Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/97 tsamba 1
  • Achikulire Saleka Kulalikira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Achikulire Saleka Kulalikira
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Amasamalira Mwachikondi Atumiki Ake Okalamba
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Muziona Kuti Achikulire Okhulupirika Ndi Amtengo Wapatali
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2021
  • Ulemerero wa Imvi
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Tumikirani Yehova Masiku Oipa Asanafike
    Nsanja ya Olonda—2014
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 8/97 tsamba 1

Achikulire Saleka Kulalikira

1 Pamene anthu akukalamba, ambiri amangoganiza zopuma pantchito yawo yakudziko ndi kusangalala ndi moyo wosavuta pa zaka zawo zotsalazo. Angaganize kuti agwira ntchito kwambiri ndithu ndipo tsopano ayeneradi kupuma. Kapena angangofuna kumasangalala masiku onse otsala a moyo wawowo.—Luka 12:19.

2 Monga atumiki odzipatulira kwa Yehova, timaona moyo mosiyana. Tikudziŵa kuti sitimapuma pa utumiki wa Mulungu. Ndife otsimikiza mtima chifukwa ‘tikulindira . . . moyo wosatha.’ (Yuda 21) Chidziŵitso ndi luso limene munthu wapeza pazaka zambiri zingawongolere kuzindikira kwake ndi luntha. Zimenezi zingapangitse munthu kukhala wanzeru ndi wokhazikika maganizo ndi woyamikira moyo kwambiri. Mikhalidwe yonseyi imamthandiza kwambiri mtumiki wa uthenga wabwino.

3 Kukula sikumatanthauza chabe kukalamba kwa thupi; kumaphatikizaponso maganizo a munthu. Ngati mukuyesayesa kukhala ndi moyo wautali ndipo mukuyesetsa kuti maganizo anu asakalambe, mungakwanitse kuchita zomwezo. Achikulire angalemeretse moyo wawo mwa kuwonjezera chidziŵitso chawo chauzimu ndi kuwauza ena za chidziŵitsocho.—1 Akor. 9:23.

4 Anthu Amene Alidi Zitsanzo: Pausinkhu wa zaka 86, mlongo wina anati: “Ndikamaganiza zaka 60 zapitazo kuyambira pamene ndinaphunzira choonadi, lonjezo lolimbikitsa la Mulungu limasangalatsa mtima wanga kwambiri. Inde, Yehova yemwe amachita mokhulupirika kwa anthu okhulupirika akutithandiza kututa chisangalalo chachikulu.” (Sal. 18:25, NW) Mbale wina wachikulire akukumbukira mmene imfa ya mkazi wake inampwetekera mtima kwambiri, ndipo pambuyo pa zimenezo thanzi lake linaipa kwambiri. Iye anati: “Komabe, mwa chisomo cha Yehova, ndinalimba bwino moti ndinatha kuloŵa utumiki waupainiya patapita zaka ziŵiri. Ndikuyamikira Yehova chotani nanga poona kuti thanzi langa lawongokera kwambiri chifukwa chofutukula ntchito imeneyi yolalikira!”

5 Nzoyamikirika chotani nanga kuti achikulire ambiri akutsimikiza kumalalikirabe malinga ndi mmene thanzi ndi nyonga yawo ilili—osaleka iyayi! Ali ndi chifukwa chabwino chonenera kuti: “Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ubwana wanga; ndipo kufikira lero ndilalikira zodabwiza zanu.”—Sal. 71:17.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena