Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/97 tsamba 2
  • Kodi Amachitiranji Zimenezi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Amachitiranji Zimenezi?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Madalitso a Utumiki Waupainiya
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Apainiya Amapereka ndi Kulandira Madalitso
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Ino Ndiyo Nthawi Yofunika Kulalikira!
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • “Upainiya Ungakuyenereni Kwabasi!”
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 4/97 tsamba 2

Kodi Amachitiranji Zimenezi?

1 Kunanenedweratu za Kristu kuti ‘changu cha panyumba ya Mulungu chidzamudya.’ (Sal. 69:9) Changu cha Yesu pakulambira koona kwa Yehova chinamkakamiza kuika utumiki patsogolo. (Luka 4:43; Yoh. 18:37) Changu chimenechi cha kuchitira umboni choonadi chimaonekanso mu utumiki wa Mboni za Yehova. Chaka chautumiki chathachi, avareji ya anthu 645,509 padziko lonse anachitako mtundu wina wa upainiya mwezi uliwonse. Malinga ndi kudzipatulira kwa Mulungu, aliyense wa ife mwapemphero ayenera kuona ngati angalinganize mikhalidwe yake kuti atumikire monga mpainiya wothandiza kapena wokhazikika.—Sal. 110:3; Mlal. 12:1; Aroma 12:1.

2 Popeza tikukhala m’dongosolo la zinthu lokondetsa chuma mwadyera, ambiri m’dziko samavetsetsa chifukwa chimene wina angazigwirira ntchito mwachangu chonchi mu utumiki pazinthu zimene sizimbweretsera ndalama zilizonse kapena ulemerero. Kodi apainiya amachitiranji zimenezi? Iwo akudziŵa kuti ali pantchito yopulumutsa miyoyo. Posonkhezeredwa ndi chikondi chachikulu cha Yehova ndi munthu mnzawo, iwo amamva kuti ali ndi thayo lofunika kwambiri la kuthandiza kupulumutsa miyoyo. (Aroma 1:14-16; 1 Tim. 2:4; 4:16) Apainiya ena mwamuna ndi mkazi wake anayankha mwachidule nati: “Tikuchitiranji upainiya? Kodi tingapereke chifukwa chilichonse kwa Yehova ngati sitikuuchita?”

3 Mlongo winanso analemba izi ponena za chosankha chake cha kuyamba upainiya: “Ineyo ndi mwamuna wanga tinalinganiza kukhala ndi magwero amodzi a ndalama, zimene zinatanthauza kusiya zonse zosafunikira. Komabe, Yehova anatidalitsa kwambiri, osatilekerera kuti tikhale aumphaŵi ndi osoŵa. . . . Ndapeza chifukwa chenicheni chokhalira moyo—kuthandizira osoŵa kudziŵa kuti Yehova, Mulungu woona, saali patali ndi omfunafuna.” Poona kufulumira kwa nthaŵi, apainiya amakhutira nazo zofunika za moyo pamene akuyesetsa kufunafuna chuma chauzimu chimene sichidzatha konse.—1 Tim. 6:8, 18, 19.

4 Ngati mikhalidwe yanu ilola, bwanji osagwirizana ndi abale anu ndi alongo anu zikwi mazana ambiri padziko lonse amene akuchita upainiya? Mwa njira imeneyi mungathe kusangalala monga akuchitira iwo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena