Phunziro la Baibulo la Mpingo ndi Msonkhano wa Utumiki Zasintha
Kuyambira ndi mlungu wa September 3, Phunziro la Baibulo la Mpingo lizichitika kwa mphindi 30 osati 25. M’mawu ake oyamba, m’bale amene akutsogolera phunziroli azifotokoza kwa mphindi imodzi mfundo zimene tinakambirana m’phunziro lapita. Nawonso Msonkhano wa Utumiki wasintha chifukwa uzichitika kwa mphindi 30 osati 35, ndipo sipazikhala nthawi yapadera ya zilengezo. M’malomwake, zilengezo ziziperekedwa kumayambiriro kwa nkhani yoyamba ya mu Msonkhano wa Utumiki. Ngati pali zilengezo zofunika kulengezedwa, ziyenera kukhala zochepa kwambiri, ndipo sipazifunika kulengeza mitu ya nkhani zimene zikambidwe mumsonkhanowu. Pa zilengezozi simuyenera kupereka moni, kulengeza za utumiki wakumunda, kapena amene akuyenera kuyeretsa Nyumba ya Ufumu. (km 10/08 tsa. 1, ndime 4) Ngati pakufunika kupereka chilengezo chachitali, amene ali ndi nkhani mumsonkhanowu azidziwitsidwa padakali nthawi, kuti afupikitse nkhani zawo.