Ndandanda ya Mlungu wa February 23
MLUNGU WOYAMBIRA FEBRUARY 23
Nyimbo Na. 109 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 9 ndime 1-7 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Oweruza 19-21 (Mph. 8)
Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
Msonkhano wa Utumiki:
Mutu wa Mwezi Uno: Khalani “Odzipereka pa Ntchito Zabwino”—Tito 2:14.
Mph. 10: Zofunika pampingo.
Mph. 10: Khalani Odzipereka pa Kulambira Koona Ngati Yesu. Nkhani yochokera mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 2013 tsamba 8 ndime 2 komanso ya December 15, 2010 tsamba 9-11 ndime 12-16. Fotokozani chifukwa chake ntchito yolalikira ndi imodzi mwa “ntchito zabwino” moti Mkhristu aliyense ayenera kuona kuti ndi mwayi kugwira nawo ntchitoyi. (Tito 2:14) Fotokozani mmene kudziwa choonadi kumatithandizira kuti tizifunitsitsa kuuza ena uthenga wabwino modzipereka komanso kuphunzira nawo Baibulo. Yamikirani mpingo wonse chifukwa cha kudzipereka kwawo pa ntchito zabwino.
Mph. 10: “Tizigwira Modzipereka Ntchito Yothandiza Ena Kudziwa Zoona Zokhudza Yesu.” Nkhani yokambirana. Chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akuchita zomwe zili mu “Chitsanzo 1,” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 2014, tsamba 8 ndime 8. Anenenso chitsanzo chomwe chili patsamba 9 ndime 13.
Nyimbo Na. 5 ndi Pemphero