Ndandanda ya Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2008
MALANGIZO
Dongosolo lotsatirali ndilo lidzagwiritsidwe ntchito pochititsa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu mu 2008.
MABUKU OPHUNZIRA: Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu [bi53-CN], Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu [bi7-CN], Nsanja ya Olonda [w-CN], Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu [be-CN], Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova [od-CN], ndi Kukambitsirana za m’Malemba [rs-CN].
Sukulu iyenera kuyamba PANTHAWI YAKE ndi nyimbo, pemphero, ndi mawu amalonje, kenako iyenera kutsatira ndondomeko yotsatirayi. Pambuyo pa nkhani iliyonse, woyang’anira sukulu atchule nkhani yotsatira ndi kuitana wokamba wake.
LUSO LA KULANKHULA: Mphindi 5. Woyang’anira sukulu, mlangizi wothandiza, kapena mkulu wina woyenerera akambe nkhani ya luso la kulankhula yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki. (Mipingo imene ili ndi akulu ochepa ingagwiritse ntchito atumiki othandiza oyenerera.)
NKHANI NA. 1: Mphindi 10. Mkulu woyenerera kapena mtumiki wothandiza woyenerera ndi amene ayenera kukamba nkhani imeneyi, ndipo izitengedwa mu Nsanja ya Olonda, m’buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, kapena m’buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova. Imeneyi ndi nkhani yolangiza imene iyenera kukambidwa kwa mphindi khumi. Cholinga chake chisakhale kufotokoza mwachisawawa mfundo za m’nkhaniyo koma kusonyeza phindu la mfundozo, ndi kutsindika mfundo zimene zingathandize kwambiri mpingowo. Agwiritse ntchito mutu wosonyezedwa. Abale amene apatsidwa nkhani imeneyi azionetsetsa kuti akusunga nthawi. M’bale amene wakamba nkhani imeneyi angapatsidwe malangizo payekha ngati pakufunika kutero.
MFUNDO ZAZIKULU ZA KUWERENGA BAIBULO: Mphindi 10. Kwa mphindi zisanu zoyambirira, mkulu kapena mtumiki wothandiza woyenerera afotokoze mmene machaputala omwe awerengedwa mlunguwo angathandizire mpingowo. Angafotokoze mbali ina iliyonse ya chigawo cha kuwerenga Baibulo cha mlunguwo. Isakhale chidule chabe cha gawo lowerenga mlunguwo. Cholinga chachikulu ndicho kuthandiza omvera kuzindikira chifukwa chake ndiponso mmene mfundozo zilili zaphindu. Wokamba nkhani ayenera kuonetsetsa kuti asapitirire mphindi zisanu zoperekedwa pa mbali yoyambirira imeneyi. Aonetsetse kuti wapereka mwayi kwa omvera kuti alankhulepo kwa mphindi zisanu zomalizira. Apemphe omvera kulankhulapo mwachidule (kwa masekondi 30 kapena kucheperapo) pa mfundo za m’Baibulo zimene zinawasangalatsa powerenga ndiponso phindu lake. Ndiyeno woyang’anira sukulu apemphe ophunzira amene ali m’makalasi ena kupita ku makalasi awo.
NKHANI NA. 2: Mphindi 4 kapena zocheperapo. Iyi ndi nkhani yoti m’bale awerenge. Wophunzira awerenge nkhani imene wapatsidwa popanda kunena mawu oyamba kapena omaliza. Woyang’anira sukulu makamaka adzaonetsetsa kuti akuthandiza wophunzira kuwerenga mosonyeza kuti akumvetsa zimene akuwerengazo, kuwerenga mosadodoma, kutsindika mfundo moyenera, kusinthasintha mawu, kupuma moyenera, ndiponso kuwerenga mwachibadwa.
NKHANI NA. 3: Mphindi 5. Iyi ndi nkhani ya alongo. Alongo amene apatsidwa nkhani imeneyi angasankhe okha kapena angachite kupatsidwa mtundu wa makambirano kuchokera pa mndandanda umene uli patsamba 82 m’buku la Sukulu ya Utumiki. Wophunzira agwiritse ntchito mutu wa nkhani umene wapatsidwa ndipo agwirizanitse ndi mbali ya utumiki wakumunda yomwe ndi yotheka ndiponso yothandiza m’gawo la mpingowo. Ngati sanasonyeze buku limene nkhaniyo yachokera, wophunzira adzafunika kupeza mfundo za nkhani imeneyo mwa kufufuza m’mabuku athu. Ophunzira atsopano azipatsidwa nkhani zimene tasonyeza buku limene nkhaniyo yachokera. Woyang’anira sukulu adzaonetsetsa makamaka mmene wophunzira akufotokozera nkhaniyo ndiponso mmene akuthandizira mwininyumba kulingalira pa Malemba ndi kumvetsa mfundo zazikulu za nkhaniyo. Woyang’anira sukulu adzasankha wothandiza mmodzi.
NKHANI NA. 4 Mphindi 5. Wophunzira akambe nkhani pa mutu umene wapatsidwa. Ngati sitinasonyeze buku limene nkhaniyo yachokera, wophunzira adzafunika kupeza mfundo za nkhani imeneyo mwa kufufuza m’mabuku athu. Akapatsidwa m’bale, aziikamba monga nkhani yokambira omvera amene asonkhana m’Nyumba ya Ufumuyo. Mlongo akapatsidwa nkhani imeneyi, nthawi zonse aziikamba mofanana ndi Nkhani Na. 3. Woyang’anira sukulu angapereke Nkhani Na. 4 kwa m’bale nthawi ina iliyonse imene akuona kuti m’poyenera kupatsa m’bale. Dziwani kuti nkhani zimene zili ndi nyenyezi ziyenera kuperekedwa kwa abale basi. Ngati mpingo wanu uli ndi akulu ndiponso atumiki othandiza ambirimbiri, mungachite bwino kupereka nkhani zokhala ndi nyenyezi kwa abale amenewa kuti akambe ngati pakufunika kutero.
MALANGIZO: Mphindi imodzi. Nkhani ya wophunzira isanayambe, woyang’anira sukulu asalengeze luso la kulankhula limene wophunzirayo wauzidwa kuti agwiritse ntchito. Wophunzira aliyense akamaliza Nkhani Na. 2, Na. 3, ndi Na. 4, woyang’anira sukulu anene zinthu zimene wophunzirayo wachita bwino pokamba nkhaniyo. Cholinga chake sindicho kungonena kuti “mwachita bwino” mbali yakutiyakuti, koma kutchula zifukwa zenizeni zimene zachititsa kuti mbali imeneyo ikhaledi yothandiza. Malinga ndi zimene wophunzira aliyense akufunikira, malangizo ena othandiza angaperekedwe kwa wophunzirayo misonkhano itatha kapena panthawi ina.
KUSUNGA NTHAWI: Nkhani iliyonse isadye nthawi, chimodzimodzinso ndi ndemanga za mlangizi. Nkhani Na. 2 mpaka Na. 4 ziziimitsidwa mwaluso nthawi yake ikatha. Ngati m’bale amene wakamba nkhani yotsegulira ya luso la kulankhula, kapena Nkhani Na. 1, kapenanso mfundo zazikulu za kuwerenga Baibulo wadya nthawi, azilangizidwa payekha. Aliyense ayenera kusamala kwambiri nthawi. Pulogalamu yonse izitenga mphindi 45, osaphatikizapo nthawi ya nyimbo ndi pemphero.
FOMU YOLANGIZIRA: Ili m’buku momwemo.
MLANGIZI WOTHANDIZA: Bungwe la akulu lingasankhe mkulu waluso, ngati alipo, kuphatikiza pa woyang’anira sukulu, kuti akhale mlangizi wothandiza. Ngati pali akulu angapo pa mpingo, ndiye kuti chaka chilichonse bungwe la akulu lizisankha mkulu wina woyenerera kuti azichita ntchito imeneyi. Iyeyu azipereka malangizo kwa abale amene akamba Nkhani Na. 1 ndi mfundo zazikulu za Baibulo ngati pangafunike kutero. Azipereka malangizowo kwa m’bale aliyense payekhapayekha. N’kosafunika kuti azipereka malangizo kwa akulu anzake kapena atumiki othandiza nthawi iliyonse yomwe akamba nkhani zimenezi.
KUBWEREZA: Mphindi 30. Miyezi iwiri iliyonse, woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwerezaku. Kudzatsatira pambuyo pa kukambirana luso la kulankhula ndi mfundo zazikulu za kuwerenga Baibulo monga mmene tafotokozera pamwambapa. Kubwerezaku kudzakhala kwa nkhani zimene zinakambidwa m’sukulu m’miyezi iwiri yapitayo, kuphatikizapo mlungu wa kubwerezaku. Ngati mpingo wanu udzakhala ndi msonkhano wadera mlungu umene muyenera kukhala ndi kubwereza, ndiye kuti kubwerezako (limodzinso ndi pulogalamu ya mlungu ndi mlungu ya mlungu umenewo) ziyenera kudzachitika mlungu wotsatira ndipo pulogalamu ya mlungu wotsatirawo iyenera kuchitidwa mlungu wa msonkhanowo. Ngati woyang’anira dera akuchezera mpingo wanu mlungu umene muyenera kukhala ndi kubwerezaku, ndiye kuti nyimbo, luso la kulankhula, ndiponso mfundo zazikulu za kuwerenga Baibulo ziyenera kuchitika mogwirizana ndi ndandanda ya mlungu umenewo. Ndiyeno nkhani yolangiza (yokambidwa pambuyo pa luso la kulankhula) iyenera kutengedwa ku ndandanda ya mlungu wotsatira. Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu wotsatira idzakhala ndi luso la kulankhula ndi mfundo zazikulu za kuwerenga Baibulo mogwirizana ndi mmene zilili pa ndandanda ya mlunguwo, ndipo kubwereza kudzatsatira pambuyo pake.
Ndandanda
Jan. 7 Kuwerenga Baibulo: Mateyo 1-6 Nyimbo 62
Luso la Kulankhula: Perekani Mafotokozedwe Ofunikira (be-CN tsa. 228 ndime 2 ndi 3)
Na. 1: Titengere Chitsanzo cha Mmene Anthu M’nthawi ya Atumwi Ankalalikirira (od-CN tsa. 92 ndime 1 mpaka tsa. 95 ndime 2)
Na. 2: Mateyo 5:1-20
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Anthu Amafa? (rs-CN tsa. 151 ndime 5)
Na. 4: Njira Zimene Mzimu wa Mulungu Umatithandizira
Jan. 14 Kuwerenga Baibulo: Mateyo 7-11 Nyimbo 224
Luso la Kulankhula: Zimadaliranso Mtima wa Munthu (be-CN tsa. 228 ndime 4 mpaka tsa. 229 ndime 1)
Na. 1: Kondwerani ndi Mawu a Mulungu (be-CN tsa. 9 mpaka tsa. 10 ndime 1)
Na. 2: Mateyo 10:1-23
Na. 3: Chifukwa chake Kuona Mtima N’kopindulitsa
Na. 4: Kodi Akufa Ali Kuti Ndipo Ali Mumkhalidwe Wotani? (rs-CN tsa. 152 ndime 7 mpaka tsa. 154 ndime 4)
Jan. 21 Kuwerenga Baibulo: Mateyo 12-15 Nyimbo 133
Luso la Kulankhula: Nkhani Yophunzitsadi Kanthu Omvera (be-CN tsa. 230 ndime 1 mpaka 6)
Na. 1: Werengani Baibulo Tsiku ndi Tsiku (be-CN tsa. 10 ndime 2 mpaka tsa. 12 ndime 3)
Na. 2: Mateyo 14:1-22
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Mboni za Yehova Sizichita Nawo Miyambo ya Makolo ya Maliro? (rs-CN tsa. 155 mpaka 156 ndime 1)
Na. 4: Kodi Wokana Khrist u Ndani?
Jan. 28 Kuwerenga Baibulo: Mateyo 16-21 Nyimbo 176
Luso la Kulankhula: Kufufuza Kumathandiza Kuti Nkhani Yanu Ikhale Yophunzitsadi Kanthu (be-CN tsa. 231 ndime 1 mpaka 3)
Na. 1: “Yang’anirani Mamvedwe Anu” (be-CN tsa. 13 mpaka tsa. 14 ndime 5)
Na. 2: Mateyo 17:1-20
Na. 3: Kuyankha Anthu Amene Ali ndi Maganizo Olakwika Pankhani ya Imfa (rs-CN tsa. 156 ndime 2 mpaka 4)
Na. 4: Zinthu Zimene Akhristu Amaziona Kuti N’zopatulika
Feb. 4 Kuwerenga Baibulo: Mateyo 22-25 Nyimbo 151
Luso la Kulankhula: Fotokozani Malemba (be-CN tsa. 231 ndime 4 ndi 5)
Na. 1: Kumvetsera Pamisonkhano Yampingo Ndiponso Pamisonkhano Ikuluikulu. (be-CN tsa. 15 ndime 1 mpaka tsa. 16 ndime 5)
Na. 2: Mateyo 23:1-24
Na. 3: Kodi Moyo Wosatha Udzakhala Wosasangalatsa?
Na. 4: Maloto Ouziridwa ndi Osauziridwa (rs-CN tsa. 246 ndime 3 mpaka tsa. 247 ndime 7)
Feb. 11 Kuwerenga Baibulo: Mateyo 26-28 Nyimbo 110
Luso la Kulankhula: Kufotokoza Tanthauzo la Mawu (be-CN tsa. 232 ndime 1)
Na. 1: Kufunafuna Oyenerera (od-CN tsa. 95 ndime 3 mpaka tsa. 96 ndime 3)
Na. 2: Mateyo 27:1-22
Na. 3: Sizokwanira Kungokhulupirira Kuti Kuli Mulungu
Na. 4: N’chifukwa Chiyani Akhristu Amaletsedwa Kugwiritsa Ntchito Mankhwala Osokoneza Bongo? (rs-CN tsa. 248 mpaka tsa. 249 ndime 3)
Feb. 18 Kuwerenga Baibulo: Maliko 1-4 Nyimbo 167
Luso la Kulankhula: Kufotokoza Malemba (be-CN tsa. 232 ndime 2 mpaka ndime 4)
Na. 1: Cholinga cha Maulendo Obwereza (od-CN tsa. 97 ndime 1 mpaka tsa. 99 ndime 1)
Na. 2: Maliko 2:1-17
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Akhristu Amapewa Kusuta Chamba (rs-CN tsa. 250 mpaka tsa. 251 ndime 1)
Na. 4: Kodi Chikondi Chingachititse Bwanji Munthu Kulimba Mtima Kwambiri?
Feb. 25 Kuwerenga Baibulo: Maliko 5-8 Nyimbo 72
Luso la Kulankhula: Kusankha Mfundo Zopindulitsa Omvera (be-CN tsa. 233 ndime 1 mpaka 5)
Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki
Mar. 3 Kuwerenga Baibulo: Maliko 9-12 Nyimbo 195
Luso la Kulankhula: Kukamba Mfundo za M’nkhani Imene Mwapatsidwa (be-CN tsa. 234 mpaka tsa. 235 ndime 3)
Na. 1: Mungathe Kunola Luso Lanu Lokumbukira Zinthu (be-CN tsa. 17 mpaka tsa. 19 ndime 1)
Na. 2: Maliko 11:1-18
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Mulungu Sanganame?
Na. 4: N’chifukwa Chiyani Akhristu Amapewa Fodya? (rs-CN tsa. 251 ndime 2 mpaka tsa. 253 ndime 1)
Mar. 10 Kuwerenga Baibulo: Maliko 13-16 Nyimbo 87
Luso la Kulankhula: Kugwiritsa Ntchito Mafunso Mwaluso (be-CN tsa. 236 ndime 1 mpaka 5)
Na. 1: Kutsogolera Anthu Achidwi ku Gulu la Yehova (od-CN tsa. 99 ndime 2 mpaka tsa. 101 ndime 2
Na. 2: Maliko 14:1-21
Na. 3: Kodi Munthu Angathane Bwanji ndi Zizolowezi Zoipa? (rs-CN tsa. 253 ndime 2 mpaka tsa. 254 ndime 1)
Na. 4: N’chifukwa Chiyani “Mkwiyo wa Munthu Subala Chilungamo cha Mulungu”? (Yak. 1:20)
Mar. 17 Kuwerenga Baibulo: Luka 1-3 Nyimbo 13
Luso la Kulankhula: Mafunso Oyambira Mfundo Zofunika Kwambiri (be-CN tsa. 237 ndime 1, 2)
Na. 1: Nthawi Imene Tingauze Anthu Ena Uthenga Wabwino (od-CN tsa. 101 ndime 3 mpaka tsa. 108 ndime 3)
Na. 2: Luka 1:1-23
Na. 3: N’chifukwa Chiyani “Chikhulupiriro Chopanda Ntchito Zake N’chopanda Pake”? (Yak. 2:20)
Na. 4: Anthu Sangasokoneze Cholinga cha Mulungu Chokhudza Dziko Lapansi (rs-CN tsa. 131 ndime 2 mpaka tsa. 132 ndime 2)
Mar. 24 Kuwerenga Baibulo: Luka 4-6 Nyimbo 156
Luso la Kulankhula: Mafunso Othandiza Kuganizapo pa Nkhaniyo (be-CN tsa. 237 ndime 3 mpaka tsa. 238 ndime 2)
Na. 1: Mmene Mzimu Woyera Umathandizira Kuti Musaiwale (be-CN tsa. 19 ndime 2 mpaka tsa. 20 ndime 3)
Na. 2: Luka 4:1-21
Na. 3: Kodi Yehova Adzawononga Dziko Lapansi ndi Moto? (rs-CN tsa. 132 ndime 3 mpaka tsa. 133 ndime 5)
Na. 4: Kuopa Mulungu Kungatiletse Kuchimwa
Mar. 31 Kuwerenga Baibulo: Luka 7-9 Nyimbo 122
Luso la Kulankhula: Mafunso Olimbikitsa Munthu Kulankhula za Kukhosi (be-CN tsa. 238 ndime 3 mpaka 5)
Na. 1: N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuchita Khama pa Kuwerenga? (be-CN tsa. 21 mpaka tsa. 23 ndime 3)
Na. 2: Luka 7:1-17
Na. 3: Umboni Woti Mulungu Amatikonda Ndipo Amafuna Kuti Tizisangalala
Na. 4: Anthu a M’gulu la Yerusalemu Watsopano Sadzabwereranso Padziko Lapansi Pambuyo Poti Oipa Awonongedwa (rs-CN tsa. 134 ndime 1 ndi 2)
Apr. 7 Kuwerenga Baibulo: Luka 10-12 Nyimbo 68
Luso la Kulankhula: Mafunso Othandiza Kutsindika Mfundo (be-CN tsa. 239 ndime 1 ndi 2)
Na. 1: Mmene Mungachitire Khama pa Kuwerenga (be-CN tsa. 23 ndime 4 mpaka tsa. 26 ndime 4)
Na. 2: Luka 11:37-54
Na. 3: Kodi Cholinga cha Mulungu Polenga Dziko Lapansi Chinasintha? (rs-CN tsa. 135 ndime 1 mpaka 5)
Na. 4: Kodi Lemba la Chivumbulutso 17:17 Limatanthauzanji?
Apr. 14 Kuwerenga Baibulo: Luka 13-17 Nyimbo 86
Luso la Kulankhula: Mafunso Ovumbula Malingaliro Olakwika (be-CN tsa. 239 ndime 3 mpaka 5)
Na. 1: Kaphunziridwe Koyenera (be-CN tsa. 27 mpaka tsa. 31 ndime 2)
Na. 2: Luka 16:1-15
Na. 3: Kodi Timaphunzira Chiyani pa Lamulo la Mulungu Lokhudza Kufunkha (Lev. 19:9, 10)
Na. 4: Kodi Odwala Tingawalimbikitse Bwanji? (rs-CN tsa. 79 ndime 1 mpaka 5)
Apr. 21 Kuwerenga Baibulo: Luka 18-21 Nyimbo 182
Luso la Kulankhula: Mafanizo ndi Zitsanzo Zophunzitsadi (be-CN tsa. 240 mpaka tsa. 241 ndime 1)
Na. 1: Kulalikira kwa Anthu a Zinenero Zonse (od-CN tsa. 104 ndime 2 mpaka tsa. 106 ndime 3)
Na. 2: Luka 18:1-17
Na. 3: Kodi Anthu Amene Abale Awo Amwalira Tingawalimbikitse Bwanji? (rs-CN tsa. 80 ndime 1 mpaka 5)
Na. 4: Kodi Kuchita Zinthu “Popanda Kung’ung’udza” Kumatanthauzanji? (Afil. 2:14)
Apr. 28 Kuwerenga Baibulo: Luka 22-24 Nyimbo 218
Luso la Kulankhula: Kugwiritsa Ntchito Zitsanzo (be-CN tsa. 241 ndime 2-4)
Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki
May 5 Kuwerenga Baibulo: Yohane 1-4 Nyimbo 31
Luso la Kulankhula: Zitsanzo za M’Malemba (be-CN tsa. 242 ndime 1 ndi 2)
Na. 1: Kugwira Ntchito m’Magawo Omwe Anthu amalankhula Zinenero Zosiyanasiyana (od-CN tsa. 107 ndime 1 mpaka tsa. 108 ndime 3)
Na. 2: Yohane 3:1-21
Na. 3: Kodi Tikuphunzira Chiyani pa Zimene Davide Anachita Pokana Kupha Mfumu Sauli?
Na. 4: Kulimbikitsa Anthu Ozunzidwa Chifukwa Chochita Chifuniro cha Mulungu (rs-CN tsa. 80 ndime 6 mpaka tsa. 81 ndime 2)
May 12 Kuwerenga Baibulo: Yohane 5-7 Nyimbo 150
Luso la Kulankhula: Kodi Fanizolo Adzalimva? (be-CN tsa. 242 ndime 3 mpaka tsa. 243 ndime 1)
Na. 1: Kuphunzira Kumapindulitsa (be-CN tsa. 31 ndime 3 mpaka tsa. 32 ndime 4)
Na. 2: Yohane 6:1-21
Na. 3: Zimene Nkhani ya Hananiya ndi Safira Imatiphunzitsa
Na. 4: Kodi Anthu Otaya Mtima Chifukwa cha Chisalungamo Mungawalimbikitse Bwanji? (rs-tsa. 81 ndime 3 mpaka 6)
May 19 Kuwerenga Baibulo: Yohane 8-11 Nyimbo 102
Luso la Kulankhula: Mafanizo a Zinthu Zodziwika Bwino (be-CN tsa. 244 ndime 1 ndi 2)
Na. 1: Kugwiritsa Ntchito Baibulo Pofufuza (be-CN tsa. 33 mpaka tsa. 35 ndime 2)
Na. 2: Yohane 11:38-57
Na. 3: Kodi Mungalimbikitse Bwanji Anthu Opanikizika Kwambiri ndi Mavuto Azachuma? (rs-CN tsa. 81 ndime 7 mpaka tsa. 82 ndime 4)
Na. 4: Kodi Lamulo Lachikhumi Analiperekeranji Popeza Kuti Palibe Munthu Amene Akanaonetsetsa Kuti Likutsatiridwa?
May 26 Kuwerenga Baibulo: Yohane 12-16 Nyimbo 3
Luso la Kulankhula: Mafanizo Oyenerera Omvera (be-CN tsa. 244 ndime 3 mpaka tsa. 245 ndime 4)
Na. 1: Kuphunzira Kugwiritsa Ntchito Zida Zina Zofufuzira (be-CN tsa. 35 ndime 3 mpaka tsa. 38 ndime 4)
Na. 2: Yohane 12:1-19
Na. 3: Kulimbikitsa Anthu Olefuka Chifukwa cha Zophophonya (rs-CN tsa. 82 ndime 5)
Na. 4: Kodi Tingam’senze Bwanji Yehova Nkhawa Zathu? (Sal. 55:22)
June 2 Kuwerenga Baibulo: Yohane 17-21 Nyimbo 198
Luso la Kulankhula: Kugwiritsa Ntchito Mwaluso Zinthu Zooneka Pophunzitsa (be-CN tsa. 247 ndime 1 ndime 2)
Na. 1: Kodi Mungawonjezere Utumiki Wanu? (od-CN tsa. 109 ndime 1 mpaka 3)
Na. 2: Yohane 21:1-14
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kukhulupirira Mulungu Ngakhale Kuti Sitimuona?
Na. 4: Kodi Zoti Zamoyo Zinachita Kusintha Kuchokera ku Zopanda Moyo N’zogwirizanadi ndi Sayansi? (rs-CN tsa. 99 mpaka tsa. 100 ndime 5)
June 9 Kuwerenga Baibulo: Machitidwe 1-4 Nyimbo 92
Luso la Kulankhula: Mmene Yesu Anagwiritsira Ntchito Zinthu Zooneka Pophunzitsa (be-CN tsa. 247 ndime 3)
Na. 1: Kukhala Wofalitsa pa Mpingo (od-CN tsa. 110 ndime 1 ndi 2)
Na. 2: Machitidwe 1:1-14
Na. 3: Kodi Zokumbidwa Pansi Zimasonyezadi Kuti Zamoyo Zinachita Kusintha Kuchokera ku Zopanda Moyo? (rs-CN tsa. 101 mpaka tsa. 104 ndime 2)
Na. 4: Kodi ‘Ufulu wa Kulankhula’ Umatanthauza Chiyani? (Aheb. 3:6)
June 16 Kuwerenga Baibulo: Machitidwe 5-7 Nyimbo 2
Luso la Kulankhula: Mmene Tingaphunzitsire ndi Zinthu Zooneka (be-CN tsa. 248 ndime 1 mpaka 3)
Na. 1: Kukonza Autilaini (be-CN tsa. 39 mpaka 42)
Na. 2: Machitidwe 5:1-16
Na. 3: Kuyankha Mafunso a Anthu Okhulupirira Mfundo za Asayansi Olimbikitsa Zoti Zamoyo Zinachita Kusintha (rs-CN tsa. 104 ndime 3 mpaka 106 ndime 3)
Na. 4: N’chifukwa Chiyani Kuopa Yehova Ndiko Chiyambi cha Nzeru? (Sal. 111:10)
June 23 Kuwerenga Baibulo: Machitidwe 8-10 Nyimbo 116
Luso la Kulankhula: Kugwiritsa Mapu, Mapulogalamu a Misonkhano Yaikulu, Ndiponso Mavidiyo (be-CN tsa. 248 ndime 4 mpaka tsa. 249 ndime 2)
Na. 1: Kukonzekera Nkhani ya Ophunzira mu Sukulu (be-CN tsa. 43 mpaka tsa. 44 ndime 3)
Na. 2: Machitidwe 8:1-17
Na. 3: Kodi Yesu “Adzapulumutsa Waumphawi” M’njira Yotani? (Sal. 72:12)
Na. 4: N’chifukwa Chiyani Anthu Ambiri Alibe Chikhulupiriro? (rs-CN tsa. 67 mpaka 68 ndime 2)
June 30 Kuwerenga Baibulo: Machitidwe 11-14 Nyimbo 79
Luso la Kulankhula: Kuphunzitsa Gulu la Anthu ndi Zinthu Zooneka (be-CN tsa. 249 ndime 3 mpaka tsa. 250 ndime 1)
Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki
July 7 Kuwerenga Baibulo: Machitidwe 15-17 Nyimbo 203
Luso la Kulankhula: Kufunika kwa Njira Yokambirana (be-CN tsa. 251 ndime 1 mpaka 3)
Na. 1: Kukonzekera Nkhani Yokambirana (be-CN tsa. 44 ndime 4 mpaka tsa. 46 ndime 2)
Na. 2: Machitidwe 16:1-15
Na. 3: Zifukwa Zotumikira Yehova Mopanda Mantha
Na. 4: Kodi Munthu Angapeze Motani Chikhulupiriro? (rs-CN tsa. 68 ndime 3 mpaka tsa. 69 ndime 1)
July 14 Kuwerenga Baibulo: Machitidwe 18-21 Nyimbo 32
Luso la Kulankhula: Poyambira Pake (be-CN tsa. 251 ndime 4 mpaka tsa. 252 ndime 3)
Na. 1: Kukonzekera Nkhani Zokambira Mpingo (be-CN tsa. 47 mpaka tsa. 49 ndime 1)
Na. 2: Machitidwe 20:1-16
Na. 3: Ntchito Zathu Ndizo Zimasonyeza Kuti Tili ndi Chikhulupiriro Choti Kukubwera Dziko Latsopano (rs-CN tsa. 69 ndime 3 mpaka tsa. 70 ndime 2)
Na. 4: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani pa Lamulo Lomwe Lili pa Eksodo 23:19b?
July 21 Kuwerenga Baibulo: Machitidwe 22-25 Nyimbo 200
Luso la Kulankhula: Pamene Muyenera Kulolera (be-CN tsa. 252 ndime 4 mpaka tsa. 253 ndime 2)
Na. 1: Kukonzekera Nkhani za Mumsonkhano wa Utumiki Ndiponso Nkhani Zina (be-CN tsa. 49 ndime 2 mpaka tsa. 51 ndime 2)
Na. 2: Machitidwe 22:1-16
Na. 3: Kodi Mboni za Yehova Zimakwaniritsa Lemba la Yohane 13:34, 35 M’njira Zotani?
Na. 4: Kodi Tingawadziwe Bwanji Aneneri Onyenga? (rs-CN tsa. 32 mpaka 33 ndime 4)
July 28 Kuwerenga Baibulo: Machitidwe 26-28 Nyimbo 29
Luso la Kulankhula: Kupereka Mafunso ndi Zifukwa (be-CN tsa. 253 ndime 3 mpaka tsa. 254 ndime 2)
Na. 1: Kukatumikira Kumene Kukufunika Antchito Ambiri (od-CN tsa. 111 ndime 1 mpaka tsa. 112 ndime 2)
Na. 2: Machitidwe 26:1-18
Na. 3: Aneneri Owona Sikuti Nthawi Zonse Amadziwa Mmene Zinthu Zimene Akulosera Zidzachitikire Kapenanso Nthawi Imene Zidzachitika (rs-CN tsa. 33 ndime 5 mpaka tsa. 34 ndime 1)
Na. 4: N’chifukwa Chiyani Yehova Akuleza Mtima?
Aug. 4 Kuwerenga Baibulo: Aroma 1-4 Nyimbo 170
Luso la Kulankhula: Kupereka Zifukwa Zomveka Zochokera M’Mawu a Mulungu (be-CN tsa. 255 mpaka tsa. 256 ndime 2)
Na. 1: Zoyenereza Munthu Kukhala Mpainiya Wothandiza, Wokhazikika ndi Wapadera (od-CN tsa. 112 ndime 3 mpaka 114 ndime 1)
Na. 2: Aroma 3:1-20
Na. 3: Mmene Angelo Amatetezera Ndiponso Kulimbikitsira Atumiki a Mulungu
Na. 4: Mboni za Yehova Zimalimbikitsa Kulambira Koona (rs-CN tsa. 34 ndime 2 ndi 3)
Aug. 11 Kuwerenga Baibulo: Aroma 5-8 Nyimbo 207
Luso la Kulankhula: Kambani Zimene Maumboni Enanso Amavomereza (be-CN tsa. 256 ndime 3 mpaka 5)
Na. 1: Kukonzekera Nkhani za Onse (be-CN tsa. 52 mpaka tsa. 54 ndime 1)
Na. 2: Aroma 6:1-20
Na. 3: Mboni za Yehova Zimadziwika ndi Zipatso Zawo (rs-CN tsa. 35 mpaka 36 ndime 1)
Na. 4: Kodi Kuchita Zinthu Zolungama Kungatiteteze Bwanji?
Aug. 18 Kuwerenga Baibulo: Aroma 9-12 Nyimbo 152
Luso la Kulankhula: Perekani Umboni Wokwanira (be-CN tsa. 257 ndime 1 mpaka 3)
Na. 1: Zolinga Zimene Mungapange Potumikira Mulungu (od-CN tsa. 114 ndime 2 mpaka tsa. 116 ndime 4
Na. 2: Aroma 9:1-18
Na. 3: Kodi Miseche ndi Yoopsa Motani?
Na. 4: Kuyankha Anthu Amene Amati Ndife Aneneri Onyenga (rs-CN tsa. 36 ndime 3 mpaka 37 ndime 2)
Aug. 25 Kuwerenga Baibulo: Aroma 13-16 Nyimbo 16
Luso la Kulankhula: Yesetsani Kuwafika Pamtima Anthu (be-CN tsa. 258 ndime 1 mpaka 5)
Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki
Sept. 1 Kuwerenga Baibulo: 1 Akorinto 1-9 Nyimbo 199
Luso la Kulankhula: Kuchititsa Anthu Kunena Zakukhosi Kwawo (be-CN tsa. 259 ndime 1 mpaka 3)
Na. 1: Kodi Zolinga Zanu Zauzimu N’zotani? (od-CN tsa. 117 ndime 2 mpaka tsa. 118 ndime 3)
Na. 2: 1 Akorinto 4:1-17
Na. 3: Mulungu Sanaikiretu Nthawi Yomwe Munthu Aliyense Adzafe (rs-CN tsa. 114 ndime 2 mpaka 5)
Na. 4: Kodi Kukhala ndi Chuma Kumasonyeza Kuti Mulungu Akutidalitsa?
Sept. 8 Kuwerenga Baibulo: 1 Akorinto 10-16 Nyimbo 35
Luso la Kulankhula: Limbikitsani Maganizo Olimbikitsa (be-CN tsa. 259 ndime 4 mpaka tsa. 260 ndime 1)
Na. 1: Dongosolo lokhudza Malo Olambirira (od-CN tsa. 119 ndime 1 mpaka tsa. 120 ndime 1)
Na. 2: 1 Akorinto 13:1–14:6
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Ochita Mawu Amasangalala?
Na. 4: Si Zochitika Zonse Zimene Zili Chifuniro cha Mulungu (rs-CN tsa. 115 mpaka tsa. 116 ndime 4)
Sept. 15 Kuwerenga Baibulo: 2 Akorinto 1-7 Nyimbo 58
Luso la Kulankhula: Thandizani Ena Kuopa Mulungu (be-CN tsa. 260 ndime 2 ndi 3)
Na. 1: Nyumba ya Ufumu ndi Malo Osonkhanira Amene Mboni za Yehova Zimagwiritsira Ntchito Kwambiri (od-CN tsa. 120 ndime 2 mpaka tsa. 123 ndime 2)
Na. 2: 2 Akorinto 1:1-14
Na. 3: Mulungu Sadziwiratu ndi Kulinganiziratu Zochitika Zonse Zam’tsogolo (rs-CN tsa. 116 ndime 5 mpaka tsa. 117 ndime 1)
Na. 4: N’chifukwa Chiyani Akhristu Oona Amakhalabe Osangalala Akamazunzidwa?
Sept. 22 Kuwerenga Baibulo: 2 Akorinto 8-13 Nyimbo 12
Luso la Kulankhula: Khalidwe Lathu N’lofunika Kwambiri kwa Mulungu (be-CN tsa. 260 ndime 4 mpaka tsa. 261 ndime 1)
Na. 1: Kumene Kumachokera Thandizo la Ntchito Yomanga Nyumba za Ufumu ndi Malo a Misonkhano (od-CN tsa. 123 ndime 3 mpaka tsa. 126 ndime 3)
Na. 2: 2 Akorinto 9:1-15
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Akhristu Oona Sali Mbali ya Dziko?
Na. 4: Mmene Mulungu Amagwiritsira Ntchito Mphamvu Yake Yodziwa ndi Kulinganiza Zam’tsogolo (rs-CN tsa. 117 ndime 2 mpaka 5)
Sept. 29 Kuwerenga Baibulo: Agalatiya 1-6 Nyimbo 163
Luso la Kulankhula: Thandizani Ena Kudzifufuza (be-CN tsa. 261 ndime 2-4)
Na. 1: Kusamalira Zinthu Zaufumu (od-CN tsa. 127 ndime 1 mpaka tsa. 128 ndime 2)
Na. 2: Agalatiya 1:1-17
Na. 3: Poti Mulungu Amatha Kudziwa Zam’tsogolo, N’chifukwa Chiyani Sanasankhe Kudziwiratu Zoti Adamu Adzachimwa? (rs-CN tsa. 118 ndime 1 mpaka 3)
Na. 4: Kodi Chikondi Chingatithandize Bwanji Kuti Tisamaope Munthu?
Oct. 6 Kuwerenga Baibulo: Aefeso 1-6 Nyimbo 99
Luso la Kulankhula: Alimbikitseni Kukhala Omvera (be-CN tsa. 262 ndime 1 mpaka 4)
Na. 1: Kusamalira Zosowa za Mpingo (od-CN tsa. 129 ndime 1 mpaka 3)
Na. 2: Aefeso 3:1-19
Na. 3: Kupepesa Si Mantha
Na. 4: Mulungu Sanalemberetu Tsogolo la Yakobo, Esau, kapenanso Yudasi (rs-CN tsa. 119 ndime 1 mpaka 3)
Oct. 13 Kuwerenga Baibulo: Afilipi 1–Akolose 4 Nyimbo 123
Luso la Kulankhula: Afikeni Anthu Pamtima Mogwirizana ndi Yehova (be-CN tsa. 262 ndime 4)
Na. 1: Ndalama Zoyendetsera Misonkhano Yadera ndi Masiku a Msonkhano Wapadera (od-CN tsa. 130 ndime 1 mpaka tsa. 131 ndime 2)
Na. 2: Afilipi 3:1-16
Na. 3: Kodi Zoti Mpingo Wachikhristu Unasankhidwiratu Zimatanthauza Chiyani? (rs-CN tsa. 119 ndime 4 mpaka 120 ndime 1)
Na. 4: a Kusamalira Anthu Okhulupirika mu Mpingo (od-CN tsa. 131 ndime 4 mpaka tsa. 132 ndime 2)
Oct. 20 Kuwerenga Baibulo: 1 Atesalonika 1–2 Atesalonika 3 Nyimbo 161
Luso la Kulankhula: Kusunga Nthawi (be-CN tsa. 263 mpaka tsa. 264 ndime 4)
Na. 1: Kayendetsedwe ka Mabuku Ndi Mbali Yofunika Kwambiri pa Ntchito Yofalitsa Uthenga wa Ufumu (od-CN tsa. 133 ndime 1 mpaka 3)
Na. 2: 1 Atesalonika 1:1–2:8
Na. 3: Kodi Malemba Angatithandize Bwanji Pankhani Yokhulupirira Nyenyezi? (rs-CN tsa. 120 ndime 2 mpaka tsa. 121 ndime 4)
Na. 4: b “Chitani Zonse ku Ulemerero wa Mulungu” (od-CN tsa. 134 ndime 1 mpaka tsa. 135 ndime 1)
Oct. 27 Kuwerenga Baibulo: 1 Timoteyo 1–2 Timoteyo 4 Nyimbo 69
Luso la Kulankhula: Kulimbikitsa Ena Mogwira Mtima Kuti Achitepo Kathu (be-CN tsa. 265 ndime 1 mpaka 3)
Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki
Nov. 3 Kuwerenga Baibulo: Tito 1–Filemoni Nyimbo 149
Luso la Kulankhula: Kulimbikitsa Ena Mwachikondi (be-CN tsa. 266 ndime 2 mpaka 5)
Na. 1: Kutsatira Miyezo ya Yehova ya Makhalidwe Imene Ili Yoyera ndi Yolungama (od-CN tsa. 135 ndime 2 mpaka tsa. 136 ndime 2)
Na. 2: Tito 1:1-16
Na. 3: Kodi Zifukwa Zina Zokhulupirira Mulungu ndi Ziti? (rs-CN tsa. 307 ndime 1 mpaka 7)
Na. 4: c Chifukwa Chake Tifunika Kukhala Aukhondo (od-CN tsa. 137 ndime 1 mpaka tsa. 138 ndime 3)
Nov. 10 Kuwerenga Baibulo: Aheberi 1-8 Nyimbo 144
Luso la Kulankhula: Kulimbikitsa Ena ndi Mawu a Mulungu (be-CN tsa. 267 ndime 1 ndi 2)
Na. 1: Masewera Ndiponso Zosangalatsa Zabwino (od-CN tsa. 139 ndime 1 mpaka tsa. 140 ndime 4)
Na. 2: Aheberi 3:1-19
Na. 3: Kuipa Ndiponso Kuvutika kwa Anthu Sikutsimikizira Kuti Kulibe Mulungu (rs-CN tsa. 307 ndime 8 mpaka tsa. 308 ndime 1)
Na. 4: Kudzichepetsa Kwenikweni N’kosiyana ndi Kudzichepetsa Kwachinyengo
Nov. 17 Kuwerenga Baibulo: Aheberi 9-13 Nyimbo 28
Luso la Kulankhula: Kukhala ndi Ufulu wa Kulankhula (be-CN tsa. 267 ndime 3 ndi 4)
Na. 1: Khalani Osiyana ndi Dziko Kusukulu ndi Pantchito Yolembedwa (od-CN tsa. 141 ndime 1 mpaka tsa. 142 ndime 3)
Na. 2: Aheberi 10:1-17
Na. 3: Mulungu ndi Munthu Weniweni Yemwe Amatha Kukhudzidwa ndi Zinthu (rs-CN tsa. 309 ndime 1 mpaka 5)
Na. 4: Mmene Kukhululuka Kumalimbikitsira Umodzi
Nov. 24 Kuwerenga Baibulo: Yakobe 1-5 Nyimbo 88
Luso la Kulankhula: Kufunika Kolimbikitsa Omvera (be-CN tsa. 268 ndime 1 mpaka 3)
Na. 1: Kukhala mu Umodzi Wachikristu (od-CN tsa. 143 ndime 1 mpaka 4)
Na. 2: Yakobe 1:1-21
Na. 3: Mulungu Alibe Chiyambi (rs-CN tsa. 309 ndime 6 mpaka tsa. 310 ndime 1)
Na. 4: Kodi “Chifundo N’chopambana Kwambiri Kuposa Chiweruzo” M’njira Yotani? (Yak. 2:13)
Dec. 1 Kuwerenga Baibulo: 1 Petulo 1–2 Petulo 3 Nyimbo 18
Luso la Kulankhula: Akumbutseni Zimene Yehova Wachita (be-CN tsa. 268 ndime 4 mpaka tsa. 269 ndime 2)
Na. 1: Mmene Tingapindulire Pogonjera Dongoloso la Mulungu Lolemekeza Mutu (od-CN tsa. 159 ndime 1 mpaka tsa. 160 ndime 2)
Na. 2: 1 Petulo 2:1-17
Na. 3: Kugwiritsa Ntchito Dzina la Mulungu N’kofunika Kuti Tidzapulumuke (rs-CN tsa. 310 ndime 2 mpaka 5)
Na. 4: d Mbali Zimene Timafunika Kulemekeza Yemwe Ali Mutu (od-CN tsa. 161 ndime 1 mpaka tsa. 163 ndime 2)
Dec. 8 Kuwerenga Baibulo: 1 Yohane 1-5; 2 Yohane 1-13; 3 Yohane 1-14–Yuda 1-25 Nyimbo 50
Luso la Kulankhula: Kusonyeza Mmene Yehova Wathandizira Anthu Ake (be-CN tsa. 269 ndime 3 mpaka 5)
Na. 1: Gulu Logwirizana la Abale (od-CN tsa. 163 ndime 3 mpaka tsa. 165 ndime 1)
Na. 2: 1 Yohane 4:1-16
Na. 3: Kodi Zipembedzo Zonse N’zabwino? (rs-CN tsa. 310 ndime 6 mpaka tsa. 311 ndime 2)
Na. 4: e Kusunga Umodzi Wathu Wapadziko Lonse (od-CN tsa. 165 ndime 2 mpaka tsa. 166 ndime 2)
Dec. 15 Kuwerenga Baibulo: Chivumbulutso 1-6 Nyimbo 219
Luso la Kulankhula: Sonyezani Kuti Mukusangalala ndi Zimene Mulungu Akuchita Tsopano (be-CN tsa. 270 mpaka tsa. 271 ndime 2)
Na. 1: Kuderana Nkhawa (od-CN tsa. 167 ndime 1 mpaka tsa. 168 ndime 1)
Na. 2: Chivumbulutso 3:1-13
Na. 3: Kodi Yesu ndi “Mulungu” M’njira Yotani? (rs-CN tsa. 311 ndime 3 ndi 4)
Na. 4: Pali Malire Osonyeza Kuleza Mtima Ndiponso Chifundo
Dec. 22 Kuwerenga Baibulo: Chivumbulutso 7-14 Nyimbo 21
Luso la Kulankhula: Pindulani Kwambiri ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (be-CN tsa. 5 mpaka tsa. 8 ndime 1)
Na. 1: Tinapatulidwa Kuti Tichite Chifuniro cha Yehova (od-CN tsa. 168 ndime 2 mpaka tsa. 170 ndime 1)
Na. 2: Chivumbulutso 8:1-13
Na. 3: Kuyankha Anthu Amene Akuti Samakhulupirira Mulungu (rs-CN tsa. 311 ndime 5 mpaka tsa. 313 ndime 1)
Na. 4: Kodi Mawu Akuti “Mulungu ndi Wamkulu Kuposa Mitima Yathu” Amatanthauza Chiyani? (1 Yoh. 3:20)
Dec. 29 Kuwerenga Baibulo: Chivumbulutso 15-22 Nyimbo 60
Luso la Kulankhula: Kuwerenga Molondola (be-CN tsa. 83 ndime 1 mpaka 5)
Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki
[Mawu a M’munsi]
a Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha, makamaka akulu ndi atumiki othandiza.
b Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha, makamaka akulu ndi atumiki othandiza.
c Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha, makamaka akulu ndi atumiki othandiza.
d Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha, makamaka akulu ndi atumiki othandiza.
e Nkhani imeneyi muipereke kwa abale okha, makamaka akulu ndi atumiki othandiza.