Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
Mlungu Woyambira December 12
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Gwiritsani ntchito mfundo zimene zili pa tsamba 8 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu) kusonyeza chitsanzo cha mmene tingagawire Galamukani! ya December 8 ndi Nsanja ya Olonda ya December 15. Mungathenso kugwiritsa ntchito zitsanzo zina zoyenerana ndi kwanuko. Pamapeto pa chitsanzo chilichonse, fotokozani mmene malemba angagwiritsidwire ntchito mosavuta pa ulaliki umene munthu angapereke. (Ngati magazini amenewa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)
Mph. 15: “Sukulu Imene Imatithandiza Kugwiritsa Ntchito Zomwe Taphunzira.” Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira sukulu. Fotokozaninso ndemanga za m’mphatika ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 2005.
Mph. 20: “Maphunziro Opatsa Moyo.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Konzani pasadakhale kuti munthu mmodzi kapena awiri adzafotokoze mmene apindulira ndi maphunziro a Mulungu kudzera m’gulu lake.
Nyimbo Na. 101 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 19
Mph. 5: Zilengezo za pampingo. Fotokozani za dongosolo lapadera la utumiki wa kumunda pa December 25 ndi pa January 1.
Mph. 40: “Kumvera Lamulo la Mulungu Losala Magazi.” Nkhani yokambidwa ndi mlembi. Nkhaniyi iwerengedwe mmene ilili. Ofalitsa onse apatsidwe makadi atsopano a DPA musanayambe kuwerenga ndime. Wofalitsa aliyense atalandira khadi lake la DPA, akhoza kuyendera limodzi ndi mlembi pamene akuwerenga ndime iliyonse, ndi malemba onse, ngakhalenso amene ali kumapeto kwa nkhaniyo. Pa mbali yakuti “Nkhani Zofunsidwa Kawirikawiri,” mlembi akonze zoti mbale wina amene amawerenga bwino, awerenge mafunso ndipo mlembi awerenge mayankho akewo. Msonkhano utatha, makolo obatizidwa apatsidwe Khadi la Mwana wawo wamng’ono aliyense wosabatizidwa. Ofalitsa osabatizidwa atha kudzilembera malangizo potengera mawu a pa khadi la DPA. Angalemberenso ana awo malangizo potengera mawu a pa Khadi la Mwana. Onse aonetsetse kuti asunga mphatika ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi uno kuti adzagwiritse ntchito m’tsogolo ndi kuthandiziranso amene angadzabatizidwe.
Nyimbo Na. 56 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira December 26
Mph. 10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pa masitetimenti. Kumbutsani ofalitsa kupereka malipoti a utumiki wa kumunda a mwezi wa December. Ngati mpingo wanu udzasintha nthawi zoyambira misonkhano poyamba chaka chatsopano, lengezani nthawi yatsopanoyo. Tchulani za mabuku odzagawira mwezi wa January, ndipo nenani za kumene angakapeze zitsanzo za maulaliki ake.
Mph. 15: “Sonyezani Ena Chidwi mwa Kukhala Wokhoza Kusintha.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Phatikizanipo chitsanzo chachidule chosonyeza mmene wofalitsa angasinthire ulaliki wake kuti ugwirizane ndi zimene mwini nyumba anganene.
Mph. 20: Kukonzekera Misonkhano pa Banja. Atate akambirane ndi banja lawo momwe onse angakonzekerere kuti aziyankha pamisonkhano. Mwa kugwiritsa ntchito malangizo a mu Nsanja ya Olonda ya July 1, 1999, masamba 19 ndi 20, ndime 9, akonzekere ndemanga zokayankha pa Phunziro la Nsanja ya Olonda la mlungu uno. (1) Onse m’banjamo asankhe funso limodzi kapena awiri oti akayankhe. (2) Akatha kuwerenga ndime zimene akayankhezo, akonze mayankho m’mawu awoawo. (3) Asankhe malemba ofunika kwambiri m’ndimezo amene sanagwidwe mawu, akambirane momwe lililonse likugwirizanira ndi nkhaniyo, ndipo akonze zonena pogwirizanitsa malembawo ndi phunzirolo. Onse akonzekere kukayankha pamsonkhano.
Nyimbo Na. 222 ndi pemphero lomaliza.
Mlungu Woyambira January 2
Mph. 8: Zilengezo za pampingo. Gwiritsani ntchito zitsanzo zimene zili pa tsamba 8 (ngati zingakhale zothandiza m’gawo lanu) kusonyeza chitsanzo cha mmene tingagawire Galamukani! ya December 8 ndi Nsanja ya Olonda ya January 1.
Mph. 17: “Gwiritsani Ntchito Mwanzeru Mabuku Athu Ofotokoza Baibulo.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Fotokozaninso ndemanga za mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa September 2002, tsamba 1.
Mph. 20: Thandizani Ena Kulimvetsetsa Baibulo. Nkhani ya mafunso ndi mayankho yochokera m’buku la Lambirani Mulungu, masamba 24 ndi 25, ndime 3 mpaka 6. Gwiritsani ntchito mafunso a m’bukulo. Phatikizanipo ndemanga za m’bulosha la Buku la Anthu Onse, tsamba 32.
Nyimbo Na. 48 ndi pemphero lomaliza.