Bokosi la Mafunso
◼ Kodi ndani ayenera kupereka zilengezo pa Msonkhano wa Utumiki?
Cholinga cha mbali imeneyi ya Msonkhano wa Utumiki ndicho kudziŵitsa mpingo zinthu zofunika pa utumiki wathu. Zilengezo zina zimakhala zongotikumbutsa zina ndi zina ndipo zimakhala zofanana mlungu ndi mlungu. Komabe, zilengezo zonse ziyenera kuŵerengedwa momveka bwino, ndipo si ziyenera kuperekedwa mosaikirapo mtima kapena mwamwambo.
Malinga ndi mmene zilengezo zina zimakhalira, zingafunike mkulu kuzipereka. Zikatere, umakhala udindo wa woyang’anira wotsogolera kukonza zoti mkulu woyenerera azipereke, ndipo mbale wina apereke zilengezo zina zimene zakonzedwa.
Ngati kalata imene ili ndi nkhani yokhudza mpingo ilinso ndi nkhani ina yokhudza akulu okha, mkulu ndiye ayenera kuŵerenga nkhani yokhudza mpingoyo. Makalata ena ochokera ku ofesi ya nthambi amene amakhala ndi malangizo a mpingo angakhale bwino atamaŵerengedwa ndi mkulu woyenerera. Makalata ngati amenewo angakhale okhudza ntchito yapadera yolemba makalata okhudza abale athu amene akuzunzidwa. Makalata ena angakhale ndi mfundo zambiri zokhudza zimene zimachitika m’gulu lathu monga maulendo a oyang’anira madera ndi misonkhano ikuluikulu.
Nthaŵi zina pangafunike kupereka chilengezo chofunika kwambiri chokhudza thanzi la mpingo, ndipo chilengezocho chiyenera kuperekedwa momveka bwino. Zingakhale bwino ngati zilengezo zotero zitamaperekedwa ndi mkulu.
Kaya olengezawo ndi akulu kapena atumiki otumikira, zilengezozo ziyenera kukhala zomveka bwino komanso zachidule. Kutsata mfundo zimenezi kudzathandiza kuti malangizo opita ku mpingo azimveka bwino ndi kuti onse azipita patsogolo mogwirizana.—Sal. 133:1; 1 Akor. 14:8, 9, 40.