Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
DZIWANI IZI: Mwachidziwikire mwaona kuti kuyambira ndi Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 2007, patsamba 2, pamapeto pamsonkhano wa mlungu uliwonse sitinatchulepo za pemphero lomaliza. Tachita choncho kuti tizitsatira dongosolo loyenera lokhudza pemphero lomaliza limene linatchulidwa pa zilengezo patsamba 7, la Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 2007.
Mlungu Woyambira December 10
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Mwa kugwiritsa ntchito malangizo amene ali pa tsamba 8 kapena ulaliki wina uliwonse umene ungakhale woyenerera gawo lanu, sonyezani zitsanzo za mmene tingachitire pogawira Nsanja ya Olonda ya December 15 ndi Galamukani! ya December.
Mph.20: Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya 2008. Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira sukulu. Fotokozani mfundo zofunika kugogomezera za mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa October 2007. Fotokozaninso ntchito ya mlangizi wothandiza. Limbikitsani onse kuti aziyesetsa kukwaniritsa mbali yawo imene apatsidwa, aziyankhapo pa mfundo zazikulu, ndi kugwiritsa ntchito malangizo amene amaperekedwa mlungu ndi mlungu kuchokera m’buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.
Mph.15: “Limbikitsani Anthu Osweka Mtima.”a Fotokozani mwachidule chochitika chimodzi kapena ziwiri za kwanuko.
Nyimbo 34
Mlungu Woyambira December 17
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Zilengezo zina musankhe mu Utumiki Wathu wa Ufumu.
Mph.15: “Tiyeni Tipitirize Kukhala Achangu Muutumiki.”b Funsani mafunso wofalitsa amene amadziwika kuti ndi wachangu muutumiki. Mafunso oti mufunse: Kodi ndi khama lotani limene mwachita kuti mupitirize kukhala wachangu? N’chiyani chakuthandizani kukhala wachangu?
Mph.20: “Gawirani Magazini Amene Amachitira Umboni Choonadi.”c Pemphani omvera kuti afotokoze mfundo zimene zili pa tsamba 8 mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2006. Limbikitsani omvera kuwerenga Nsanja ya Olonda ya January 1 ndi Galamukani ya January. Apempheni adzabweretse magazini amenewa kumsonkhano wa mlungu wamawa.
Nyimbo 139
Mlungu Woyambira December 24
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Werengani lipoti la maakaunti ndi mawu oyamikira zopereka olembedwa pa sitetimenti yochokera ku ofesi. Tchulani mabuku ogawira mu January, ndipo onetsani chitsanzo chimodzi cha kagawiridwe kake.
Mph.15: Konzekerani Kugawira Magazini Atsopano. Nkhani yokambirana ndi omvera pogwiritsa ntchito Nsanja ya Olonda ya January 1 ndi Galamukani! ya January. Mutafotokoza mwachidule zimene zili m’magazini iliyonse, pemphani omvera kuti atchule nkhani zimene zingakhale zogwira mtima kwa anthu a m’gawo lanu ndipo afotokoze zifukwa zake. Pemphani omvera kuti afotokoze mmene angachitire pogawira magaziniwo mwa kugwiritsa ntchito nkhani zimene angasankhe. Kodi mungafunse funso lotani kuti muyambitse makambirano? Kenako, kodi ndi lemba liti m’nkhaniyo limene mungagwiritse ntchito? Kodi mungagwirizanitse motani lembalo ndi nkhaniyo? Pogwiritsa ntchito zitsanzo za mu Utumiki Wathu wa Ufumu kapena ulaliki wina umene omvera afotokoza, chitani chitsanzo cha mmene mungagawirire magazini iliyonse.
Mph.20: “Khalani ndi Cholinga Chopeza Phunziro la Baibulo.”d Funsani mafunso munthu mmodzi kapena awiri amene ayambitsa phunziro la Baibulo posachedwa. Kodi analiyambitsa motani phunzirolo? Kodi likupita patsogolo motani?
Nyimbo 21
Mlungu Woyambira December 31
Mph.10: Zilengezo za pampingo. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti awo a utumiki wakumunda a mwezi wa December.
Mph.15: “Kodi Kukhala Munthu Wodzipereka kwa Mulungu Kumatithandiza kucita Zotani?” Nkhaniyi ikambidwe ndi mkulu n’cholinga cholimbikitsa mpingo.
Mph.20: “Makolo, Phunzitsani Ana Anu Mowafika Pamtima—Gawo 1.”e Kambiranani ndime 1 mpaka 7. Werengani ndi kukambirana Malemba onse osagwidwa mawu.
Nyimbo 202
Mlungu Woyambira January 7
Mph.10: Zilengezo za pampingo.
Mph.15: Zosowa za pampingo.
Mph.20: “Makolo, Phunzitsani Ana Anu Mowafika Pamtima—Gawo 1.”f Kambiranani ndime 8 mpaka 13. Werengani ndi kukambirana Malemba onse osagwidwa mawu.
[Mawu a M’munsi]
a Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
b Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
c Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
d Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
e Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.
f Mawu oyamba asapitirire mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho.