Ndandanda ya Mlungu wa April 26
MLUNGU WOYAMBIRA APRIL 26
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 1 Samueli 26-31
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Konzekerani Kugawira Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Choyamba chitani chitsanzo. Mpainiya asonyeze zimene angachite pogawira magazini atsopano a Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! Kenako pemphani omvera kuti atchule mwachidule nkhani, mafunso ndiponso malemba amene angagwiritse ntchito pogawira magaziniwo.
Mph. 20: Gwirani Nawo Ntchito Yaikulu Yofunafuna Anthu. Nkhani yochokera m’buku la Gulu, kuyambira patsamba 95 pakamutu kakuti, “Kufunafuna Oyenerera.” Pemphani omvera kuyankha mafunso otsatirawa. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi maganizo abwino polankhula ndi anthu a m’gawo lathu? Kodi kukhala ndi maganizo abwino kungathandize bwanji utumiki wathu kuyenda bwino? Funsani mwachidule wofalitsa mmodzi amene khama lake lathandiza kuti akhale ndi zotsatira zabwino mu utumiki.