Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 8/12 tsamba 3
  • Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
km 8/12 tsamba 3

Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira August 27, 2012. Taikanso tsiku limene likusonyeza mlungu umene mfundoyo idzakambidwe.

1. Kodi masomphenya amene Ezekieli anaona onena za mzinda wa Yuda umene unali wampatuko ankaimira chiyani ndipo tikuphunzirapo mfundo yofunika iti? (Ezek. 8:15-17) [July 2, w07 7/1 tsa. 13 ndime 6; w93 1/15 tsa. 27 mpaka 28 ndime 7 ndi 12]

2. Kodi atsogoleri ambiri achipembedzo amatsanzira bwanji aneneri onyenga a m’nthawi ya Ezekieli? (Ezek. 13:3, 7) [July 9, w99 10/1 tsa. 13 ndime 14 ndi 15]

3. Pa ulosi wolembedwa pa Ezekieli 17:22-24, kodi “nsonga yanthete,” ikuimira ndani? Nanga “phiri lalitali” limene akubzalidwapo n’chiyani ndipo idzakhala bwanji “mtengo waukulu wa mkungudza”? [July 16, w07 7/1 tsa. 12 ndi 13 ndime 6]

4. Kodi tikuphunzira chiyani pa mwambi wopezeka pa Ezekieli 18:2? [July 23, w07 7/1 tsa. 13 ndime 10; Ezek. 18:20]

5. Kodi nkhani imene inalembedwa pa Ezekieli 21:18-22 imasonyeza bwanji kuti anthu kapena ziwanda sizingasinthe zolinga za Mulungu? [July 30, w07 7/1 tsa. 14 ndime 4]

6. Malinga ndi zimene zinalembedwa pa Ezekieli 24:6, 11, 12, kodi dzimbiri la mphika likuimira chiyani ndipo tikupeza mfundo yotani mu vesi 14? [Aug. 6, w07 7/1 tsa. 14 ndime 2]

7. N’chifukwa chiyani Yehova anawononga anthu a mumzinda wa Turo? Nanga ifeyo tikuphunzira chiyani pa mawu a pa Ezekieli 28:2-7? [Aug. 13, w08 6/1 tsa. 27 ndime 3 ndi 4]

8. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yehova anachitira Nebukadinezara zolembedwa pa Ezekieli 29:19, 20? [Aug. 13, w07 8/1 tsa. 9 ndime 1]

9. Kodi Iguputo anasanduka liti bwinja kwa zaka 40, ndipo tili ndi zifukwa ziti zokhulupirira kuti Iguputo anawonongedwadi? (Ezek. 29:8-12) [Aug. 13, w07 8/1 tsa. 8 ndime 5]

10. Kodi Ezekieli anachita zotani nthawi imene anthu analibe chidwi, ankamunyoza ndiponso sankamvetsera uthenga wake ndipo Yehova anamutsimikizira chiyani? (Ezek. 33:31-33) [Aug. 20, w91 3/15 tsa. 17 ndime 16 ndi 17]

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena