Atumiki Achikhristu Ayenera Kupemphera
1. Kodi chofunika n’chiyani kuti tikwanitse utumiki wathu?
1 Sitingathe kukwaniritsa utumiki wathu popanda thandizo la Yehova. Iye amatipatsa mphamvu yofunikira kuti tigwire ntchitoyi. (Afil. 4:13) Iye amagwiritsa ntchito angelo ake kuti atithandize kupeza anthu onga nkhosa. (Chiv. 14:6,7) Yehova ndi amene amakulitsa mbewu za choonadi zimene timabzala ndiponso kuthirira. (1 Akor. 3:6, 9) Choncho, m’pofunika kwambiri kuti Atumiki achikhristu azipemphera kwa Yehova posonyeza kuti amamudalira.
2. Kodi zina mwa zinthu zimene tingapempherere ndi ziti?
2 Tizipemphera Patokha: Tiyenera kupemphera nthawi iliyonse tikamapita kolalikira. (Aef. 6:18) Kodi tiyenera kupempherera zinthu zotani? Tingapemphe kuti tiziwaona bwino anthu a m’gawo lathu ndiponso kuti tikhale olimba mtima. (Mac. 4:29) Tingam’pemphe Yehova kuti atitsogolere kwa anthu amitima yabwino omwe tingathe kuphunzira nawo Baibulo. Ngati mwininyumba watifunsa funso, tingapereke pemphero lachidule la mumtima lopempha Yehova kuti atithandize kuyankha moyenera. (Neh. 2:4) Tingapempherenso kuti tiziuona utumiki wathu kukhala chinthu chofunika kwambiri. (Yak. 1:5) Komanso Yehova amasangalala ngati popemphera timatchula mawu oyamikira chifukwa chotipatsa mwayi wapadera wokhala atumiki ake.—Akol. 3:15.
3. Kodi kupempherera ena kumapititsa bwanji patsogolo ntchito yolalikira?
3 Tizipempherera Ena: Tiyeneranso “kupemphererana wina ndi mnzake,” ndipo nthawi zina ndi bwino kutchula mayina a atumiki anzathu m’pempherolo. (Yak. 5:16; Mac. 12:5) Kodi mavuto ena okhudza thanzi lanu akukulepheretsani kulalikira mokwanira? Ngati ndi choncho, mungapempherere atumiki ena amene ali ndi thanzi labwino. Nthawi zonse muzidziwa kuti pemphero limene mungapereke m’malo mwawo ndi lamtengo wapatali. Ndibwinonso kupemphera kuti atsogoleri andale asamatsutse ntchito yathu yolalikira, n’cholinga choti abale athu akhale ndi “moyo wabata ndi wamtendere.”—1 Tim. 2:1, 2.
4. N’chifukwa chiyani tiyenera kulimbikirabe kupemphera?
4 Patokha sitingathe kukwanitsa kulengeza uthenga wabwino padziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Koma ngati ‘titalimbikirabe kupemphera,’ Yehova angatithandize.—Aroma 12:12.