Ndandanda ya Mlungu wa January 11
MLUNGU WOYAMBIRA JANUARY 11
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
lv mutu 1, ndime 10-18 ndi bokosi patsamba 13a
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yoswa 21-24
Na. 1: Yoswa 24:1-13
Na. 2: Kodi Mulungu Ndi Wouma Mtima Ndipo Saganizira Anthu?
Na. 3: Kodi Baibulo Limasonyeza Kuti Moyo Umapulumuka Imfa ya Thupi? (rs tsa. 144 ndime 4 mpaka tsa. 145 ndime 1.
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 15: Phunzitsani Ophunzira Anu Kaphunziridwe Koyenera. Nkhani yokambirana ndi omvera yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki pa kamutu kakuti “Kaphunziridwe Koyenera” patsamba 28 mpaka tsamba 31. Yambani ndi chitsanzo chosonyeza wofalitsa waluso amene akusonyeza munthu amene wayamba kumene kuphunzira Baibulo, kuti adziwe zoyenera kuchita pokonzekera kuphunzira. Agwiritse ntchito mfundo za patsamba 7 m’buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani.
Mph. 15: “Kodi Ndine Woyenerera Kulalikira?” Nkhani ya mafunso ndi mayankho. Pambuyo pokambirana ndime 4, funsani wofalitsa wina mafunso ngati awa: Kodi ndi mavuto ati amene munalimbana nawo kuti muzilalikira mogwira mtima? Kodi munathandizidwa bwanji kuti mukhale wofalitsa wachangu komanso waluso?
[Mawu a M’munsi]
a Mungasankhe kukambirana bokosi kapena ayi.