Ndandanda ya Mlungu wa August 27
MLUNGU WOYAMBIRA AUGUST 27
Nyimbo Na. 85 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 11 ndime 5-12 ndi bokosi patsamba 89 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Ezekieli 35-38 (Mph. 10)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zilengezo. “Phunziro la Baibulo la Mpingo ndi Msonkhano wa Utumiki Zasintha.” Nkhani. Mukamaliza kukamba nkhaniyi, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki chimene chili patsamba 4 posonyeza mmene tingagwiritsire ntchito magazini poyambitsa maphunziro a Baibulo Loweruka loyambirira m’mwezi wa September.
Mph. 15: Muzilalikira Momveka Bwino. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki, tsamba 226 mpaka 229. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingagwiritsire ntchito mfundo imodzi kapena ziwiri za m’nkhaniyi.
Mph. 10: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani Luka 10:1-4, 17. Kambiranani mmene malemba amenewa angatithandizire mu utumiki wathu.
Nyimbo Na. 57 ndi Pemphero