Misonkhano Yautumiki ya October
Mlungu Woyambira October 5
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu Waufumu.
Mph. 15: “Tinapindula ndi Misonkhano Yachigawo ya ‘Njira ya Moyo ya Mulungu.’” Mafunso ndi mayankho. Sonyezani buku ndi brosha latsopano ndipo tchulani njira zimene tingagwiritsire ntchito bwino mabukuwa.
Mph. 20: “‘Kufesa Mbewu za Ufumu’ pa Njira za Magazini.” Kukambitsirana ndi omvetsera. Ena alongosole mmene anayambira ndi kusungira njira ya magazini. Ndiyeno chitirani chitsanzo ulaliki wa magazini umene makonzedwe akupangidwa odzabweretsa makope otsatira. Perekani malingaliro a mmene tingatchulire za chopereka mochenjera.
Nyimbo Na. 133 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 12
Mph. 5: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 10: “Oyang’anira Amene Amatitsogolera—Mlembi.” Nkhani ya mlembi wampingo, alongosole ntchito zake. Agogomezere kuti onse angagwirizane naye mwa kupereka malipoti autumiki wakumunda mwachangu.
Mph. 10: Ali ndi Mzimu Wachimwemwe Waupainiya. Nkhani yolimbikitsa kuchokera mu 1998 Yearbook, masamba 104-7. Fotokozani chifukwa chake ku Japan kuli apainiya ochuluka, chimene chimapangitsa akazi apanyumba ochuluka kuika zinthu zauzimu pamalo oyamba, chimene chimasonkhezera aliyense wofunsira kuchita upainiya, ndi amene ali ochuluka mwa apainiya onse. Sonyezani ziyambukiro zabwino zimene makolo ochita upainiya amakhala nazo. Sonyezani chikhulupiriro chimene chimafunikira kuti munthu apange masinthidwe ofunikira pamoyo wake kuti achite upainiya. Limbikitsani onse kuti aganizire mozama ndi mwapemphero kuti apendenso ziyembekezo zawo zochita upainiya.
Mph. 20: “Kodi Magaziniwo Mumawaŵerenga?” Mafunso ndi mayankho. Onani malingaliro othandiza pokonza ndandanda yaumwini yoŵerengera amene ali mu Bukhu Lolangiza la Sukulu, phunziro 4, ndime 5-6.
Nyimbo Na. 107 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 19
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Pendani mfundo zokambitsirana m’magazini atsopano. Simbani zokumana nazo zomwe zili mu 1997 Yearbook, tsamba 45 ndi Galamukani! wa May 8, 1998, tsamba 32. Limbikitsani onse kuti agaŵire nawo magazini mapeto a mlungu uno.
Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 20: Mmene Mungakonzekerere Phunziro la Nsanja ya Olonda. Kukambitsirana ndi omvetsera kochitidwa ndi wochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda, kozikidwa pa Nsanja ya Olonda ya November 1, 1986, masamba 13-14, ndime 16-18 ndiponso mu Bukhu Lolangiza la Sukulu, phunziro 7, ndime 11, ndi phunziro 18, ndime 4-6. Pemphani ndemanga pamafunso aŵa: (1) Nchifukwa chiyani kuli kofunika kuti tizipindula kotheratu ndi nkhani iliyonse yophunziridwa mu Nsanja ya Olonda? (2) Kodi tiyenera kuchitanji pamene talandira kope latsopano? (3) Kodi njira yabwino yokonzekerera Phunziro la Nsanja ya Olonda ndi yotani? (4) Kodi malemba amene asonyezedwa koma sanagwidwe mawu ndi mutu waphunziro tiyenera kuziona motani? (5) Kodi tingabwereremo bwanji m’zimene tinaphunzira? (6) Kodi ndi nsonga zikuluzikulu zotani zimene tiyenera kusinkhasinkhapo pamene tamaliza phunziro laumwini pa zophunziridwazo? (7) Kodi tingakonzekere bwanji kupereka ndemanga? (8) Ndi motani mmene tingaperekepo ndemanga zosiyanasiyana pafunso limodzi? Ena alongosole zimene iwo achita kuti ziwathandize kupeza phindu lalikulu pa Phunziro la Nsanja ya Olonda.—Onaninso Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, masamba 65-7.
Nyimbo Na. 95 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira October 26
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Tchulani zofalitsa zakale zimene mpingo uli nazo ndi zimene zingagaŵiridwe mu utumuki pamene mpata wapezeka. Popeza kuti kudzakhala maholide mu November ndi December, imeneyi ingakhale nthaŵi yabwino yoti achinyamata obatizidwa ndi enanso aganizire zochita upainiya wothandiza.
Mph. 20: Kumvera Kwaumulungu m’Banja la Zipembedzo Zosiyana. Nkhani yozikidwa pa Nsanja ya Olonda ya June 1, 1995, masamba 26-9. Perekani chilimbikitso chabwino ndi uphungu wokoma zimene zidzathandiza amene ali ndi anzawo a muukwati osakhulupirira kukhalabe ndi malingaliro abwino ndi kumagwirizana nthaŵi zonse ndi mpingo.
Mph. 15: Kufika Pamisonkhano Panthaŵi Yake. Kukambitsirana ndi ochititsa Phunziro la Buku la Mpingo aŵiri kapena atatu, kapena ndi atumiki otumikira pavuto la kufika mochedwa pamisonkhano. Akuvomereza kuti mikhalidwe yakamodzikamodzi, monga ngati zochitika zamwadzidzidzi, nyengo, kuchuluka kwa magalimoto, ndi zina, ingachedwetse aliyense. Komabe, ena nchizoloŵezi chawo kuchedwa. Molimbikitsa, kaguluko kakambirane ndi kuchitira fanizo zimene zimafunika kuti munthu azifika panthaŵi yake: (1) kuyamikira ndi mtima wonse mwayi wopezeka pamisonkhano kuphatikizapo chakudya chauzimu ndi mayanjano amene amakhalapo, (2) kukonzekeratu bwino pasadakhale ndi kulinganiza zochita zaumwini, (3) kugwirizana mofunitsitsa kwa onse a m’banja, (4) kunyamuka mofulumira ndi kupereka mpata wa mavuto osawayembekezera, ndi (5) kumadzimva kuti sufunika kusokoneza ena amene ali pamsonkhanopo. Onse akugwirizana kuti vuto limeneli lofika mochedwa lingathetsedwe mwa kuyesayesa kuwongolera nthaŵi zonse.
Nyimbo Na. 86 ndi pemphero lomaliza.