Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/03 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira August 11
  • Mlungu Woyambira August 18
  • Mlungu Woyambira August 25
  • Mlungu Woyambira September 1
Utumiki Wathu wa Ufumu—2003
km 8/03 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Mlungu Woyambira August 11

Nyimbo Na. 101

Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu.

Mph. 17: “Tsanzirani Ubwino wa Yehova.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Pemphani omvera kufotokoza mwachidule zimene anakumana nazo zosonyeza mmene kuchitira ena zabwino kunawathandizira kuti alalikire. Yamikirani mpingowo chifukwa cha khama lawo pothandiza okhulupirira anzawo.

Mph. 20: “Madalitso a Utumiki wa Upainiya.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. Pemphani mpainiya m’modzi kapena aŵiri kuti afotokoze madalitso amene apeza chifukwa cha upainiya. Fotokozani kuti aliyense amene akufuna kuchita upainiya angapeze fomu yofunsira utumikiwu kwa mlembi.

Nyimbo Na. 11 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira August 18

Nyimbo Na. 82

Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Kambiranani nkhani yakuti “Pulogalamu Yatsopano ya Tsiku la Msonkhano Wapadera.” Lengezani tsiku la msonkhano wapadera ukubwerawo, ndipo limbikitsani onse kukapezekako. Ngati msonkhanowo udzachitika m’miyezi ingapo ikubwerayi, fotokozani kuti amene akufuna kubatizidwa adziŵitse woyang’anira wotsogolera.

Mph. 15: “Ntchito Imene Imatsitsimula.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Konzeranitu kuti anthu aŵiri kapena atatu adzafotokoze mmene utumiki wachikristu umawatsitsimulira.

Mph. 18: “Tiyeni Tizikonza Malo Athu Olambirirapo.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. (Ndime 1 mpaka 5) Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. Pokambirana ndime 3 ndi 4, fotokozani zimene mpingo wanu unakonza pankhani yoyeretsa Nyumba ya Ufumu. Tchulani ngati pali mbali zimene zikufunika kuzisamalira. Yamikirani mpingowo chifukwa cha khama lawo pokonza malowo kuti akhale oyenerera kulambira koona.

Nyimbo Na. 114 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira August 25

Nyimbo Na. 175

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Mwakugwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 8, khalani ndi zitsanzo ziŵiri zosonyeza mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya August 15 ndi Galamukani! ya August 8. M’zitsanzo ziŵiri zonsezo, agaŵire magazini onse aŵiri ngakhale kuti adzachitira chitsanzo magazini imodzi. Pa chitsanzo china mwa zitsanzo ziŵirizi, sonyezani mmene tingayankhire munthu amene akufuna kuti tisakambirane naye ponena kuti “Ndatanganidwa.”—Onani buku la Kukambitsirana, tsamba 19.

Mph. 15: Zosoŵa za pampingo.

Mph. 20: Limbani Mtima Kuti Mulalikire. (1 Ates. 2:2) Nkhani ndi kukambirana ndi omvera. Fotokozani chifukwa chake ambiri amachita mantha kuuza ena uthenga wa Ufumu. Zimenezi zimachitikiranso ngakhale anthu amene agwira ntchitoyi kwa zaka zambiri. Simbani zokumana nazo zimene zili m’makope a Nsanja ya Olonda a December 1, 1999, tsamba 25; December 15, 1999, tsamba 25; April 1, 1996, tsamba 31. Pemphani omverawo kufotokoza mmene iwo analimbira mtima kuti auze ena uthenga wabwino panthaŵi imene anali ndi mantha. Malizani mwa kuwalimbikitsa kupeza mphamvu kwa Yehova, ndipo teroni pogwiritsa ntchito mfundo za mu Nsanja ya Olonda ya December 15, 1999, masamba 23 mpaka 24.

Nyimbo Na. 125 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira September 1

Nyimbo Na. 84

Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti awo a mwezi wa August. Mwakugwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 8, khalani ndi zitsanzo ziŵiri zosonyeza mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya September 1 ndi Galamukani! ya August 8. M’zitsanzo ziŵiri zonsezo, agaŵire magazini onse aŵiri ngakhale kuti adzachitira chitsanzo magazini imodzi. M’zitsanzo zonsezo sonyezani kholo ndi mwana wake wamwamuna kapena wamkazi akuyeserera ulaliki pokonzekera kukagaŵira magazini. Abwereze mwachidule zimene akufuna kukanena asanachite chitsanzo.

Mph. 15: Kodi Mumasunga Lonjezo Lanu Loti Mudzabwererako? Nkhani ndi kukambirana ndi omvera pogwiritsa ntchito Nsanja ya Olonda ya September 15, 1999, masamba 10 mpaka 11, pa mutu wakuti “Njira Zina Zosungira Malonjezo Athu.” Tikapeza anthu mu utumiki wathu amene asonyeza chidwi, nthaŵi zambiri timakonza zoti tidzapitirize kukambirana nawo nthaŵi ina. Kodi timabwererako mokhulupirika monga mmene tinalonjezera? Pendani mfundo za m’Baibulo zimene ziyenera kutilimbikitsa kusunga malonjezo athu. Pemphani omvera kusimba zokumana nazo zimene zikusonyeza mmene anapindulira chifukwa chobwererako mwamsanga.

Mph. 20: “Tiyeni Tizikonza Malo Athu Olambirirapo.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. (Ndime 6 mpaka 12) Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. Gogomezerani kufunika kokonza bwinobwino Nyumba ya Ufumu, tsindikani zimene zili m’bokosi pa tsamba 5. Fotokozani mwachidule mmene Nyumba ya Ufumu yanu ilili, ndipo tchulani ngati pali zimene zakonzedwa pofuna kukonza moonongeka kapena pofuna kuti malowo azioneka bwinopo kuposa mmene alili.

Nyimbo Na. 41 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena