Kodi Tingatani Kuti Mabanja Athu Akhale Olimba Mwauzimu?
1 Tikuyamikira mabanja achikristu chifukwa ‘chosonyeza kudzipereka kwaumulungu m’mabanja awo.’ (1 Tim. 5:4, NW) Koma chifukwa chakuti zinthu zoipa zimene zingafooketse chikhulupiriro chathu zachuluka, mabanja akufunika kuyesetsa kuti akhale olimba mwauzimu. Kodi tingachite motani zimenezi?
2 Tsanzirani Kristu Monga Mutu: Mitu ya mabanja ifunika kutsanzira Yesu Kristu posamalira ntchito yawo yolimbitsa mabanja awo. Yesu atasonyeza kutikonda mwa imfa yake ya nsembe, anapitiriza ‘kudyetsa ndi kusamalira mpingo. (Aef. 5:25-29, NW) Makolo achikondi amatsatira chitsanzo cha chikondi chimenechi mwa kusamalira zinthu zauzimu zimene mabanja awo amafuna. Zimenezi ndi zinthu monga kuchita phunziro la Baibulo la banja mlungu uliwonse, kukambirana zinthu zauzimu mozama ngati n’kotheka, ndiponso kuthetsa mavuto akabuka.—Deut. 6:6, 7.
3 Mu Utumiki wa Kumunda: Anthu onse m’banja ayenera kudziŵa kuti kukhalira mboni Yehova ndi zolinga zake mwa kulalikira kwa ena ndi mbali yofunika kwambiri pa kulambira kwawo. (Yes. 43:10-12) Makolonu ngati mukufuna ana anu kukhala Mboni za Yehova zokhulupirika, yambirirani kukonzekeretsa mitima yawo kukonda utumiki. Kambiranani chifukwa chake kudzimana ndiponso kupita mu utumiki mlungu uliwonse kuli kofunika. (Mat. 22:37-39) Ndiyeno konzani zoti anawo azipita nanu nthaŵi zonse mu utumiki wa kumunda.
4 Kuti muthandize banja lanu kuzindikira kuti ntchito yolalikira n’njofunika kwambiri, muzipatula nthaŵi yochita phunziro la banja mlungu ndi mlungu kukonzekera ndi kuyeserera ulaliki wogwira mtima. Phunzitsani ana anu utumiki payekhapayekha, kuwathandiza kupita patsogolo malinga ndi msinkhu wawo ndi nzeru zawo. Mukachoka mu utumiki ndi ana anu, afunseni momwe aonera paokha kuti Yehova ndi wabwino. Simbani zinthu zimene akumana nazo zolimbitsa chikhulupiriro. Mabanja akamapitirizabe ‘kulaŵa kuti Ambuye ali wokoma mtima’ amayandikana kwambiri ndi Yehova, ndipo amawalimbitsa kukana “choipa chonse.”—1 Pet. 2:1-3.
5 Pamisonkhano: Zimakhala bwino zedi anthu pabanja akamalimbikitsana kupezeka pamisonkhano yonse ya mpingo, makamaka wina akatopa, akakhumudwa, kapena akakhala ndi mavuto osautsa. Mlongo wina mtsikana ananena kuti: “Bambo anga amabwera kuntchito, atatopa. Koma ndimawauza mfundo yabwino imene tikaphunzire kumsonkhano madzulo tsiku limenelo, ndipo zimawalimbikitsa kupitako. Inenso ndikatopa, amandilimbikitsa kuti ndipite.”—Aheb. 10:24, 25.
6 Kuchitira Zinthu Pamodzi: Mabanja azichitira zinthu pamodzi, monga kuthandizana ntchito za panyumba. Azikhalanso ndi nthaŵi yosangalala atasankha bwino zosangalatsazo. Kukacheza kumalo ena, kukawongola miyendo, kuchita maseŵero, ndi kuyendera achibale kapena anzawo kumapereka mpata wabwino wosangalala ndiponso azisangalala akamakumbukira zimenezi.—Mlal. 3:4.
7 Mabanja olimba achikristu tsiku lililonse amagonjetsa mavuto amene angasokoneze khalidwe lawo lauzimu. Pokhala ogwirizana kwambiri ndi Yehova, amapeza mphamvu imene iye amawapatsa.—Aef. 6:10.