Misonkhano Yautumiki ya April
Mlungu Woyambira April 7
Mph. 12: Zilengezo zapamalopo. Ŵerengani Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu kusiyapo zija zimene zaperekedwa kwa anthu akutiakuti monga woyang’anira wotsogoza. Tchulani mfundo zokambitsirana za m’magazini atsopano.
Mph. 15: “Ambirimbiri Akuwonjezedwa.” Mafunso ndi mayankho. Pendani mfundo zazikulu za mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 1993, masamba 12-17.
Mph. 18: “Thandizani Osoŵa Chidziŵitso Kuti Azindikire.” Mafunso ndi mayankho. Pendani mbali za brosha la Mulungu Amafunanji: njira yopepuka yophunzirira, mafunso apanthaŵi yake, zithunzi zokopa, malifalensi ambirimbiri a Malemba. Gogomezerani chonulirapo cha kuyambitsa maphunziro amene m’kupita kwa nthaŵi adzaloŵa m’buku la Chidziŵitso. Wofalitsa wokhoza achite chitsanzo cha mmene tingayambitsire phunziro mwa kugwiritsira ntchito mafikidwe osonyezedwa m’ndime 4. Limbikitsani makolo onse mumpingo kuphunzira broshalo ndi ana awo aang’ono.
Nyimbo Na. 130 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira April 14
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti. Ngati nthaŵi ilola, simbani mwachidule zokumana nazo za m’munda zakumaloko pogaŵira brosha la Mulungu Amafunanji kapena kuyambitsa maphunziro a Baibulo mwa kugwiritsira ntchito broshali.
Mph. 15: “Kutsogoza Ophunzira ku Gulu la Dzina Lathu.” (Ndime 1-6) Mafunso ndi mayankho. Ŵerengani ndime 5-6 ndi malemba osagwidwa mawu. Simbani zokumana nazo zakumaloko za zimene ophunzira Baibulo achita atapenyerera vidiyo yakuti Jehovah’s Witnesses—The Organization Behind the Name.
Mph. 20: “Phunzitsani Ena Zimene Mulungu Amafuna.” Kukambitsirana ndime 1-4 ndi omvetsera. Chitirani zitsanzo maulaliki a m’ndime 5 mwa kugwiritsira ntchito mikhalidwe inayi yosiyanasiyana—m’khwalala, panyumba, pamalo a malonda, ndi m’paki. Onse akumbutseni kuombola mabrosha ndi magazini a mu utumiki wakumunda asanachoke pa Nyumba ya Ufumu.
Nyimbo Na. 126 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira April 21
Mph. 15: Zilengezo zapamalopo. Fotokozani kuti nthaŵi yopereka mafomu ofunsira upainiya wothandiza m’May idakalipo. Pendani Bokosi la Mafunso, ndipo dziŵitsani mpingo ngati pali mabuku amene akufunika kuti laibulale ya m’Nyumba ya Ufumu ikhale yachikwanekwane.
Mph. 15: “Kutsogoza Ophunzira ku Gulu la Dzina Lathu.” (Ndime 7-14) Mafunso ndi mayankho. Mphunzitsi wokhoza bwino achite chitsanzo cha mmene tingakambitsirane mwachifundo ndi mosabisa kalikonse ndi wophunzira wathu ponena za kufunika kwa kupezeka pamisonkhano.
Mph. 15: Kugwiritsira Ntchito Mabuku Athu Mokwana. Nkhani ya mkulu. (Onani Utumiki Wathu Waufumu wa September 1995 masamba 3-5.) Malipoti akusonyeza kuti kaŵirikaŵiri mipingo imaoda magazini ambiri kuposa amene amagaŵira mwezi uliwonse. Magazini ngati 50 peresenti samachitidwa lipoti kuti anagaŵidwa. (Tchulani zimene ziŵerengero za kwanuko zikusonyeza.) Kodi nchiyani chimachitika ndi magaziniwa? Ambiri amangokhala pa shelufu kapena amatayidwa. Kodi tingazipeŵe motani zimenezi? Wofalitsa aliyense ayenera kuona kuti akufuna angati ndi kuoda kokha amene angagaŵire. Chipangeni chizoloŵezi kugaŵira magazini kwa onse amene tilankhula nawo. Musalekerere makope akale kuwonongeka. Khalani ndi phande mu utumiki wa magazini patsiku Loŵeruka loyamba ndi lachitatu.
Nyimbo Na. 128 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira April 28
Mph. 15: Zilengezo zapamalopo. Kumbutsani onse kupereka malipoti awo a utumiki wakumunda a April. Lengezani maina a amene adzachita upainiya wothandiza m’May. Longosolani makonzedwe owonjezera apamalopo a kukumana kwa utumiki amene akupangidwa. M’May tiyenera kuyesetsa ndithu kubwerera kumene tinagaŵira mabrosha ndi chonulirapo cha kuyambitsa maphunziro. Mwachidule tchulani njira zimene tingapemphere mochenjera dzina ndi keyala ya anthu amene tawalalikira mwamwaŵi. Mungayambe mwatchula dzina lanu ndi keyala yanu kenako nkudzafunsa ngati pali nambala ya foni imene mungatumizireko kuti mulankhule nawo. Pemphani omvetsera kutchula njira zina zimene zagwira bwino ntchito kwa iwo.
Mph. 15: “Kodi Amachitiranji Zimenezi?” Mkulu akambitsirana nkhaniyi ndi apainiya okhazikika aŵiri kapena atatu. (Ngati palibe, gwiritsirani ntchito amene amalembetsa upainiya wothandiza kaŵirikaŵiri.) Phatikizanipo mfundo zazikulu za m’nkhani yakuti “Apainiya Amapereka ndi Kulandira Madalitso,” ya mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 1994. Yense wa iwo afotokoze chifukwa chimene analoŵera utumiki waupainiya. Apempheni kusimba zokumana nazo zosonyeza madalitso amene apeza chifukwa chochita utumikiwu.
Mph. 15: Zosoŵa zapamalopo. Akulu angagwiritsire ntchito nthaŵiyi kupereka chidziŵitso pa zosoŵa zakutizakuti zapamalopo.
Nyimbo Na. 129 ndi pemphero lomaliza.