Ndandanda ya Mlungu wa September 27
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 27
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo
lv mutu 12 ndime 15-22, ndi bokosi patsamba 140
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Kuwerenga Baibulo: 2 Mafumu 23-25
Na. 1: 2 Mafumu 23:1-7
Na. 2: Kodi Ndi Zikhulupiriro za Mboni za Yehova Ziti Zimene Zimawapangitsa Kukhala Osiyana ndi Zipembedzo Zina? (rs-CN tsa. 270 ndime 3–tsa. 272 ndime 3)
Na. 3: Kodi Akhristu Oona Angaonetse Kuwala Kwawo M’njira Ziti? (Mat. 5:14-16)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 15: Konzekerani Kugawira Magazini a October. Nkhani yokambirana. Fotokozani nkhani zimene zili m’magaziniwo kwa mphindi imodzi kapena ziwiri. Ndiyeno sankhani nkhani ziwiri kapena zitatu ndi kupempha omvera kuti atchule mafunso ndi malemba okhudza nkhanizo amene angagwiritse ntchito pogawira magaziniwo. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawirire magaziniwo.
Mph. 15: “Kodi Muyambitsa Nawo Phunziro la Baibulo M’mwezi wa October?” Nkhani ya mafunso ndi mayankho. Chitani chitsanzo chimodzi kapena ziwiri.