Tizigwira Modzipereka Ntchito Yothandiza Ena Kudziwa Zoona Zokhudza Yesu
Tikadziwa zambiri zokhudza Yesu, zingakhale zosavuta kuti tiziphunzitsa anthu zokhudza Yesuyo modzipereka. Yesu ndi ‘mwala wapakona wa maziko’ pamene chikhulupiriro chenicheni chimamangidwa. (Aef. 2:20) Popanda Yesu, sitikanakhala ndi chiyembekezo chilichonse. (Mac. 4:12) Choncho, n’zofunika kwambiri kuti aliyense adziwe udindo wa Yesu pokwaniritsa cholinga cha Mulungu. Komatu anthu ambiri sadziwa zolondola zokhudza Yesu chifukwa anaphunzitsidwa zabodza. Zimenezi zingapangitse kuti asadzapeze madalitso amene Baibulo limanena kuti adzaperekedwa kwa anthu omwe amakhulupirira Yesu. Choncho, tikamalalikira modzipereka, tingathandize anthu a mitima yabwino kudziwa zoona zokhudza Yesu komanso udindo wake pokwaniritsa cholinga cha Mulungu. Kodi inuyo mudzalalikira modzipereka zokhudza Yesu pa nyengo ya Chikumbutso ikubwerayi?