Mwayi wa Ana
1 Onse amene ali makolo pakali pano amakumbukira bwinobwino mwayi umene anali nawo monga ana okulira m’choonadi—mwayi wa ntchito ya Tsiku la Magazini. Ntchito imeneyi inayamba m’mipingo yonse m’chaka cha 1949. Tsiku limodzi pamlungu, aliyense anayenera kuika maganizo pa kugaŵira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! mumsewu, kunyumba ndi nyumba, kusitolo ndi sitolo, ndi mwa njira zina. Makamaka ofalitsa achinyamata ankayembekezera kwambiri kuchita nawo ntchito imeneyi chifukwa inkawapatsa mpata wochita ntchito yofanana ndi achikulire mu mpingo. Kodi munali kuchita zimenezi muli wamng’ono?
2 Phatikizanimo Ana Anu: Ana ang’onoang’ono kwambiri amene sangathe kuyamba kukambirana za Malemba panyumba ya munthu angathe kugaŵira magazini. Kumangofunika kuphunzira ulaliki wosavuta wa ziganizo zingapo zazifupizifupi basi. Kukamba ndemanga yachidule, mwinamwake pazithunzi zapachikuto, kungakhale kokwanira. Eninyumba ambiri savuta kulandira magazini kwa ana athu, nthaŵi zina amanena zabwino ponena za kuona mtima ndi khalidwe labwino la achinyamata ameneŵa. Mwa kuwathandiza pang’ono chabe, utumiki umenewu n’chinthu chimene ana angachite bwino kwambiri, kuthandiza kwambiri kufalitsa uthenga wa Ufumu. N’zoona, pamene ana akukula, makolo awo adzafuna kuwathandiza kuti apitirize kupita patsogolo pokulitsa maluso awo ochitira umboni.
3 Manuel anayamba kulalikira ku khomo ndi khomo ali ndi zaka zitatu zakubadwa. Makolo ake anam’phunzitsa kuloŵeza pamtima ulaliki wachidule. Iye amalalikira mwachangu pamodzi ndi makolo ake, kugaŵira magazini, mabulosha, ndi mathirakiti ochuluka. Amachitanso umboni wamwamwayi. Nthaŵi ina makolo ake atapita naye kukasangalala kumalo osungirako zinyama, anayamba kugaŵira mathirakiti kwa anthu ena amene anali kumeneko. Ngakhale kuti akadali wamng’ono kwambiri, changu cha Manuel pa utumiki chimalimbikitsa makolo ake ndiponso mpingo wonse.—Miy. 22:6.
4 Loŵeruka lililonse pa Kalendala ya Mboni za Yehova ya 2000 laikidwa kukhala “Tsiku la Magazini.” Makolo, tikukulimbikitsani kuti mukhalenso ndi chidwi mu ntchito imeneyi, thandizani ana anu kuchita nawo mwayi wa utumiki umenewu mokhazikika momwe angathere.