Misonkhano Yautumiki ya August
Mlungu Woyambira August 4
Mph. 7 : Zilengezo zapamalopo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu. Kambanipo za lipoti la March la utumiki wakumunda la m’dzikomo ndi la mpingo wanu.
Mph. 13: “Misonkhano Imafulumiza ku Ntchito Zabwino.” Mafunso ndi mayankho. Sonyezani mapindu a kukambitsirana kolimbikitsa misonkhano isanayambe kapena pambuyo pa misonkhano.—Onani Bukhu Lolangiza la Sukulu, tsamba 83, ndime 17-18.
Mph. 25: “Kodi Tiyenera Kusamala za Ukhondo?” Mafunso ndi mayankho. Yokambidwa ndi mkulu.
Nyimbo Na. 78 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 11
Mph. 5 : Zilengezo zapamalopo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: “Achikulire Saleka Kulalikira.” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo chokumana nacho cha agogo achikulire amene anachitapo upainiya wothandiza, cha mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1988, tsamba 13.
Mph. 25: “Dalirani Yehova Kuti Akulitse Zinthu.” Nkhani ndi zitsanzo. Gogomezerani kuti nkofunika kupanga maulendo obwereza kwa amene tinasiyako mabrosha. Chitani zitsanzo ziŵiri zokonzedwa bwino zosonyeza mmene tingayambire maphunziro. Phatikizanipo malingaliro a m’mphatika ya Utumiki Wathu Waufumu wa May 1997, ndime 7-11.
Nyimbo Na. 71 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 18
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Pendani “Programu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera.”
Mph. 10: Zosoŵa zapamalopo.
Mph. 25: Pangani Maulendo Obwereza mwa Kugwiritsira Ntchito Brosha la Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Sonyezani mmene tingafunsire funso ndi kupeza yankho m’broshalo. Mwachitsanzo, broshalo limayankha mafunso ngati otsatirawa: Kodi pali chiyembekezo chilichonse kwa akufa? (Masamba 5-6) Kodi kumva chisoni nkulakwa? (Masamba 8-9) Kodi munthu angapirire bwanji chisoni? (Tsamba 18) Kodi ena angathandize motani? (Masamba 20-3) Kodi ana angathandizidwe motani kumvetsa imfa? (Tsamba 25) Kodi Baibulo limapereka chitonthozo chotani? (Tsamba 27) Kenaka, kambitsiranani mwachidule ndi ofalitsa aŵiri aluso mmene agwiritsirira ntchito brosha limeneli pamaulendo obwereza kukayankha mafunso onena za imfa amene nthaŵi zonse anthu amafunsa. Chitirani chitsanzo mmene tingagwiritsirire ntchito broshalo paulendo wobwereza.
Nyimbo Na. 94 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira August 25
Mph. 10: Zilengezo zapamalopo. Kumbutsani onse kupereka malipoti a utumiki wakumunda. Lengezani za makonzedwe a utumiki a pa September 1.
Mph. 15: “Mtsatireni Yesu Mosaleka.” Mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo zokumana nazo za mu Nsanja ya Olonda ya June 1, 1993, tsamba 12.
Mph. 20: Lalikirani ndi Cholinga. Mkulu ndi mtumiki wotumikira mmodzi kapena aŵiri apenda buku la Uminisitala Wathu, masamba 8-12. Gogomezerani kwambiri zifukwa zazikulu zimene tiyenera kukhalira ndi maganizo abwino ndiponso opita patsogolo kulinga ku utumiki wathu ndi kugwirizana kwambiri ndi gulu nthaŵi zonse.
Nyimbo Na. 100 ndi pemphero lomaliza.