Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira March 14
Mph. 7: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili patsamba 8 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu) kusonyeza chitsanzo cha mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya March 15 ndi Galamukani! ya April 8. Mungathe kugwiritsanso ntchito maulaliki ena amene angakhale othandiza. M’chitsanzo chimodzi, asonyeze akuchita ulendo wobwereza kwa amene amakam’patsira magazini. Kumapeto kwa chitsanzocho, agwiritse ntchito tsamba lomaliza la Nsanja ya Olonda ya March 15 kukumbutsa mwininyumba za mwambo wa Chikumbutso umene ukubwera. (Ngati magazini amenewa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 18: “Kugogomezera Kwambiri Baibulo!” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
Mph. 20: Kulitsani Chidwi mwa Kugwiritsa Ntchito Bulosha Latsopano. Nkhani ndi kukambirana ndi omvera. Ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Tiyenera kubwerera kwa munthu aliyense amene analandira bulosha la Dikirani! kuti tikakulitse chidwi chake. Mwa kugwiritsa ntchito tsamba 2 la za m’kati mwake, fotokozani mwachidule za buloshalo, kutsindika makamaka zigawo zachidule za maonekedwe osiyanasiyana (zimene ndime zake n’zazilembo za masiku onse koma mitu yake n’njazilembo zakuda kwambiri). Mbali zimenezi zingagwiritsidwe ntchito pokambirana mwachidule pa maulendo obwereza. Mwachitsanzo, ngati ulendo woyamba munakambirana masamba 3 mpaka 4, pa ulendo wobwereza mungagwiritse ntchito mbali yakuti “Kodi Mulungu Amatiganiziradi?” imene ili patsamba 5. Fotokozani mmene tingachitire zimenezo. Pendani zigawo zinanso, monga zimene zili pamasamba 6 mpaka 8 ndi 17 mpaka 18 kapena zina zothandiza m’gawo lanu. Chitani chitsanzo cha ulendo wobwereza mwa kugwiritsa ntchito chimodzi mwa zigawo za maonekedwe osiyanasiyana. Awerenge ndi kukambirana lemba kapena malemba angapo osagwidwa mawu. Pomaliza, wofalitsa asonyeze mwininyumba chigawo china chimene angadzakambirane ulendo wotsatira.
Nyimbo Na. 137 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 21
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Ndiponso fotokozani masiku ndi malo a Msonkhano Wachigawo wa 2005 wakuti “Kumvera Mulungu” umene mudzapitako.
Mph. 15: “Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo—Gawo 6.” Phatikizanipo chitsanzo cha mphindi zinayi. Wophunzira Baibulo afunse chifukwa chake anthu owerengeka chabe mwa opezeka pa Chikumbutso ndiwo amadya mkate ndi kumwa vinyo. Wophunzitsayo ayamikire munthuyo chifukwa cha funso lake, alilembe, ndipo apemphe ngati angakambirane funsolo atamaliza phunziro la mlunguwo. Atamaliza phunziro, wofalitsa asonyeza wophunzira mfundo zimene zili pamutu wakuti “Kodi ndani amene ayenera kudya mkate ndi vinyo”? pamasamba 72 mpaka 73 m’buku la Kukambitsirana. Awerengere limodzi, ndipo wophunzirayo ayamikire yankho lomveka la funso lake.
Mph. 20: “Gawirani Magazini mu Utumiki Wanu.” Pokambirana ndime 3 ndi 4, sonyezani mmene mfundozo zingagwirire ntchito kwanuko. Mwachidule funsani wofalitsa mmodzi kapena awiri amene amatha kugawira magazini kumalo a malonda, m’misewu, malo opezekako anthu ambiri, kapena polalikira mwamwayi. Apempheni afotokoze mmene amagawira magazini kumalo amenewo. Chitani chitsanzo chachidule cha ulalikiwo kapena cha zimene zinachitikazo.
Nyimbo Na. 109 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira March 28
Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi kuyamikira zopereka. Limbikitsani onse kuitanira anthu achidwi ku nkhani yapadera ya onse ya pa April 10. Tchulani mabuku ogawira mu April ndi May. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 8 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu), sonyezani chitsanzo cha mmene tingagawire Nsanja ya Olonda ya April 1 ndi Galamukani! ya April 8. Mungathe kugwiritsanso ntchito maulaliki ena amene angakhale othandiza. M’chitsanzo chilichonse fotokozani kumene kumachokera thandizo la ndalama zoyendetsera ntchito yathu ya padziko lonse imeneyi.—Onani mu Nsanja ya Olonda, patsamba 2, kapena mu Galamukani, patsamba 5. (Ngati magazini amenewa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 15: Zosowa za pampingo.
Mph. 18: “Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira.” Nkhani ndi kukambirana ndi omvera.
Nyimbo Na. 116 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira April 4
Mph. 5: Zilengezo za pampingo.
Mph. 15: Kondanani Wina ndi Mnzake. (Yoh. 13:35) Nkhani yokambidwa ndi mkulu kuchokera mu Nsanja ya Olonda ya February 1, 2003, masamba 15 mpaka 18, ndime 10 mpaka 21. Malinga ndi zimene zanenedwa pa mabuku ogawira mu April ndi May, tikulimbikitsidwa kuyambitsa maphunziro a Baibulo ndi anthu amene anaphunzira kale buku la Chidziŵitso ndi bulosha la Mulungu Amafunanji. Fotokozani momveka bwino mmene ofalitsa angachitire zinthu mogwirizana ndi akulu kuthandiza amene ali ofooka.
Mph. 25: “Kodi Pangakhale Vuto Lililonse ndi Kuchita za Matsenga ndi Ufiti?—Gawo 2.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Malemba otsindika mfundo afunika kuwawerenga ndi kuthirirapo ndemanga.
Nyimbo Na. 36 ndi pemphero lomaliza.