Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2004
Malangizo
Dongosolo lotsatirali ndilo lidzagwiritsidwe ntchito pochititsa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu mu 2004.
MABUKU OPHUNZIRA: Revised Nyanja (Union) Version [bi53-CN], Nsanja ya Olonda [w-CN], Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu [be-CN], Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako [gt-CN], ndi Kukambitsirana za m’Malemba [rs-CN].
Sukulu iyenera kuyamba PANTHAŴI YAKE ndi nyimbo, pemphero, ndi mawu amalonje, ndiyeno n’kupitirira motere:
LUSO LA KULANKHULA: Mphindi 5. Woyang’anira sukulu, mlangizi wothandiza, kapena mkulu wina woyenerera adzafotokoza luso la kulankhula kuchokera m’buku la Sukulu ya Utumiki. (Mipingo imene ili ndi akulu ochepa, ingagwiritse ntchito mtumiki wotumikira woyenerera.) Fotokozaninso zimene zili m’mabokosi amene ali m’nkhani imene yaperekedwayo ngati sitinanene kuti musafotokoze. Musaphatikizepo mbali ya zochita. Mbali imeneyi kwenikweni ndi yoti munthu aziigwiritsa ntchito payekha ndiponso popereka malangizo am’seri.
NKHANI NA. 1: Mphindi 10. Mkulu kapena mtumiki wotumikira ndi amene ayenera kukamba nkhani imeneyi, ndipo izitengedwa mu Nsanja ya Olonda, m’buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, kapena m’buku la Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako. Imeneyi ndi nkhani yolangiza imene ayenera kuikamba kwa mphindi khumi popanda mafunso obwereza. Cholinga chake chiyenera kukhala kufotokoza mfundo za m’nkhaniyo komanso kusonyeza phindu la mfundozo, ndi kutsindika mfundo zomwe zidzathandiza kwambiri mpingowo. Agwiritse ntchito mutu wosonyezedwa. Abale amene apatsidwa nkhani imeneyi azionetsetsa kuti akusunga nthaŵi. Malangizo am’seri angaperekedwe ngati pakufunika kutero.
MFUNDO ZAZIKULU ZA KUŴERENGA BAIBULO: Mphindi 10. Kwa mphindi sikisi zoyambirira, mkulu kapena mtumiki wotumikira woyenerera afotokoze mmene mfundozo zingathandizire pa zofunika za mpingowo. Angafotokoze mbali ina iliyonse ya chigawo cha kuŵerenga Baibulo cha mlunguwo. Isakhale chidule chabe cha gawo loŵerenga mlunguwo. Cholinga chachikulu ndicho kuthandiza omvera kuzindikira chifukwa chake komanso mmene mfundozo zilili zaphindu. Wokamba nkhaniyo ayenera kuonetsetsa kuti asapitirire mphindi zisanu ndi imodzi zoperekedwa pa mbali yoyambirira imeneyi. Agwiritse ntchito mphindi zinayi zomalizira kuti omvera alankhulepo. Apemphe omvera kulankhulapo mwachidule (kwa masekondi 30 kapena kucheperapo) pa mfundo za m’Baibulo zimene zinawasangalatsa poŵerenga ndiponso phindu lake. Ndiyeno woyang’anira sukulu apemphe ophunzira amene ali m’makalasi ena kupita ku makalasi awo.
NKHANI NA. 2: Mphindi 4. Iyi ndi nkhani yoti mbale aŵerenge. Nthaŵi zambiri aziŵerenga m’Baibulo. Koma kamodzi pamwezi, wopatsidwa nkhaniyi adzaŵerenga nkhani ya mu Nsanja ya Olonda. Wophunzira aŵerenge nkhani imene wapatsidwa popanda kukamba mawu oyamba kapena omaliza. Kutalika kwa nkhani yoŵerenga kuzisiyana pang’ono mlungu uliwonse koma ayenera kuŵerenga mphindi zinayi kapena kucheperapo. Woyang’anira sukulu aziona nkhaniyo asanagaŵire munthu, kuti pogaŵa aigwirizanitse ndi misinkhu ndiponso luso la ophunzira. Woyang’anira sukulu makamaka adzaonetsetsa kuti akuthandiza wophunzira kumvetsa zimene akuŵerengazo, kuŵerenga mosadodoma, kutsindika ganizo moyenera, kusinthasintha mawu, kupuma moyenera, ndiponso kuŵerenga mwachibadwa.
NKHANI NA. 3: Mphindi 5. Nkhani imeneyi azikamba ndi mlongo. Wophunzira amene wapatsidwa nkhani imeneyi azisankha yekha kapena azipatsidwa mtundu wa makambirano kuchokera pa mndandanda umene uli pa tsamba 82 m’buku la Sukulu ya Utumiki. Wophunzira agwiritse ntchito mutu wa nkhani umene wapatsidwa ndipo agwirizanitse ndi mbali ya utumiki wakumunda yomwe ndi yotheka ndiponso yothandiza m’gawo la mpingowo. Ngati sitinasonyeze buku limene nkhaniyo yachokera, wophunzira adzafunika kupeza mfundo za nkhani imeneyi mwa kufufuza m’zofalitsa za gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Ophunzira atsopano azipatsidwa nkhani zimene tasonyeza buku limene nkhaniyo yachokera. Woyang’anira sukulu adzaonetsetsa makamaka mmene wophunzira akufotokozera nkhaniyo ndiponso mmene akuthandizira mwininyumba kulingalira pa Malemba ndi kumvetsa mfundo zazikulu za nkhaniyo. Ophunzira amene angapatsidwe nkhani imeneyi ayenera kukhala odziŵa kuŵerenga. Woyang’anira sukulu adzasankha wothandiza mmodzi.
NKHANI NA. 4: Mphindi 5. Wophunzira akambe nkhani pa mutu umene wapatsidwa. Ngati sitinasonyeze buku limene nkhaniyo yachokera, wophunzira adzafunika kupeza mfundo za nkhaniyi mwa kufufuza m’zofalitsa za gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Akapatsidwa mbale, angaikambe monga nkhani ndipo akumbukire kuti omvera ake ndi anthu amene asonkhana m’Nyumba ya Ufumuyo. Mlongo akapatsidwa nkhani imeneyi, nthaŵi zonse aziikamba mofanana ndi Nkhani Na. 3. Woyang’anira sukulu angapereke nkhani Na. 4 kwa mbale nthaŵi ina iliyonse imene akuona kuti m’poyenera kupatsa mbale. Dziŵani kuti nkhani zimene zili ndi nyenyezi ziyenera kuperekedwa kwa abale basi kuti akambe ngati nkhani.
KUSUNGA NTHAŴI: Nkhani iliyonse isadye nthaŵi. Chimodzimodzinso ndi ndemanga za mlangizi. Nkhani Na. 2 mpaka Na. 4 ziziimitsidwa mwaluso nthaŵi yake ikatha. Ngati abale amene akamba nkhani yotsegulira ya luso la kulankhula, Nkhani Na. 1, kapena mfundo zazikulu za kuŵerenga Baibulo adya nthaŵi, azilangizidwa m’seri. Aliyense ayenera kusamala kwambiri nthaŵi. Pulogalamu yonse izitenga mphindi 45, osaphatikizapo nthaŵi ya nyimbo ndi pemphero.
MALANGIZO: Mphindi 1. Wophunzira aliyense akamaliza nkhani yake, woyang’anira sukulu adzanena mfundo zolimbikitsa za mbali ya nkhaniyo zimene wophunzirayo wachita bwino. Asapitirire mphindi imodzi pofotokoza zimenezi. Cholinga chake sindicho kungonena kuti “mwachita bwino” koma kutchula zifukwa zenizeni zimene mbali za nkhaniyo zimene watchulazo zinali zogwira mtima. Malinga ndi zimene wophunzira aliyense akufunikira, malangizo ena othandiza angaperekedwe m’seri misonkhano itatha kapena panthaŵi ina.
MLANGIZI WOTHANDIZA: Bungwe la akulu lingasankhe mkulu waluso, ngati alipo, kuphatikiza pa woyang’anira sukulu, kuti akhale mlangizi wothandiza. Ngati pali akulu angapo pa mpingo, ndiye kuti chaka chilichonse mkulu wina woyenerera angasamalire udindo umenewu. Ntchito yake idzakhala yopereka malangizo am’seri, ngati angafunike, kwa abale amene akamba Nkhani Na. 1 ndi mfundo zazikulu za Baibulo. N’kosafunika kuti azipereka malangizo kwa mkulu mnzake aliyense kapena mtumiki wotumikira aliyense akakamba nkhani zimenezi. Dongosolo limeneli lipitiriza kugwira ntchito mu 2004 ndipo mwina lingasinthidwe m’tsogolo.
FOMU YOLANGIZIRA: Ili m’buku momwemo.
KUBWEREZA KWA PAKAMWA: Mphindi 30. M’miyezi iŵiri iliyonse, woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza kwa pakamwa. Kudzatsatira pambuyo pa kukambirana luso la kulankhula ndi mfundo zazikulu za kuŵerenga Baibulo monga mmene tafotokozera kale. Kubwereza kwa pakamwaku kudzakhala kwa nkhani zimene zinakambidwa m’sukulu m’miyezi iŵiri yapita, kuphatikizapo mlungu wa kubwerezaku.
NDANDANDA4
Jan. 5 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 1-5 Nyimbo 154
Luso la Kulankhula: Kumveketsa Phindu la Nkhani Yanu (be-CN tsa. 157 ndime 1-5)
Na. 1: Kukonza Autilaini (be-CN tsa. 39-42)
Na. 2: Genesis 2:7-25
Na. 3: Kodi “Chipangano Chatsopano” Chimatchula za Paradaiso Wam’tsogolo wa Padziko Lapansi, Kapena Kodi Amatchulidwa mu “Chipangano Chakale” Chokha? (rs-CN tsa. 336 ndime 1-3)
Na. 4: aZimene Tingaphunzire pa Zitsanzo za m’Baibulo za Machimo Onyalanyaza Zinthu
Jan. 12 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 6-10 Nyimbo 215
Luso la Kulankhula: Kuonetsa Mmene Mfundo Zimagwirira Ntchito (be-CN tsa. 158 ndime 1-3)
Na. 1: Kodi Ukhondo Umatanthauza Chiyani Makamaka? (w02-CN 2/1 mas. 4-7)
Na. 2: Genesis 8:1-17
Na. 3: Chifukwa Chake Kunama Kuli Kulakwa
Na. 4: Chifukwa Chake “Paradaiso” Wotchulidwa pa Luka 23:43 Sangakhale Mbali Ina ya Hade Kapena ya Kumwamba (rs-CN tsa. 337 ndime 1-tsa. 338 ndime 1)
Jan. 19 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 11-16 Nyimbo 218
Luso la Kulankhula: Kuthandiza Ena Kuona Phindu la Nkhani Yanu (be-CN tsa. 159 ndime 1-4)
Na. 1: Mfundo za Chikhalidwe za Mulungu Zingakupindulitseni (w02-CN 2/15 mas. 4-7)
Na. 2: Genesis 13:1-18
Na. 3: Kodi N’chiyani Chimene Chimasonyeza Kuti Paradaiso Wotchulidwa pa Luka 23:43 Ndi Wapadziko Lapansi? (rs-CN tsa. 338 ndime 2-tsa. 339 ndime 2)
Na. 4: Chifukwa Chake Mboni za Yehova Sizitembenuza Anthu Malinga ndi Mmene Tanthauzo la Liwuli Lilili Masiku Ano
Jan. 26 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 17-20 Nyimbo 106
Luso la Kulankhula: Kusankha Bwino Mawu (be-CN tsa. 160 ndime 1-3)
Na. 1: Chisoni Chimalimbikitsa Munthu kukhala Wokoma Mtima ndi Wachifundo (w02-CN 4/15 mas. 24-7)
Na. 2: w02-CN 1/1 mas. 10-11 ndime 9-11
Na. 3: Zimene Mawu a Yesu Olembedwa pa Luka 13:24 Amatanthauza
Na. 4: Kodi Aliyense wa Ife Angapeze Motani Chidziŵitso Choona ndi Nzeru? (rs-CN tsa. 136 ndime 1-3)
Feb. 2 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 21-24 Nyimbo 64
Luso la Kulankhula: Kulankhula Kosavuta Kumva Bwino (be-CN tsa. 161 ndime 1-4)
Na. 1: Kukonzekera Nkhani ya Ophunzira mu Sukulu (be-CN tsa. 43 ndime 1-tsa. 44 ndime 3)
Na. 2: Genesis 21:1-21
Na. 3: Kodi Mafilosofi a Anthu Amachokera Kuti? (rs-CN tsa. 137 ndime 1-3)
Na. 4: bChifukwa Chake Pangano Lodzakwatirana Lifunika Kuonedwa Kukhala Lofunika Kwambiri
Feb. 9 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 25-28 Nyimbo 9
Luso la Kulankhula: Mawu Osiyanasiyana ndi Olondola (be-CN tsa. 161 ndime 5-tsa. 162 ndime 4)
Na. 1: Kukonzekera Nkhani Yokambirana (be-CN tsa. 44 ndime 4-tsa. 46 ndime 2)
Na. 2: Genesis 28:1-15
Na. 3: Mmene Tingakhalire Ndi Mtendere Wamumtima M’dziko la Mavutoli
Na. 4: Kodi N’chifukwa Ninji Kuphunzira Ziphunzitso za Yesu Kristu M’malo mwa Filosofi ya Anthu Uli Umboni Wakuti Munthuyo Amalingalira Bwino? (rs-CN tsa. 138 ndime 1–tsa. 139 ndime 1)
Feb. 16 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 29-31 Nyimbo 160
Luso la Kulankhula: Mawu Opereka Mphamvu, Okhudza Mtima, ndi Opereka Bwino Chithunzi (be-CN tsa. 163 ndime 1–tsa. 164 ndime 2)
Na. 1: Kuongoka Mtima Kumatsogolera Olungama (w02-CN 5/15 mas. 24-7)
Na. 2: w02-CN 2/1 mas. 15-16 ndime 6-10
Na. 3: Kodi ndi Mapemphero Ayani Amene Mulungu Ali Wofunitsitsa Kumva? (rs-CN tsa. 339 ndime 3-tsa. 340 ndime 6)
Na. 4: Chifukwa Chake Khalidwe Labwino Lili Lofunika kwa Akristu
Feb. 23 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 32-35 Nyimbo 1
Luso la Kulankhula: Kalankhulidwe Kotsatira Galamala (be-_CN tsa. 164 ndime 3–tsa. 165 ndime 1)
Kubwereza kwa Pakamwa
Mar. 1 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 36-39 Nyimbo 49
Luso la Kulankhula: Kugwiritsa Ntchito Autilaini (be-CN tsa. 166 ndime 1–tsa. 167 ndime 1)
Na. 1: Kukonzekera Nkhani Zokambira Mpingo (be-CN tsa. 47 ndime 1–tsa. 49 ndime 1)
Na. 2: Genesis 37:12-28
Na. 3: Chifukwa Chiyani Chikhulupiriro Chathu Chiyenera Kuyendera Limodzi ndi Chipiriro?
Na. 4: cKodi N’chiyani Chimene Chingapangitse Mapemphero a Munthu Kukhala Osavomerezeka Pamaso pa Mulungu? (rs-CN tsa. 340 ndime 7-tsa. 341 ndime 7)
Mar. 8 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 40-42 Nyimbo 205
Luso la Kulankhula: Kukonza Maganizo Anu (be-CN tsa. 167 ndime 2–tsa. 168 ndime 1)
Na. 1: Kukonzekera Mbali za Msonkhano wa Utumiki ndi Nkhani Zina (be-CN tsa. 49 ndime 2-tsa. 51 ndime 2)
Na. 2: Genesis 42:1-20
Na. 3: Mmene Tingakulitsire Unansi Wolimba ndi Yehova
Na. 4: dKodi ndi Nkhani Zoyenerera Zotani Zimene Tingapempherere? (rs-CN tsa. 341 ndime 8–tsa. 342 ndime 6)
Mar. 15 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 43-46 Nyimbo 67
Luso la Kulankhula: Lembani Autilaini Yosavuta (be-CN tsa. 168 ndime 2-tsa. 169 ndime 5)
Na. 1: Kodi Yehova Amalidalitsa Liti Khama la Munthu? (w02-CN 8/1 mas. 29-31)
Na. 2: Genesis 43:1-18
Na. 3: eNgati Wina Anena Kuti, ‘Yambani Mwapemphera Nane, Ndiyeno Ndilalikireni Uthenga Wanu’ (rs-CN tsa. 342 ndime 7-8)
Na. 4: Kodi Tingadzipezere Tokha Motani Mabwenzi Pogwiritsa Ntchito Chuma Chosalungama?
Mar. 22 Kuŵerenga Baibulo: Genesis 47-50 Nyimbo 187
Luso la Kulankhula: Kukamba Nkhani M’njira Yotsatirika (be-CN tsa. 170 ndime 1–tsa. 171 ndime 2)
Na. 1: N’chifukwa Chiyani Yehova Anavomereza Nsembe ya Abele Osati ya Kaini? (w02-CN 8/1 tsa. 28)
Na. 2: Genesis 47:1-17
Na. 3: Kodi ndi Maulosi Ena ati a Padera a Baibulo Amene Sanakwaniritsidwebe? (rs-CN tsa. 389 ndime 2–tsa. 390 ndime 2)
Na. 4: Chifukwa Chake Kuopa Yehova Ndicho Chiyambi cha Nzeru
Mar. 29 Kuŵerenga Baibulo: Eksodo 1- 6 Nyimbo 52
Luso la Kulankhula: Kufotokoza Mfundo mwa Ndondomeko Yotsatirika (be-CN tsa. 171 ndime 3–tsa. 172 ndime 6)
Na. 1: Kodi Luso la Kulingalira Lingakutetezeni Bwanji? (w02-CN 8/15 mas. 21-4)
Na. 2: w02-CN 2/15 mas. 19-20 ndime 7-11
Na. 3: Mmene Yehova Amaonera Kunyada
Na. 4: Kodi N’chifukwa Chiyani Akristu Ayenera Kukhala Okondweretsedwa Kwambiri ndi Maulosi a Baibulo? (rs-CN tsa. 390 ndime 3-7)
Apr. 5 Kuŵerenga Baibulo: Eksodo 7-10 Nyimbo 61
Luso la Kulankhula: Kugwiritsa Ntchito Mfundo Zoyenerera Zokha (be-CN tsa. 173ndime 1-4)
Na. 1: Kukonzekera Nkhani za Onse (be-CN tsa. 52 ndime 1-tsa. 54 ndime 1)
Na. 2: Eksodo 8:1-19
Na. 3: fNgati Wina Anena Kuti, ‘Mumagogomezera Kwambiri pa Ulosi’ (rs-CN tsa. 390 ndime 8-tsa. 391 ndime 1)
Na. 4: Chifukwa Chake Chiyembekezo Chili Ngati “Nangula wa Moyo”
Apr. 12 Kuŵerenga Baibulo: Eksodo 11-14 Nyimbo 87
Luso la Kulankhula: Kulankhula Kochokera mu Mtima (be-CN tsa. 174 ndime 1-tsa. 175 ndime 5)
Na. 1: Zimene Wokamba Nkhani Ayenera Kusankha (be-CN tsa. 54 ndime 2-4; tsa. 55, bokosi)
Na. 2: Eksodo 12:1-16
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Tifunika Kuvomereza Chilango cha Yehova?
Na. 4: Kodi Chiphunzitso cha Purigatoriyo Chazikidwa pa Chiyani? (rs-CN tsa. 343 ndime 1-tsa. 344 ndime 3)
Apr. 19 Kuŵerenga Baibulo: Eksodo 15-18 Nyimbo 171
Luso la Kulankhula: Kupeŵa Mbuna Mukamalankhula Kuchokera mu Mtima (be-CN tsa. 175 ndime 6–tsa. 177 ndime 2)
Na. 1: Kodi Mayesero Tiziwaona Bwanji? (w02-CN 9/1 mas. 29-31)
Na. 2: w02-CN 3/1 mas. 15-16 ndime 8-11
Na. 3: Kodi Munthu Akafa Amalandira Chilango Chowonjezereka pa Machimo Ake? (rs-CN tsa. 344 ndime 5-tsa. 345 ndime 1)
Na. 4: gChifukwa Chake Ukwati Uyenera Kukhala Mgwirizano wa Moyo Wonse
Apr. 26 Kuŵerenga Baibulo: Eksodo 19-22 Nyimbo 59
Luso la Kulankhula: Pamene Ena Afunsa Chifukwa pa Chikhulupiriro Chathu (be-CN tsa. 177 ndime 3–tsa. 178 ndime 3)
Kubwereza kwa Pakamwa
May 3 Kuŵerenga Baibulo: Eksodo 23-26 Nyimbo 13
Luso la Kulankhula: Kukamba Nkhani Mmene Mumalankhulira Ndi Anthu (be-CN mas. 179-80)
Na. 1: Kulitsani Luso la Kuphunzitsa (be-CN tsa. 56 ndime 1–tsa. 57 ndime 2)
Na. 2: Eksodo 23:1-17
Na. 3: Kodi Yehova Angathandize Munthu Motani Kuthetsa Zizoloŵezi Zake Zoipa?
Na. 4: Kodi Mafuko Osiyanasiyana Anachokera Kuti? (rs-CN tsa. 234 ndime 2-tsa. 235 ndime 1)
May 10 Kuŵerenga Baibulo: Eksodo 27-29 Nyimbo 28
Luso la Kulankhula: Kamvekedwe Kabwino ka Mawu (be-CN tsa. 181 ndime 1-4)
Na. 1: “Musiyanitse” (be-CN tsa. 57 ndime 3-tsa. 58 ndime 2)
Na. 2: Eksodo 28:29-43
Na. 3: Kodi Kaini Anapeza Kuti Mkazi Wake Ngati Panali Banja Limodzi Lokha? (rs-CN tsa. 235 ndime 2-4)
Na. 4: Chifukwa Chake Kusankhana Mitundu Kuli Kulakwa
May 17 Kuŵerenga Baibulo: Eksodo 30-33 Nyimbo 93
Luso la Kulankhula: Kapumidwe Koyenera (be-CN tsa. 181 ndime 5-tsa. 183 ndime 2; tsa. 182, bokosi)
Na. 1: Limbikitsani Omvera Anu Kulingalira (be-CN tsa. 58 ndime 3-tsa. 59 ndime 3)
Na. 2: Eksodo 30:1-21
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Tifunika Kukhala Ofatsa?
Na. 4: Kodi Kusiyana kwa Mikhalidwe ya Mafuko Kunabwera Bwanji? (rs-CN tsa. 235 ndime 5-tsa. 237 ndime 1)
May 24 Kuŵerenga Baibulo: Eksodo 34-37 Nyimbo 86
Luso la Kulankhula: Kumasula Minofu Yokungika (be-CN tsa. 184 ndime 1–tsa. 185 ndime 2; tsa. 184, bokosi)
Na. 1: Sonyezani Mmene Mfundozo Zimagwirira Ntchito Ndipo Khalani Chitsanzo Chabwino (be-CN tsa. 60 ndime 1-tsa. 61 ndime 3)
Na. 2: Eksodo 36:1-18
Na. 3: Kodi Anthu Onse Ali Ana a Mulungu? (rs-CN tsa. 237 ndime 2-6)
Na. 4: Kodi N’chifukwa Chiyani Tifunika Kukhala Okhulupirika M’zinthu Zazing’ono?
May 31 Kuŵerenga Baibulo: Eksodo 38-40 Nyimbo 202
Luso la Kulankhula: Kusonyeza Chidwi mwa Munthu Winayo (be-CN tsa. 186 ndime 1-4)
Na. 1: Mmene Mungakulitsire Luso la Kucheza ndi Anthu (be-CN tsa. 62 ndime 1–tsa. 64 ndime 1)
Na. 2: w02-CN 5/1 mas. 19-20 ndime 3-6
Na. 3: Kodi Kumvetsa Bwino 1 Yohane 3:19, 20 Kungamutonthoze Motani Munthu?
Na. 4: Kodi Anthu a Mafuko Onse Adzagwirizanadi Monga Abale ndi Alongo? (rs-CN tsa. 238 ndime 1-tsa. 239 ndime 1)
June 7 Kuŵerenga Baibulo: Levitiko 1-5 Nyimbo 123
Luso la Kulankhula: Kumvetsera Mosamala (be-CN tsa. 186 ndime 5-tsa. 187 ndime 4)
Na. 1: Mmene Mungapitirizire Kucheza Kwanu (be-CN tsa. 64 ndime 2-tsa. 65 ndime 4)
Na. 2: Levitiko 3:1-17
Na. 3: Kodi ndi Motani Mmene Imfa ya Yesu Kristu Inalili Yosiyana ndi ya Ena Amene Akhala Ophedwera Chikhulupiriro? (rs-CN tsa. 122 ndime 1-4)
Na. 4: Kodi Cholakwika ndi Chiyani Kuchitako Chidwi Pang’ono Ndi Zamatsenga?
June 14 Kuŵerenga Baibulo: Levitiko 6-9 Nyimbo 121
Luso la Kulankhula: Kuthandiza Ena Kupita Patsogolo (be-CN tsa. 187 ndime 5–tsa. 188 ndime 3)
Na. 1: Kuzindikira Maganizo a Wofunsayo (be-CN tsa. 66 ndime 1-tsa. 68 ndime 1)
Na. 2: Levitiko 7:1-19
Na. 3: Kodi Tingaphunzire Bwanji Kudana ndi Choipa?
Na. 4: Kodi N’chifukwa Chiyani Kunali Kofunika kuti Dipo Liperekedwe mwa Njira Imene Linaperekedwera? (rs-CN tsa. 122 ndime 6-tsa. 123 ndime 1)
June 21 Kuŵerenga Baibulo: Levitiko 10-13 Nyimbo 183
Luso la Kulankhula: Thandizani pa Zosoŵa Zawo (be-CN tsa. 188 ndime 4–tsa. 189 ndime 4)
Na. 1: Dziŵani Mayankhidwe Oyenera (be-CN tsa. 68 ndime 2-tsa. 70 ndime 3)
Na. 2: Levitiko 11:1-25
Na. 3: Kodi N’chifukwa Chiyani Mulungu Sanangolamula Kuti Onse Amene Akamvera Akakhala ndi Moyo Kosatha? (rs-CN tsa. 123 ndime 2–tsa. 124 ndime 1)
Na. 4: Mmene Yehova Amaonera Zachinyengo
June 28 Kuŵerenga Baibulo: Levitiko 14-16 Nyimbo 216
Luso la Kulankhula: Kulemekeza Ena (be-CN tsa. 190 ndime 1-tsa. 191 ndime 1 )
Kubwereza kwa Pakamwa
July 5 Kuŵerenga Baibulo: Levitiko 17-20 Nyimbo 54
Luso la Kulankhula: Ulemu Pokumana ndi Munthu (be-CN tsa. 191 ndime 2–tsa. 192 ndime 1)
Na. 1: Kukambirana M’makalata (be-CN tsa. 71-3)
Na. 2: Levitiko 17:1-16
Na. 3: Dalirani Gulu la Yehova
Na. 4: Kodi Mtengo wa Nsembe ya Yesu Unagwira Ntchito Choyamba pa Ndani, Ndipo N’cholinga Chotani? (rs-CN tsa. 124 ndime 2-3)
July 12 Kuŵerenga Baibulo: Levitiko 21-24 Nyimbo 138
Luso la Kulankhula: Kulankhula Mwaulemu (be-CN tsa. 192 ndime 2-tsa. 193 ndime 2)
Na. 1: Khalani Womapitabe Patsogolo (be-CN tsa. 74 ndime 1-tsa. 75 ndime 3)
Na. 2: Levitiko 22:1-16
Na. 3: Kodi Ndani Amenenso Akupindula M’tsiku Lathu ndi Nsembe ya Yesu? (rs-CN tsa. 125 ndime 1-3)
Na. 4: Kodi Yehova Anali Mulungu Wafuko la Ayuda?
July 19 Kuŵerenga Baibulo: Levitiko 25-27 Nyimbo 7
Luso la Kulankhula: Kulankhula Motsimikiza (be-CN tsa. 194 ndime 1-tsa. 195 ndime 2)
Na. 1: Gwiritsani Ntchito Mphatso Yanu (be-CN tsa. 75 ndime 4-tsa. 77 ndime 2)
Na. 2: Levitiko 25:1-19
Na. 3: Mmene Uchigaŵenga Udzathere
Na. 4: Kodi Kudzakhala Kusangalala ndi Madalitso a M’tsogolo Otani Chifukwa cha Dipo? (rs-CN tsa. 126 ndime 1-4)
July 26 Kuŵerenga Baibulo: Numeri 1-3 Nyimbo 30
Luso la Kulankhula: Mmene Mungalankhulire Motsimikiza (be-CN tsa. 195 ndime 3–tsa. 196 ndime 4)
Na. 1: Kodi Akristu Ayenera Kukhala Ansanje? (w02-CN 10/15 mas. 28-31)
Na. 2: w02-CN 6/15 mas. 18-19 ndime 6-9
Na. 3: Kodi Timafunika Kuchitanji Kuti Tipindule ndi Nsembe ya Yesu? (rs-CN tsa. 126 ndime 5–tsa. 127 ndime 3)
Na. 4: Kodi N’kulakwa Kulira pa Maliro a Munthu Amene Timakonda?
Aug. 2 Kuŵerenga Baibulo: Numeri 4-6 Nyimbo 128
Luso la Kulankhula: Khalani Wosamala Komanso Wolimba (be-CN tsa. 197 ndime 1-3)
Na. 1: Mmene Tingachitire Kuti Masiku a Moyo Wathu Asangalatse Yehova (w02-CN 11/15 mas. 20-3)
Na. 2: Numeri 6:1-17
Na. 3: Kodi Baibulo Lingathandize Motani Anthu Kuti Asiye Kudana?
Na. 4: Kodi Dipo Liyenera Kukhudza Motani Mmene Timagwiritsira Ntchito Miyoyo Yathu? (rs-CN tsa. 127 ndime 4-6)
Aug. 9 Kuŵerenga Baibulo: Numeri 7-9 Nyimbo 35
Luso la Kulankhula: Kusamala Polalikira (be-CN tsa. 197 ndime 4-tsa. 198 ndime 5)
Na. 1: Kodi N’zothekadi Kuti Anthu Azikhala Mofanana? (w02-CN 1/1 mas. 4-7)
Na. 2: Numeri 8:1-19
Na. 3: Pamene Mtumwi Paulo Ananena Kuti Akristu ‘Akakwatulidwa’ Kukakhala ndi Ambuye, Kodi Anali Kulankhula Nkhani Yanji? (rs-CN tsa. 213 ndime 1-2)
Na. 4: Kodi Wokana Kristu Ndi Ndani?
Aug. 16 Kuŵerenga Baibulo: Numeri 10-13 Nyimbo 203
Luso la Kulankhula: Mawu Oyenerera a Panthaŵi Yake (be-CN tsa. 199 ndime 1-4)
Na. 1: Khulupirirani Yehova—Mulungu Weniweni (w02-CN 1/15 mas. 5-7)
Na. 2: Numeri 12:1-16
Na. 3: Kodi Kubwezera Chilango kwa Mulungu N’kogwirizana ndi Chikondi Chake?
Na. 4: Kodi Kristu Adzaoneka ndi Maso Pamtambo Ndiyeno N’kukwatula Akristu Okhulupirika Kuloŵa Nawo Kumwamba Pamene Dziko Lonse Likupenyerera? (rs-CN tsa. 213 mutu womalizira-tsa. 214 ndime 3)
Aug. 23 Kuŵerenga Baibulo: Numeri 14-16 Nyimbo 207
Luso la Kulankhula: Khalani Wosamala M’kalankhulidwe ndi a Pabanja Ndiponso Anthu Ena (be-CN tsa. 200 ndime 1-4)
Na. 1: Anthu Aŵiri a Pachibale Amene Anali ndi Mitima Yosiyana (w02-CN 1/15 mas. 21-3)
Na. 2: w02-CN 7/15 mas. 23-4 ndime 15-19
Na. 3: Kodi N’kotheka Kuti Akristu Atengedwe Kumwamba ndi Matupi Awo Enieni? (rs-CN tsa. 214 ndime 4-tsa. 215 ndime 1)
Na. 4: hChifukwa Chake Akristu Sayenera Kuchita Maseŵera Achiwawa Apavidiyo
Aug. 30 Kuŵerenga Baibulo: Numeri 17-21 Nyimbo 150
Luso la Kulankhula: Khalani Wolimbikitsa (be-CN tsa. 202 ndime 1–tsa. 203 ndime 2)
Kubwereza kwa Pakamwa
Sept. 6 Kuŵerenga Baibulo: Numeri 22-25 Nyimbo 22
Luso la Kulankhula: Mawu Anu Azimveka Olimbikitsa (be-CN tsa. 203 ndime 3−tsa. 204 ndime 1)
Na. 1: N’chifukwa Chiyani Dziko Lakale Limenelo Linawonongedwa? (w02-CN 3/1 mas. 5-7)
Na. 2: Numeri 22:1-19
Na. 3: Kodi Akristu Okhulupirika Adzatengedwa Kumka Kumwamba Mobisa Popanda Kufa? (rs-CN tsa. 215 ndime 2-tsa. 216 ndime 1)
Na. 4: iChifukwa Chake Makolo Achikristu Afunika Kuŵerengera Mabuku Ana Awo
Sept. 13 Kuŵerenga Baibulo: Numeri 26-29 Nyimbo 71
Luso la Kulankhula: Pocheza ndi Okhulupirira Anzathu (be-CN tsa. 204 ndime 2-tsa. 205 ndime 4)
Na. 1: Mmene Kulumala Konse Kudzathere (w02-CN 5/1 mas. 4-7)
Na. 2: Numeri 29:1-19
Na. 3: Kodi N’chitetezo Chotani Chimene Chidzakhalapo kwa Akristu Oona M’kati mwa Chisautso Chachikulu? (rs-CN tsa. 216 ndime 2-6)
Na. 4: Kodi Malonjezano a Mulungu Akhala Bwanji Odalirika mwa Yesu Kristu?
Sept. 20 Kuŵerenga Baibulo: Numeri 30-32 Nyimbo 51
Luso la Kulankhula: Kubwereza Komveketsa Mfundo (be-CN tsa. 206 ndime 1-4)
Na. 1: Bzalani Chilungamo, Kololani Kukoma Mtima kwa Mulungu (w02-CN 7/15 mas. 28-31)
Na. 2: Numeri 30:1-16
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Akristu Ena Amatengeredwa Kumwamba Kukakhala Ndi Kristu? (rs-CN tsa. 217 ndime 1-4)
Na. 4: jChifukwa Chake Tifunika Kupeŵa Zithunzi Zolaula
Sept. 27 Kuŵerenga Baibulo: Numeri 33-36 Nyimbo 100
Luso la Kulankhula: Kubwereza Mfundo mu Utumiki wa Kumunda ndi Pokamba Nkhani (be-CN tsa. 207 ndime 1–tsa. 208 ndime 4)
Na. 1: Kodi Anthu Oyera Mtima Enieni Angakuthandizeni Bwanji? (w02-CN 9/15 mas. 4-7)
Na. 2: w02-CN 8/1 mas. 18-19 ndime 15-19
Na. 3: k‘Kodi Mumakhulupirira mu Kutengedwa M’thupi?’ (rs-CN tsa. 217 ndime 5-tsa. 218 ndime 1)
Na. 4: Chifukwa Chake Tifunika Kupeŵa Zinthu Zonyamula Mtima
Oct. 4 Kuŵerenga Baibulo: Deuteronomo 1-3 Nyimbo 191
Luso la Kulankhula: Kutambasula Mutu wa Nkhani (be-CN tsa. 209 ndime 1-3)
Na. 1: Kudziŵa Zolondola Zokhudza Mulungu Kumatilimbikitsa (w02-CN 10/1 mas. 5-7)
Na. 2: Deuteronomo 1:1-18
Na. 3: Zomwe Kupanga Choonadi Kukhala Chanuchanu Kumatanthauza
Na. 4: Munthu Akamaona ngati Kuti ndi Wozoloŵerana Kale ndi Mabwenzi Ndiponso Malo Atsopano Kotheratu, Kodi Ndiye Kuti Zimenezi Zimatsimikizira Kuti Kudziveka Thupi la Nyama Kumachitikadi? (rs-CN tsa. 174 ndime 3-tsa. 176 ndime 1)
Oct. 11 Kuŵerenga Baibulo: Deuteronomo 4-6 Nyimbo 181
Luso la Kulankhula: Kusankha Mutu Woyenera (be-CN tsa. 210 ndime 1–tsa. 211 ndime 1; tsa. 211, bokosi)
Na. 1: Anakhudza Chovala Chake (gt-CN mutu 46)
Na. 2: Deuteronomo 4:1-14
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Mawu Olembedwa pa Yohane 9:1, 2 Sasonyeza Kudziveka ndi Thupi la Nyama? (rs-CN tsa. 176 ndime 2-tsa. 177 ndime 3)
Na. 4: Kodi “Chisamaliro cha Mzimu” Chimaphatikizapo Chiyani?
Oct. 18 Kuŵerenga Baibulo: Deuteronomo 7-10 Nyimbo 78
Luso la Kulankhula: Kuunika Mfundo Zazikulu (be-CN tsa. 212 ndime 1–tsa. 213 ndime 2)
Na. 1: Misozi Isanduka Chikondwerero Chachikulu (gt-CN mutu 47)
Na. 2: w02-CN 8/15 mas. 15-16 ndime 3-6
Na. 3: Kodi Pali Kusiyana Kwakukulu Kotani Kumene Kulipo Pakati pa Kudziveka Thupi la Nyama ndi Chiyembekezo Choperekedwa m’Baibulo? (rs-CN tsa. 177 ndime 4-tsa. 178 ndime 1)
Na. 4: lMmene Yehova Amaonera Ampatuko
Oct. 25 Kuŵerenga Baibulo: Deuteronomo 11-13 Nyimbo 57
Luso la Kulankhula: Musachulukitse Mfundo Zazikulu (be-CN tsa. 213 ndime 3-tsa. 214 ndime 5)
Kubwereza kwa Pakamwa
Nov. 1 Kuŵerenga Baibulo: Deuteronomo 14-18 Nyimbo 26
Luso la Kulankhula: Mawu Oyamba Okopa Chidwi (be-CN tsa. 215 ndime 1–tsa. 216 ndime 4)
Na. 1: Yesu Anakanidwa Ngakhale Anachita Zozizwitsa (gt-CN mutu 48)
Na. 2: Deuteronomo 14:1-23
Na. 3: aNgati Wina Anena Kuti, ‘Ndimakhulupirira mu Kudziveka Thupi la Nyama’ (rs-CN tsa. 178 ndime 2-4)
Na. 4: Chifukwa Chake Akristu Afunika Kukhala ndi Moyo Wosalira Zambiri
Nov. 8 Kuŵerenga Baibulo: Deuteronomo 19-22 Nyimbo 182
Luso la Kulankhula: Kukopa Chidwi cha Anthu mu Utumiki Wakumunda (be-CN tsa. 216 ndime 5-tsa. 217 ndime 3 )
Na. 1: Ulendo Wachitatu Wokalalikira ku Galileya (gt-CN mutu 49)
Na. 2: Deuteronomo 21:1-17
Na. 3: Kodi N’chifukwa Ninji Pali Zipembedzo Zambiri? (rs-CN tsa. 83 ndime 1–tsa. 84 ndime 2)
Na. 4: Kodi Zitsanzo za m’Baibulo Zingatithandize Motani Kuti Tilimbane ndi Zofooketsa?
Nov. 15 Kuŵerenga Baibulo: Deuteronomo 23-27 Nyimbo 162
Luso la Kulankhula: Kutchula Nkhani Yanu M’mawu Oyamba (be-CN mas. 217 ndime 4-tsa. 219 ndime 1)
Na. 1: Kukonzekeretsa Atumwi Ake Kukumana ndi Chizunzo (gt-CN mutu 50)
Na. 2: Deuteronomo 24:1-16
Na. 3: Mmene Tingadziŵire Anthu Ochirikizidwa ndi Mulungu
Na. 4: Kodi N’zoona Kuti M’zipembedzo Zonse Muli Abwino? (rs-CN tsa. 84 ndime 3-tsa. 85 ndime 1)
Nov. 22 Kuŵerenga Baibulo: Deuteronomo 28-31 Nyimbo 32
Luso la Kulankhula: Mawu Omaliza Ogwira Mtima (be-CN tsa. 220 ndime 1-3)
Na. 1: Kupha Mwambanda pa Phwando la Tsiku Lakubadwa (gt-CN mutu 51)
Na. 2: Deuteronomo 29:1-18
Na. 3: Kodi Kuli Koyenera Kusiya Chipembedzo cha Makolo a Munthuwe? (rs-CN tsa. 85 ndime 2-4)
Na. 4: Chifukwa Chake Akristu Afunika Kukhala Odzichepetsa
Nov. 29 Kuŵerenga Baibulo: Deuteronomo 32-34 Nyimbo 41
Luso la Kulankhula: Mfundo Zofunika Kuzikumbukira (be-CN tsa. 221 ndime 1-5)
Na. 1: Yesu Adyetsa Zikwi Zambiri Mozizwitsa (gt-CN mutu 52)
Na. 2: w02-CN 10/15 tsa. 11 ndime 10-13
Na. 3: Njira Zimene Tingayeretsere Dzina la Mulungu
Na. 4: Kodi N’chiyani Chili Lingaliro la Baibulo Ponena za Chikhulupiriro Choloŵana? (rs-CN tsa. 86 ndime 1-tsa. 87 ndime 1)
Dec. 6 Kuŵerenga Baibulo: Yoswa 1-5 Nyimbo 40
Luso la Kulankhula: Mu Utumiki wa Kumunda (be-CN tsa. 221 ndime 6-tsa. 222 ndime 6)
Na. 1: Pamene Yesu Anayenda Pamadzi (gt-CN mutu 53)
Na. 2: Yoswa 4:1-14
Na. 3: Kodi Kukhala Mbali ya Chipembedzo Cholinganizidwa N’kofunika? (rs-CN tsa. 87 ndime 2-tsa. 88 ndime 1)
Na. 4: Kodi Khirisimasi ndi Chikondwerero cha Akristu?
Dec. 13 Kuŵerenga Baibulo: Yoswa 6-8 Nyimbo 213
Luso la Kulankhula: Kunena Zoona Zokhazokha (be-CN tsa. 223 ndime 1-5)
Na. 1: Kupepesa—Njira Yothandiza Yopezera Mtendere (w02-CN 11/1 mas. 4-7)
Na. 2: Yoswa 6:10-23
Na. 3: Kodi N’chifukwa Chiyani Tifunika Kupitiriza Kulalikira Kunyumba ndi Nyumba?
Na. 4: Kodi Kukonda Munthu Mnzanu Kulidi N’kanthu? (rs-CN tsa. 88 ndime 3)
Dec. 20 Kuŵerenga Baibulo: Yoswa 9-11 Nyimbo 135
Luso la Kulankhula: ‘Kugwiritsa Mawu Okhulupirika’ (be-CN tsa. 224 ndime 1-4)
Na. 1: Limbitsani Manja Anu (w02-CN 12/1 mas. 30-1)
Na. 2: w02-CN 11/15 mas. 18-19 ndime 19-23
Na. 3: Kodi Kukhala ndi Unansi Wathu ndi Mulungu Kulidi Chinthu Chofunika? (rs-CN tsa. 88 ndime 4-5)
Na. 4: bZomwe Kukhala a Mtendere Kumatanthauza
Dec. 27 Kuŵerenga Baibulo: Yoswa 12-15 Nyimbo 210
Luso la Kulankhula: Tsimikizani Zochokera ku Magwero Ena Kuti N’zolondola (be-CN tsa. 225 ndime 1-3)
Kubwereza kwa Pakamwa
[Mawu a M’munsi]
a Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
b Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
c Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
d Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
e Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha.
f Ngati nthaŵi ilola, sonyezani mmene mungayankhire zimene anthu amanena, kutsutsa, ndi zina zotero zimene zingagwirizane bwino ndi zofunika za m’gawo lanu.
g Ngati nthaŵi ilola, sonyezani mmene mungayankhire zimene anthu amanena, kutsutsa, ndi zina zotero zimene zingagwirizane bwino ndi zofunika za m’gawo lanu.
h Ngati nthaŵi ilola, sonyezani mmene mungayankhire zimene anthu amanena, kutsutsa, ndi zina zotero zimene zingagwirizane bwino ndi zofunika za m’gawo lanu.
i Ngati nthaŵi ilola, sonyezani mmene mungayankhire zimene anthu amanena, kutsutsa, ndi zina zotero zimene zingagwirizane bwino ndi zofunika za m’gawo lanu.
j Ngati nthaŵi ilola, sonyezani mmene mungayankhire zimene anthu amanena, kutsutsa, ndi zina zotero zimene zingagwirizane bwino ndi zofunika za m’gawo lanu.
k Ngati nthaŵi ilola, sonyezani mmene mungayankhire zimene anthu amanena, kutsutsa, ndi zina zotero zimene zingagwirizane bwino ndi zofunika za m’gawo lanu.
l Ngati nthaŵi ilola, sonyezani mmene mungayankhire zimene anthu amanena, kutsutsa, ndi zina zotero zimene zingagwirizane bwino ndi zofunika za m’gawo lanu.
a Ngati nthaŵi ilola, sonyezani mmene mungayankhire zimene anthu amanena, kutsutsa, ndi zina zotero zimene zingagwirizane bwino ndi zofunika za m’gawo lanu.
b Ngati nthaŵi ilola, sonyezani mmene mungayankhire zimene anthu amanena, kutsutsa, ndi zina zotero zimene zingagwirizane bwino ndi zofunika za m’gawo lanu.