Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/02 tsamba 7
  • Zilengezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zilengezo
  • Utumiki wathu wa Ufumu—2002
Utumiki wathu wa Ufumu—2002
km 4/02 tsamba 7

Zilengezo

◼ Mabuku ogaŵira mu April ndi May: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ngati mwapeza munthu wachidwi paulendo wobwereza, muikeni pandandanda ya anthu amene mumakawagaŵira magazini. Gaŵirani bulosha la Mulungu Amafunanji n’cholinga choyambitsa maphunziro a Baibulo. June: Kodi Mulungu Amafunanji kwa Ife? kapena Chidziŵitso Chotsogolera ku Moyo Wosatha. Ngati eninyumba ali nazo kale zofalitsa tatchulazi, gaŵirani bulosha loyenera limene mpingo uli nalo. July: Mungagwiritse ntchito lililonse la mabulosha a masamba 32 awa: Boma Limene Lidzabweretsa Paradaiso, Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, Kodi Chifuno cha Moyo Nchiyani? Kodi Mungachipeze Motani?, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Kodi Muyenera Kukhulupirira Utatu?, Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira, Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, ndiponso “Taonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano.” Mabulosha a Buku la Anthu Onse ndiponso Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi? mungawagaŵire pamene kuli koyenera kutero.

◼ Miyezi ikubwerayi, mabaji a msonkhano wachigawo wa 2002 a Chicheŵa, Chingelezi ndi Chitumbuka abwerera pamodzi ndi mabuku. Simukufunika kuitanitsa zimenezi. Mabaji adzaikidwa m’mipukutu ya mabaji 20, malinga ndi kukula kwa mpingo uliwonse. Ngati mipingo ikufuna mabaji ena, itanitsani pa Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Funsirani mapulasitiki oikamo mabaji ngati ena pampingopo akuwafuna.

◼ Sosaite imafunika kukhala ndi maadiresi ndi manambala a telefoni amene akugwira ntchito panopo a oyang’anira otsogolera ndi alembi onse m’kaundula wake. Komiti ya Utumiki ya Mpingo iziti zimenezi zikangosintha nthaŵi ina iliyonse, izilemba fomu ya Kusintha Keyala ya Woyang’anira Wotsogolera/Mlembi (S-29) ndi kuitumiza mwamsanga ku ofesi ya nthambi.

◼ Alembi a mipingo azisunga mafomu okwanira a Chofunsirapo Utumiki wa Upainiya Wokhazikika (S-205) ndi Chofunsirapo Utumiki wa Upainiya Wothandiza (S-205b). Angaode mafomuwa pogwiritsa ntchito Fomu Yofunsira Mabuku (S-14). Sungani okwanira chaka chimodzi. Pendani mafomu a ofunsira upainiya wokhazikika kuti mutsimikizire kuti alembedwa bwino. Ngati wofunsirayo sakukumbukira tsiku limene anabatizidwa, angoyerekeza tsikulo ndiyeno asunge limenelo.

◼ Ngati mukukonza zopita kudziko lina ndipo mukufuna kukapezeka pamisonkhano ya mpingo, msonkhano wadera, kapena msonkhano wachigawo, funsani masiku, nthaŵi, ndi malo a misonkhanoyo ku ofesi ya nthambi imene imayang’anira ntchito m’dziko limene mukupitalo. Maadiresi a maofesi a nthambi ali patsamba lomaliza la Yearbook yatsopano.

◼ Tikukukumbutsani kuti masabusikiripishoni a Kagulu akutha, choncho amene munalembetsa akatha musalembetsenso ena. Anthu amene amakhala kutali ndi mpingo ndi amene azilembetsa magazini kuti azilandira papositi.

◼ Mipingo iyambe kufunsira mabaundi voliyumu a Watchtower ndi Awake! a 2001. Mabaundi voliyumuwa adzakhalapo m’Chingelezi. Adzaonekera monga “Zoyembekezeredwa” pa mipambo yolongedzera katundu wa mipingo kufikira pamene mabaundi voliyumu adzakhalapo ndi kutumizidwa.

◼ Zofalitsa Zatsopano Zimene Zilipo:

Moyo Wokhutiritsa—Mmene Mungaupezere—Chicheŵa, Chingelezi, Chitumbuka

Kodi Muli ndi Mzimu Wosafa? (Thirakiti Na. 25)—Chicheŵa, Chingelezi, Chitumbuka

Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu—Chicheŵa, Chingelezi, Chitumbuka

Ulosi wa Yesaya—Muuni wa Anthu Onse 2—Chicheŵa, Chingelezi

Ulosi wa Yesaya—Muuni wa Anthu Onse 2—La Zilembo Zikuluzikulu—Chingelezi

◼ Kompakiti Disiki Yatsopano Imene Ilipo:

Respect Jehovah’s Authority—Chingelezi

◼ Kaseti Yatsopano Imene Ilipo:

Respect Jehovah’s Authority—Chingelezi

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena