Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/97 tsamba 3
  • Kodi Tiyenera Kusamala za Ukhondo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Tiyenera Kusamala za Ukhondo?
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
Utumiki Wathu wa Ufumu—1997
km 8/97 tsamba 3

Kodi Tiyenera Kusamala za Ukhondo?

1 Kodi Yehova amasamala za ukhondo? Inde amatero! Chivumbulutso 11:18 chimati ‘adzawononga iwo akuwononga dziko.’ Chili chifuno chake chenicheni cha kusanduliza pulaneti lathuli kukhala dziko lapansi latsopano loyeretsedwa ndi kusalolamo anthu osafuna kutsatira miyezo yake ya ukhondo. Ndithudi, ngati anthu a mikhalidwe yauve aloledwa kuloŵa m’dziko lapansi latsopano, angaike pangozi kukongola kwake kwauparadaiso. Angadetsenso dziko lapansi ndi kuliwononganso. Motero, Yehova ali ndi chifukwa chomveka pamene akuwamana anthu oterowo moyo wa m’Paradaiso. Ndicho chifukwa chake kuli koyenera kuti tilimbane ndi zizoloŵezi kapena mikhalidwe yauve kuti tikhale aukhondo.

2 M’dongosolo lino, kusunga ukhondo ndi chipambano chenicheni chifukwa dzikoli nlauve. Zimbudzi zambiri za onse nzosatheka kuloŵamo chifukwa cha uve. M’makwalala, pamisika, panyumba ndi m’malo ena kaya apoyera kapena apadera, zinyalala zimangoti mbwee paliponse. Mwa tsoka lake, ngakhale mumpingo mwenimwenimo, zikuoneka kuti ambiri sakuzindikira kuti kuipitsa kapena uve nchiyani.

3 Kuipitsa kungachititsidwe ndi zinthu zonga zakudya zotsala, dothi, mapepala, zitini, mabotolo, zotengera zapulasitiki, zovala zakale, ndi zina zotero. Kumaphatikizapo kutaya chitayetaye zinyatsi ndi kumangoziunjika paliponse ndiko njira ina yofalitsira matenda. Chifukwa chake, zinyalala ndizo chilichonse chotayidwa ndi kusiyidwa pansi. Pamalo a msonkhano, zimaphatikizapo maprogramu a msonkhano wachigawo, wadera ndi wapadera, matishu, totsekera mabotolo, mapulasitiki, mapepala amaswiti, zikamba za zipatso, nyenyeswa za zakudya, ndi zina zotero, zimene zimangotayidwa paliponse.

4 Nchifukwa Ninji Tiyenera Kusunga Ukhondo? Monga Mboni za Yehova, tiyenera kusonkhezereka kukhala osiyana ndi dziko mwa kuyamikira uphungu wa Baibulo wa kuzuliratu dyera, kusalingalira ena, umbombo, ndi kupanda chikondi. Tiyenera ‘kuvula munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake,’ ndipo m’malo mwake ‘tivale watsopano, amene alikukonzeka watsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha Iye amene anamlenga iye.’ Kukonda ukhondo, dongosolo, ndi kukongola kudzatiletsa kuipitsa malo athu.—Akol. 3:9, 10.

5 Ngakhale kuti anthu onse a maganizo abwino amakhumba thanzi labwino ndi moyo wautali, ena samadziŵa kuti kuipitsa kumavulaza thanzi ndipo kumaika anthu pangozi. Malo auve amakhala malo oswerana makoswe, mphemvu, ntchentche ndi mabakitiliya, zomwe zimanyamula matenda. Zinyatsi zosatoledwa ndi zimbudzi za onse zauve zimadzetsa matenda. Chifukwa cha zimenezi anthu ambirimbiri amadwala matenda oyambukira, monga kolera, typhoid, kamwazi ndi chifuŵa cha TB. Matenda otayitsa ndalama zambiri ndi akupha ameneŵa angapeŵedwe mwa kungosamalira uphungu wa m’Baibulo. Chifukwa chake, tonsefe tiyenera kulandira ndi kugwiritsira ntchito uphungu wa m’Malemba wa kusunga miyezo yapamwamba ya ukhondo wakuthupi. Aliyense wa tonsefe ayenera kugwiritsira ntchito zimene wamasalmo ananena kuti: “Chilamulo cha pakamwa panu chindikomera koposa golidi ndi siliva zikwizikwi.”—Sal. 119:72.

6 Ena amaganiza kuti kusunga ukhondo kumalira ndalama zambiri, choncho amangoti anthu osauka sangakhale aukhondo. Komabe, kukhala waukhondo kumadalira kwambiri pa maganizo a munthu koposa ndalama zimene banja limapeza. Mwakhama ndi ndalama pang’ono, Akristu ena m’maiko osauka akhoza kusunga nyumba zawo zili zaukhondo. Talingalirani chochitika cha Joseph, mutu wa banja amene anasonkhezereka kuphunzitsa banja lake kusunga ukhondo, atamvetsera nkhani yonena za ukhondo. Banja lake linkakhala m’nyumba yaing’ono yamatabwa, pakati penipeni pa nyumba zambiri za anansi. Iwo anagwiritsira ntchito chimbudzi cha onse kudzera m’kanjira kosasamalidwa. Ngakhale ndi choncho, Joseph ndi banja lake anayesa kugwiritsira ntchito mapulinsipulo olangiza za ukhondo panyumba. Anaona kuti zimenezi zinathandiza kwambiri banjalo kupeza thanzi labwino ndi kuchepetsa ndalama zotayidwa pa kusamalira matenda. “Ana anga tsopano amavala masandasi, timapukuta mapazi athu, timasamba m’manja ndi sopo ndi madzi ndi kutsatira njira zina zaukhondo. Ana samadwalanso kaŵirikaŵiri, ndipo sitimatayanso ndalama zambiri kuchipatala,” anatero.

7 Pa Nyumba ya Ufumu: Pa Nyumba ya Ufumu timafuna kuthandiza kusunga malowo omwe timagwiritsira ntchito kukhala aukhondo. Kodi timataya zinthu ndi kuzisiya zili mbwee paliponse? Kodi chimbudzi timachisamalira motani? Kodi timataya zinyalala m’Nyumba ya Ufumu kapena pabwalo pake ndi kuyembekezera kuti wina adzazitola? Kodi ntchito ya kusunga ukhondo timangoisiyira gulu loyeretsa holo mlunguwo? Ndithudi zoyesayesa zathu zidzathandiza kwambiri kusungitsa ukhondo ngati nthaŵi zonse timazindikira kufunika kwake kwa kusunga bwino malo athu kuti asaipitsidwe.

8 Kuganizira ena ndicho chizindikiro cha Chikristu choona. Ndicho chifukwa chake Yesu Kristu anati lachiŵiri pa malamulo aakulu koposa ndi ili: “Uzikonda mnzako monga udzikonda mwini.” (Marko 12:31) Kodi zimenezo sindizo zimene muyenera kuchita? Chikondi chaumulungu pa mnansi chiyenera kutisonkhezera kuti tisonyeze ulemu pa zinthu kaya za anthu onse kapena za mwini ndi kusataya zinyatsi paliponse.

9 Kunena za kuchitira umboni kwathu poyera, kaŵirikaŵiri timadziŵika kwambiri kumene timakhala. Kukhala ndi nyumba yaudongo ndi yadongosolo, mkati ndi kunja komwe, mwa iko kokha kumapereka umboni ku dziko. Ngati tikhala auve, kodi atsopano adzalingalira motani? Kodi adzakuona motani kulambira koona? Mwa zimene amaona kwa ife, iwo angakopeke ndi gulu la Yehova kapena angalifutuke. Tonsefe timagaŵana thayo limeneli, motero tikufuna kutsimikiza kuti zimene ena akuona ziyenera kuwakopera ku gulu la Yehova laukhondo. Monga momwe mtumwi Paulo ananenera: “Chifukwa chake mungakhale mudya, mungakhale mumwa, mungakhale muchita kanthu kena, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu. Khalani osakhumudwitsa.”—1 Akor. 10:31-32.

10 Brosha lakuti Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? limavomereza kuti pamafunikira khama lenileni kuti munthu asunge ukhondo wakuthupi chifukwa tikukhala m’dziko lodetsedwa. Komabe, sitiyenera kugwa mphwayi chifukwa Yehova ali waukhondo ndi woyera m’njira iliyonse. Ponena za ukhondo wakuthupi broshalo limati: “Chifukwa chakuti Akristu amaimira Mulungu, iwo ayenera kusunga matupi awo ali oyera limodzi ndi zovala zawo. Tiyenera kusamba kumanja titachoka kuchimbudzi, ndipo tiyenera kusambanso kumanja tisanadye chakudya kapena kugwira chakudya. Ngati mulibe zimbudzi, muyenera kufotsera zonyansazo. (Deuteronomo 23:12, 13) Kukhala woyera kuthupi kumapatsa thanzi labwino. Nyumba ya Mkristu iyenera kukhala yaukhondo ndi yoyera mkati ndi kunja komwe. Iyenera kuonekera kumaloko monga chitsanzo chabwino.”—Phunziro 9, ndime 1 ndi 5.

11 Tingatenge phunziro ku mtundu wakale wa Israyeli. Mtunduwo unali wosiyanadi ndi ena, chifukwa cha muyezo wa ukhondo umene Yehova anawaphunzitsa. Pazimenezi, Insight Voliyumu 1 imati: “Makhalidwe awo aliyense payekha anachititsa mtundu wa Israyeli kukhala ndi thanzi labwino kuposa ena, mosasamala kanthu za umoyo wawo wopupulika m’chipululu kwa zaka 40. Malamulo a Mulungu olamulira moyo wawo pamsasa, ophatikizapo kupima ndi kuchiritsa matenda, ndiwodi anatheketsa zimenezi. Makonzedwe ameneŵa anagogomezera kufunika kwake kwa madzi oyera. Si nyama zonse zimene zinaikidwa m’gulu la zoyera zoyenera kudya. Malangizo otetezera anasonyeza kasamaliridwe ndi katayidwe ka mitembo. Kubindikiza kunakhala monga chochinga matenda oyambukira kuti asafalikire. Kufotsera zonyansa za munthu kunali chofunika chaukhondo chapatsogolo kwambiri poyerekezera ndi nthaŵi yawo. (Deut. 23:12-14) Malangizo pa zakusamba kaŵirikaŵiri ndi kuchapa zovala analinso makonzedwe opindulitsa pa mpambo wa malamulo wa mtunduwo.”

12 Malo a Misonkhano Yaikulu: Vuto lalikulu limakhala pamisokhano yaikulu kumene kumasonkhana anthu ochuluka kwambiri. Pangakhale zinyatsi zambiri za zakudya, zakumwa ndi zinthu zina zomwe timadza nazo ndi kuzitaya pamalo a msonkhano. Koma ngati nthaŵi zonse timazindikira mbali imene mmodzi ndi mmodzi wa ife angachite pakusungitsa ukhondo, pambuyo pake sipadzakhala ntchito yaikulu yoyeretsa. Maenje amakumbidwa pamalo oyenerera kuti tizitayiramo zinyalala.

13 Ponena za malamulo amene Yehova anapatsa mtundu wa Israyeli, buku la Chimwemwe cha Banja limati: “Limodzi la malamulo amenewo linali la katayidwe ka zonyansa za munthu, zimene zinayenera kufotseredwa bwino kutali ndi msasa kotero kuti malo okhalako anthu asaipitsidwe. (Deuteronomo 23:12, 13) Lamulo lakale limenelo lidakali uphungu wabwino. Ngakhale lerolino anthu amadwala ndi kufa chifukwa chosawatsatira.” (Onani Chimwemwe cha Banja, masamba 45-9, ndime 12-20, kuphatikizapo mawu amtsinde pa ndime 16.)

14 Ndandanda Yoonerapo Ingathandize: Nkhani yonena za ‘Kulimbana ndi Vuto la Udongo’ mu Galamukani! wa October 8, 1988, inapereka malingaliro omwe angagwiritsiridwe ntchito kusunga ukhondo panyumba. Kunena zoona, malinga ndi kumene anthu akukhala ndi mtundu wa nyumba yomwe ali nayo, akhoza kugwiritsira ntchito njira zina zokhalira ndi ukhondo umodzimodzi. Mwachitsanzo, kumene amagwiritsira ntchito zimbudzi zokumba, angasunge ukhondo mwa kutsimikiza kuti amagwiritsira ntchito mankhwala ophera tizilombo. Kumene mankhwalawo samapezeka, angagwiritsire ntchito laimu kapena maphulusa chifukwa nazonso zili ndi mphamvu. Chiboo chiyenera kukhala ndi chotsekerapo ndi kumatsekedwa pamene sichikugwiritsiridwa ntchito. Kumene amagwiritsira ntchito zimbudzi zogujumula, angasunge ukhondo mwa kutsimikiza kuti chokhalapocho, mbale yake, sinki ndi zina za m’chimbudzi zimatsukidwa nthaŵi zonse ndi mankhwala. Nkothandiza kukhala ndi ndandanda ya zinthu zoyenera kuchita. Ndandanda yoonerapo yotero iyenera kuphatikizapo zonse kuti pasakhale mbali imene idzanyalanyazidwa. Zoyenera kuchita zingagaŵidwe m’magulu onga aŵa: Zochita Poyeretsa Chimbudzi, Zochita Mkati mwa Nyumba, Zochita Panja.

15 Posonyeza kufunika kwa kuyeretsa bwinobwino, Galamukani! ameneyo anati: ‘Musakhale ndi maganizo akuti zoonekera zokha ndizo ziyenera kukhala zaudongo. Ena amalingalira kuti kutsogolo kwa nyumba kuyenera kukhala kwaukhondo, koma zilibe kanthu ngati kumbuyo kungakhale kwauve; kuti chipinda chochezeramo chifunikira kuoneka bwino, koma zilibe kanthu ngati chipinda chogonamo chingakhale chosasamalika kapena ngati zipupa za m’khichini zingakhale zakuda ndi litsiro lakumanja ndi utsi. Kusasamala bwino koteroko kumatikumbutsa mawu a Yesu kwa Afarisi: “Mutsuka kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma mkatimo iwo adzala ndi kulanda . . . yambotsuka mkati mwa chikho ndi mbale, kuti kunja kwake kukhalenso koyera.”’—Mat. 23:25, 26.

16 Musapatse Yehova Chifukwa Chakuti Atipotolokere: Yehova akunena kuti adzatipotolokera ngati aona kanthu kena konyansa pakati pathu. (Yerekezerani ndi Deuteronomo 23:14.) Chifukwa chake, nkofunika kwambiri kuti tisunge ukhondo kotero kuti njira yathu ya moyo igwirizane ndi muyezo wake. Tiyeni tonse tiyeseyese kusunga ukhondo wakuthupi ndi kusamalira malo athu kuti asadetsedwe, makamaka Nyumba za Ufumu ndi malo ena osonkhanira, kotero kuti Yehova asaone ‘kanthu kodetsa mwa ife.’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena