Ndandanda ya Mlungu wa May 25
MLUNGU WOYAMBIRA MAY 25
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl-CN mutu 19 ndime 18-23 ndi bokosi la patsamba 198
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Eksodo 34–37
Na. 1: Eksodo 37:1-24
Na. 2: Kodi Ndi Bwino Kuchita Ndewu? (lr-CN mutu 19)
Na. 3: Kodi Khalidwe Lolekerera Ndi Lotani, Ndipo N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kulipewa?
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph.5: Zilengezo.
Mph.10: Konzekerani Kugawira Magazini ya Nsanja ya Olonda ya June 1 ndi Galamukani! ya June. Fotokozani mwachidule mfundo za m’magaziniwa ndipo funsani omvera kuti atchule nkhani zimene akonzekera kudzagwiritsa ntchito pogawira magaziniwa ndipo anene chifukwa chake. Kodi ndi mafunso komanso malemba ati amene angagwiritse ntchito pogawira magaziniwa? Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawire magazini iliyonse m’gawo lanu.
Mph.10: Kuchitira Umboni za Yesu. Nkhaniyi ili m’buku la Sukulu ya Utumiki kuyambira pakamutu komwe kali patsamba 275 ndime 1-3 ndiponso tsamba 276 ndime 1.
Mph.10: “Gwiritsani Ntchito Bwino Mabuku Athu.” Nkhani ya mafunso ndi mayankho. Dziwitsani mpingo za kusiyana kwa chiwerengero cha mabuku amene mumalandira ndi chiwerengero chimene anthu amachitira lipoti kuti agawira mu utumiki.