Ndandanda ya Mlungu wa February 28
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 28
Nyimbo Na. 5 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 3 ndime 10-19 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Esitere 1-5 (Mph. 10)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Uthenga Wanu Uzikhala Wolimbikitsa. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 202. Pogwiritsa ntchito buku logawira mwezi uno, chitani chitsanzo chotsatira mfundo zimene zili mu ndime yomaliza.
Mph. 10: Pindulani ndi Kabuku ka Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku. Nkhani yokambirana pogwiritsa ntchito mawu oyamba a m’kabuku ka Kusanthula Malemba—2011. Limbikitsani onse kuti azikambirana lemba la m’kabukuka tsiku lililonse. Pemphani omvera kuti afotokoze nthawi imene amawerenga lemba la m’kabukuka ndi mmene apindulira. Fotokozani mwachidule lemba la chaka cha 2011. Kambiranani kamutu kakuti “Lemba la Tsiku Silizigwiritsidwanso Ntchito pa Msonkhano Wokonzekera Utumiki Wakumunda.”
Mph. 10: Konzekerani Kugawira Magazini Mwezi wa March. Nkhani yokambirana. Fotokozani zimene zili m’magaziniwo kwa mphindi imodzi kapena ziwiri. Kenako sankhani nkhani ziwiri kapena zitatu, ndipo pemphani omvetsera kuti anene mafunso ndiponso malemba a m’nkhaniyo amene angagwiritsire ntchito pogawira magaziniwo. Chitani chitsanzo chosonyeza zimene tingachite pogawira magazini iliyonse.
Nyimbo Na. 33 ndi Pemphero