Kulalikira Ufumu Kumathandiza Kupulumutsa Anthu!
1 Masiku ano padziko lonse lapansi pakuchitika ntchito yofunika kwambiri. Yehova Mulungu, Yesu Kristu, ndi angelo ambirimbiri maganizo awo onse ali pantchito yomweyi. Kodi ndi ntchito yanji, ndipo n’chifukwa chiyani ili yofunika? Ndi ntchito yolalikira Ufumu, ndipo imathandiza kupulumutsa anthu.—Aroma 1:16; 10:13, 14.
2 Anthu ena amaganiza kuti tingathandize kwambiri zikanakhala kuti timayesetsa kusintha dzikoli kukhala labwino. Anthu ambiri akuyesetsa kuti apeze mtendere, achize matenda, ndi kuthetsa mavuto a zachuma. Koma kodi chingathandize kwambiri anthu n’chiyani?
3 Ntchito Yofunika Kwambiri: Ndi uthenga wa Ufumu wokha umene umanena cholinga cha moyo, chinayambitsa kuti anthu azivutika, ndiponso zinthu zodalirika zimene tiyenera kuyembekezera. Uthenga wabwino umathandiza anthu kukhala mabwenzi a Yehova ndipo amalandira “mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse.” (Afil. 4:7) Ndi uthenga wa Ufumu wokha umene uli ndi malangizo abwino othandiza anthu kupirira mavuto amene amapeza pa moyo masiku ano ndiponso umafotokoza zimene angachite kuti akapulumuke pamene dziko loipali lidzawonongedwa. (1 Yoh. 2:17) Kodi pamenepa, si pofunika kulalikira Ufumu mwakhama?
4 Mwachitsanzo: Kodi njira yabwino yothandizira anthu m’mudzi amene agona kuti apeŵe ngozi ya damu limene liphulike nthaŵi ina iliyonse ingakhale iti? Kodi ingakhale yokapa madzi m’damulo? Kukongoletsa mudziwo? Ayi, koma kudzutsa anthu m’mudzimo, kuwachenjeza za ngoziyo, ndi kuwathandiza kuti athaŵe. Anthu amene ali mtulo mwauzimu lerolino ali pangozi yoopsa. (Luka 21:34-36) Popeza dongosolo lino la zinthu litha posachedwapa, tiyeni tiyesetse kuwalalikira mwachangu kwambiri anthu omwe tingathe.—2 Tim. 4:2; 2 Pet. 3:11, 12.
5 Ilimbikireni Ntchitoyi: Tiyeni tifunefune njira zimene tingafikire anthu ambiri oona mtima ndi uthenga wabwino—m’nyumba zawo, mumsewu, patelefoni, ndi mwamwayi. Ntchito imene Yehova watipatsa kuti tigwire ndi yofunika kwambiri kuposa ina iliyonse. Tikaigwira mwachangu, ‘tidzadzipulumutsa tokha ndi iwo akutimvera.’—1 Tim. 4:16.