Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 4/10 tsamba 3
  • Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
km 4/10 tsamba 3

Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira April 26, 2010. Woyang’anira sukulu adzatsogolera kubwereza nkhani zomwe zakambidwa m’kati mwa milungu ya March 1 mpaka April 26, 2010. Kubwerezaku kudzakhala kwa mphindi 20.

1. Kodi Naomi ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti “Yehova wandichitira umboni wakunditsutsa, ndi Wamphamvuyonse wandichitira chowawa”? (Rute 1:21) [w05 3/1 tsa. 27 ndime 1]

2. Kodi ndi makhalidwe ati amene anachititsa Rute kukhala “mkazi waulemu” kapena kuti wabwino? (Rute 3:11) [w05 3/1 tsa. 28 ndime 6]

3. Kodi mawu a Elikana akuti “ine sindili wakuposa ana khumi kwa iwe kodi” analimbikitsa bwanji mkazi wake? (1 Sam. 1:8) [w90 3/15 tsa. 27 ndime 5-6]

4. Kodi chinalakwika n’chiyani pamene Aisiraeli anapempha kuti akhale ndi mfumu? (1 Sam. 8:5) [w05 9/15 tsa. 20, ndime 17; it-2-E tsa. 163 ndime 1]

5. Pamene Samueli anali “wokalamba waimvi” anapereka bwanji chitsanzo chabwino pa nkhani yopempherera ena, ndipo kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani? (1 Sam. 12:2, 23) [w07 6/1 tsa. 29 ndime 14-15]

6. N’chifukwa chiyani Sauli anakomera mtima Akeni? (1 Sam. 15:6) [w05 3/15 tsa. 22 ndime 10]

7. N’chifukwa chiyani Sauli anafunsa Davide kuti, “Mnyamata iwe, ndiwe mwana wa yani?” (1 Sam. 17:58) [w07 8/1 tsa. 31 ndime 3, 5]

8. Kodi zimene Davide anachita ku Gati atakumana ndi vuto lalikulu zikutiphunzitsa chiyani? (1 Sam. 21:12, 13) [w05 3/15 tsa. 24 ndime 4]

9. Kodi Jonatani anasonyeza bwanji chikondi ndiponso kudzichepetsa pa nthawi imene anafunika kuthandiza ndiponso kulimbikitsa Davide yemwe anali mnzake? (1 Sam. 23:17) [lv tsa. 30 ndime 10, mawu a m’munsi.]

10. Kodi nkhani ya Sauli ndi mkazi wobwebweta wa ku Endori ikutiphunzitsa chiyani? (1 Sam. 28:8-19) [w05 3/15 tsa. 24 ndime 7]

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena