Ndandanda ya Mlungu wa September 3
MLUNGU WOYAMBIRA SEPTEMBER 3
Nyimbo Na. 75 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 11 ndime 13-19 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Ezekieli 39-41 (Mph. 10)
Na. 1: Ezekieli 40:17-31 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Maso Athu Angatisocheretse Bwanji?—Gen. 3:2-6 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Kusalowerera Ndale kwa Akhristu Kumasonyeza Kuti Safunira Zabwino Anthu Anzawo?—rs tsa. 374 ndime 2 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Kukambirana Ndi Anthu mu Utumiki—Mbali Yachiwiri. Nkhani yokambirana yochokera m’buku la Sukulu ya Utumiki tsamba 253, ndime 2 mpaka kumaliza tsamba 254. Chitani chitsanzo chachidule chosonyeza mmene tingagwiritsire ntchito mfundo imodzi kapena ziwiri za m’nkhaniyi.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini mu September. Nkhani yokambirana. Kwa masekondi 30 kapena 60, fotokozani chifukwa chake magaziniwo angakhale othandiza m’gawo lanu. Kenako, pogwiritsa ntchito nkhani zoyambirira za mu Nsanja ya Olonda, pemphani omvera kuti anene funso lochititsa chidwi ndiponso lemba limene angawerenge pogawira magaziniwo. Chitaninso chimodzimodzi ndi nkhani zoyambirira m’magazini ya Galamukani! Ngati nthawi ilipo mungachitenso zimenezi ndi nkhani ina imodzi m’magazini ya Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawirire magazini iliyonse.
Nyimbo Na. 34 ndi Pemphero