Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira May 8
Mph. 5: Zilengezo za pampingo ndi zilengezo zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu.
Mph. 25: “Makonzedwe Athu Opepukitsidwa a Kagaŵidwe ka Mabuku.” Mkulu woyeneretsedwa apende nkhaniyi ndi omvetsera. Mkuluyo angaphatikizeponso mfundo za m’kalata yochokera ku Sosaite ya October 15, 1999. Ndiyeno wofalitsa wozoloŵera achite chitsanzo cha mmene angagwiritsire ntchito chidziŵitso chimene chili m’nkhaniyo mu utumiki wakumunda. Pogwiritsira ntchito imodzi ya magazini atsopano amene akagaŵiridwe mu utumiki wakumunda mapeto a mlungu uno, wofalitsa akambirane ndi mwininyumba nkhani imodzi ya m’magaziniyo. Wofalitsa asonyeze mwininyumba mfundo ina m’magaziniyo, mwininyumba anene kuti: “N’losangalatsa.” Wofalitsa anene kuti: “Ndingakonde kukusiyirani magaziniyi kuti muŵerenge nkhani imeneyi komanso nkhani zonse m’magaziniyi.” Mwininyumba afunse kuti: “Mumagulitsa ndalama zingati?” Wofalitsa ayankhe kuti: “Alibe mtengo, chofunika n’choti muŵerenge. Mutha kuona apa patsamba la ofalitsa kuti magaziniyi ndi mbali ya ntchito yophunzitsa Baibulo ya padziko lonse ndipo imachirikizidwa ndi zopereka zaufulu. [Muonetseni chiganizo cha patsamba 4 la Galamukani! ndiponso patsamba 2 la Nsanja ya Olonda m’danga la m’munsi kudzanja lamanja.] Ndine m’modzi wa Mboni za Yehova zoposa 5 miliyoni zimene zikupereka nthaŵi ndiponso zinthu zawo kuti ntchito yofunika imeneyi igwiridwe m’mayiko oposa 200. Ngati ena angafune kupereka kangachepe kothandiza ntchitoyi, tidzalandira ndi manja aŵiri.” Mwininyumba apereke choperekacho ndipo wofalitsayo achiike mu envulopu imene ali nayo yoikamo ndalama za ntchito yapadziko lonse. Athokoze chifukwa cha choperekacho ndipo anene kuti nthaŵi ina adzabweranso ndi makope ena a magazini. M’chitsanzo chachiŵiri chachidule, onetsani mmene wofalitsa sakusiyira buku mwininyumba chifukwa chakuti alibe chidwi chenicheni ndi uthenga wa Ufumu, ngakhale kuti ndi wofuna kulankhula naye. M’chitsanzo chachitatu chachidule, onetsani mmene tingaperekere thirakiti kwa munthu amene akusonyeza chidwi chenicheni koma amene panthaŵiyo ali wotanganidwa kwambiri ndipo zikuoneka kuti nthaŵi ngati imeneyi sikoyenera kumufotokozera mmene ntchito yathu yapadziko lonse imachirikizidwira. Wofalitsa akulonjeza kudzabweranso nthaŵi ina yabwino. Akadzafikakonso adzayesetsa kuona ngati mwininyumba uja alidi wachidwi ndi ntchito yathu, ndipo ngati ndi choncho, afotokoze mmene ulaliki wathu umayendera ndiponso mmene ntchitoyi imachirikizidwira.
Mph. 15: “Kuthandiza Ena pa Phunziro la Buku la Mpingo.” Mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi mkulu amene ali wochititsa phunziro la buku wodziŵa bwino.
Nyimbo Na. 201 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 15
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.
Mph. 15: “Kodi Ndinu Nokha M’banja Mwanu Amene Muli M’choonadi?” Kukambirana nkhaniyi mwa mafunso ndi mayankho. Sonyezani zinthu zabwino zimene ofalitsa ameneŵa akuchita ndi mmene akuchitira ndi mkhalidwe wawowo. Gogomezerani mmene ena angawathandizire ndiponso chifukwa chake timayamikira chitsanzo chawo chabwinocho. Tikufunika kudziŵa onse amene ali mu mkhalidwe woterewu mu mpingo ndipo tione aliyense payekha mmene tingawathandizire ndi kuwalimbikitsa.
Mph. 20: “Kodi Mumapanga Zolinga Zauzimu Monga Banja?” Kukambirana mwa mafunso ndi mayankho. Ŵerengani ndime ndi malemba ngati nthaŵi ilipo.
Nyimbo Na. 203 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 22
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Pendani Bokosi la Mafunso.
Mph. 20: “Dikirani.” Kukambirana mwa mafunso ndi mayankho. Fotokozani chifukwa chake kuli kofunika kwambiri kuti tikhale ogalamuka mwauzimu ngakhale kuti sitikudziŵa tsiku ndi nthaŵi.—Onani Nsanja ya Olonda ya November 1, 1995, tsamba 20.
Mph. 15: Chikhulupiriro. Kuchokera mu buku la Kukambitsirana, masamba 67-70. Mkulu akambirane ndi gulu la achinyamata. Mkulu afotokoze tanthauzo la chikhulupiriro, ndiyeno awafunse anyamatawo mafunso. Chifukwa chiyani tingakhale opanda chikhulupiriro? N’chiyani chimene chili maziko achikhulupiriro chathu? Kodi ndi motani mmene tingakhalire ndi chikhulupiriro cholimba? Kodi tingasonyeze motani chikhulupiriro choterocho? Mkuluyo amalize mwakuyamikira ndiponso kulimbikitsa achinyamatawo.
Nyimbo Na. 83 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira May 29
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani onse kupereka malipoti awo a muutumiki wakumunda a May. Sonyezani chitsanzo chachidule cha kugaŵira mabuku mu June. Onetsani mmene mungayambire phunziro la Baibulo, pogwiritsa ntchito phunziro 13 mu bulosha la Mulungu Amafunanji.
Mph. 15: “Kupeza Chimwemwe mu Utumiki Wanu Wopatulika.” Nkhani. Kambani zifukwa zimene timakhalira achimwemwe mu utumiki wathu.—Onani w95-CN 1/15 tsamba 19, ndime 13-15. Tchulani zimene tingachite kuti tipeze chimwemwe chochuluka.
Mph. 18: Kuŵerenga Baibulo Kumene Kuli Kopindulitsa. Nkhani ndi chitsanzo kuchokera mu Buku Lolangiza la Sukulu, masamba 34-5, ndime 6-7. Pulogalamu yolinganizidwa yoŵerenga Baibulo, pamene pamachokera mfundo zazikulu za Baibulo, ndi mbali ya maphunziro a Sukulu ya Utumiki Wateokalase. (Utumiki Wathu wa Ufumu, wa December 1999, tsamba 7) Pemphani banja lichite chitsanzo cha mmene banja likanakonzekerera kuŵerenga kwa mlungu uno kwa pasukulu. Asankhe mfundo yosangalatsa imodzi kapena ziŵiri ndipo afufuze zowonjezereka. Sonyezani mmene kuŵerenga Baibulo kungakhalire kwatanthauzo, kutikonzekeretsa bwino ‘kulunjika nawo bwino mawu a choonadi.’—2 Tim. 2:15.
Nyimbo Na. 95 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira June 5
Mph. 5: Zilengezo za pampingo.
Mph. 10: Zosoŵa za pampingo.
Mph. 15: “Mwayi wa Ana.” Nkhani ndi kukambirana ndi omvetsera. Phatikizanipo zokumana nazo za mu Nsanja ya Olonda ya December 1, 1996, tsamba 13, ndime 15. Pemphani ana kunena mmene anasangalalira kugaŵira magazini. Mwana mmodzi kapena aŵiri asonyeze ulaliki wogaŵira magazini wosavuta wa kukhomo ndi khomo. Limbikitsani makolo kutenga ana awo mlungu uliwonse kogaŵira magazini.
Mph. 15: “‘Ayesedwe’—Motani?” Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Pendani zifukwa za m’Malemba zokhalira ndi atumiki otumikira mu mpingo. Sonyezani ziyeneretso zimene ayenera kukhala nazo kuti asankhidwe. (Onani buku la Olinganizidwa, masamba 55-7.) Tchulani njira zimene atumiki otumikira angatumikirire, ndipo limbikitsani abale ambiri kukalamira mwayi umenewu.
Nyimbo Na. 82 ndi pemphero lomaliza.