Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/01 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira May 14
  • Mlungu Woyambira May 21
  • Mlungu Woyambira May 28
  • Mlungu Woyambira June 4
Utumiki Wathu wa Ufumu—2001
km 5/01 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira May 14

Nyimbo Na. 3

Mph. 10: Zilengezo za pampingo ndi zosankhidwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu.

Mph. 15: Kodi Mudzachita Chiyani m’Chilimwe? Mkulu kapena mtumiki wotumikira akambirane ndi banja lake zimene adzachite m’miyezi yachilimwe. Akambirane zopezeka pamsonkhano wachigawo masiku onse, kuchita upainiya wothandiza kapenanso kupita kutchuti ndiponso kokasangalala. Onse avomereze kusanyalanyaza zinthu za teokalase monga kupezeka pamisonkhano ya mpingo, utumiki wakumunda, ndiponso kuchita phunziro la Baibulo la banja, ngakhale apite kwina. Adzaonetsetsa kuti ampatsa mlembi malipoti awo a utumiki wakumunda mofulumira, kaya ali kwawo kapena kwinakwake.

Mph. 20: “Kodi Mumayamikira Makonzedwe Opepukitsidwa Akagaŵidwe ka Mabuku?” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ŵerengani ndime 4-6.

Nyimbo Na. 31 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira May 21

Nyimbo Na. 52

Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti.

Mph. 12: Tisanyalanyaze Malo Athu Olambirira. Kukambirana mwa mafunso ndi mayankho kuchokera m’buku la om—CN, masamba 60-64 pakamutu kakuti, “Nyumba ya Ufumu.” Ŵerengani ndime zambiri. Gwiritsani ntchito kwambiri malemba ngati nthaŵi ilipo.

Mph. 25: “Kuphunzira Pakati pa Anthu a Mulungu.” Ikambidwe ndi woyang’anira Sukulu ya Utumiki Wateokalase. Phatikizanipo “Malangizo Pophunzitsa Achikulire Kuŵerenga ndi Kulemba.” Kambirananinso bokosi la “Kuŵerenga Mokweza.” Limbikitsani ofuna kudziŵa kuŵerenga ndi kulemba kupeza nawo mwayi pamakonzedwe achikondi amenewa mofulumira.

Nyimbo Na. 105 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira May 28

Nyimbo Na. 58

Mph. 13: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti autumiki wakumunda a May. Kambiranani Bokosi la Mafunso.

Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 17: “Mawu a Mulungu. . . Amapatsa Mphamvu.” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo zitsanzo ziŵiri zokonzedwa bwino, zosonyeza mmene ulaliki wachidule ungakhalire wa m’Mawu a Mulungu.

Nyimbo Na. 79 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira June 4

Nyimbo Na. 100

Mph. 12: Zilengezo za pampingo ndi zokumana nazo muutumiki wakumunda.

Mph. 15: “Gwirani Nawo Ntchito Yotuta Mokwanira.” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pokambirana ndime 4, tchulaninso chitsanzo cha mu Nsanja ya Olonda ya September 15, 1996 patsamba 19, ndime 10, kusonyeza zimene ena akuchita kuti awonjezere zomwe akuchita mu utumiki.

Mph. 18: “Tafola Gawo Lathu Kambirimbiri!” Kambani mawu oyamba m’mphindi yosaposa imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Woyang’anira utumiki akambe nkhaniyi. (Mipingo imene ili ndi magawo ofoledwa mwa apo ndi apo ipende nkhani yakuti “Magazini Amalengeza Ufumu,” mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa April 1998.) Kambani zimene mpingowo ungachite kuti usamadumphe malo ena pofola gawo. Phatikizanipo zokumana nazo za mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 1996, patsamba 26. Nenani kufunika kosunga bwino cholembapo za kunyumba ndi nyumba, kupitanso kwa amene sitinawapeze panyumba, ndi kuchita maulendo obwereza mofulumira.

Nyimbo Na. 142 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena