Ndandanda ya Mlungu wa August 29
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 29
Nyimbo Na. 45 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 12, ndime 1-7 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Masalimo 110–118 (Mph. 10)
Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zilengezo. Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chimene chili patsamba 8, chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingayambitsire phunziro la Baibulo, Loweruka loyamba m’mwezi wa September. Limbikitsani onse kuti ayesetse kuyambitsa maphunziro. Kambani nkhani pogwiritsa ntchito mutu wakuti “Gawirani Magazini Kapena Kabuku Kakale Kogwirizana Ndi Zimene Munthu Alinazo Chidwi.”
Mph. 15 Akhama mu Utumiki Ngakhale Kuti ndi Okalamba. Nkhani yokambirana, yochokera mu Nsanja ya Olonda ya June 1, 2007, tsamba 28 ndi 29, ndime 10 mpaka 15. Pemphani omvera kufotokoza zimene aphunzira mu nkhaniyi.
Mph. 10 Konzekerani Kugawira Magazini M’mwezi wa September. Nkhani yokambirana. Fotokozani zimene zili m’magaziniwo kwa mphindi imodzi kapena ziwiri. Kenako sankhani mitu iwiri kapena itatu, ndipo funsani omvera kuti afotokoze mafunso ndiponso malemba amene angagwiritse ntchito pogawira magaziniwo. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawire magazini iliyonse.
Nyimbo Na. 31 ndi Pemphero