumalimbana ndi ziyeso zimene zimafuna kuwononga mbiri yanu ya khalidwe labwino. Mofanana ndi achikulire, inu muyenera “kumenya nkhondo ya chikhulupiriro zolimba” ngati muti muchirimike pa mayesero otero.—Yuda 3, NW; onani Nsanja ya Olonda ya July 15, 1991, masamba 23-6.

3 Kusukulu kuli zikondwerero zautundu ndi maholide adziko. Kodi mumadziŵa kuti ndi maholide ati autundu ndi achipembedzo amene amachirikizidwa kusukulu kwanu? Ngati mkhalidwe wovuta ubuka, kodi ‘mudzakhala nacho chikumbumtima chabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino . . . akachitidwe manyazi’?—1 Pet. 3:16.

4 Mungakopedwe ndi chikoka cha zamaseŵero a pasukulu kapena macheza. Muyenera kukhala maso pa kudziŵa mmene zochitachita zooneka ngati zosangalatsa zimenezi zingafooketsere chikhulupiriro chanu. Mufunikira kusankha mabwenzi amene mungathe ‘kusinthana nawo chilimbikitso,’ aliyense akumamangiriridwa ndi chikhulupiriro cha wina.—Aroma 1:12, NW.

5 Mukhoza Kuchirimika, ndi Thandizo la Yehova: Nthaŵi zonse Satana akuyesa chikhulupiriro chanu. Mayesero amene mufunikira kuchirimika angakhale aakulu, koma mfupo zake nzoyenererana ndi mayeserowo. (1 Pet. 1:6, 7) Simungathe kuchirimika mwa inu nokha; muyenera kuyang’ana kwa Yehova kaamba ka thandizo. Yesu analimbikitsa ophunzira ake kuti: “Chezerani ndi kupemphera, kuti mungaloŵe m’kuyesedwa.” (Mat. 26:41) Kudzilanga ndi kudziletsa nzofunika kwambiri.—1 Akor. 9:27.

6 Nthaŵi zonse kumbukirani kuti muli ndi mlandu kwa Yehova wa khalidwe lanu. (Mlal. 11:9) Ngakhale kuti zimene mukuchita zingakhale zisakuonedwa ndi ena, Yehova akudziŵa zimene mukuchita ndipo adzapereka chiweruzo. (Aheb. 4:13) Chikhumbo choona cha kumkondweretsa chiyenera kukusonkhezerani ‘kugwira ntchito yanu ya chipulumutso chanu ndi mantha, ndi kunthunthumira.’ (Afil. 2:12) Kuŵerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku nkothandiza kwambiri. Iwo ngwodzala ndi uphungu wabwino koposa ndi zitsanzo zabwino kwambiri zozitsanzira.—Aheb. 12:1-3.

7 Makolo, mumachita mbali yofunika. Mufunikira kuyang’anira ana anu, khalani maso pa zovuta zimene amakumana nazo, ndipo perekani thandizo pamene lili lofunika. Kodi muli ndi unansi wabwino ndi ana anu? Kodi mwawaphunzitsa kuzindikira ndi kuyamikira malamulo a Mulungu ndi njira zake? Pamene ayang’anizana ndi zitsenderezo kapena mayeso, kodi ana anu ngolimba, kapena kodi amangogonja mosavuta? Kodi amalefulidwa chifukwa chakuti ayenera kukhala osiyana ndi ausinkhu wawo? Monga makolo, muli ndi thayo la kuwathandiza. (Deut. 6:6, 7) Ngati muchita bwino thayo lanu, mudzawathandiza kukhala olakika mu nkhondo ya chikhulupiriro.—Miy. 22:6.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena