Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, ya mlungu woyambira February 23, 2015.
Kodi mizinda yothawirako ya ku Isiraeli wakale inkasiyana bwanji ndi akachisi omwe zigawenga komanso othawa milandu ankakabisalako? (Yos. 20:2, 3) [Jan. 5, w10 11/1 tsa. 15 ndime 4-6]
N’chifukwa chiyani Yoswa ananena motsimikiza mawu omwe ali pa Yoswa 23:14? Nanga n’chifukwa chiyani ifenso tiyenera kukhulupirira ndi mtima wonse kuti zonse zomwe Yehova walonjeza zidzakwaniritsidwa? [Jan. 12, w07 11/1 tsa. 26 ndime 19]
N’chifukwa chiyani fuko la Yuda linasankhidwa kukhala loyamba kulandira dziko lomwe analigawira? (Ower. 1:2, 4) [Jan. 19, w05 1/15 tsa. 24 ndime 5]
N’chifukwa chiyani Baraki anaumirira kuti mneneri wamkazi Debora apite naye limodzi kunkhondo? (Ower. 4:8) [Jan. 19, w05 1/15 tsa. 25 ndime 4]
Kodi dzina limene Gidiyoni anapatsa guwa la nsembe lomwe anamanga likutiuza chiyani za Gidiyoniyo? Nanga ifeyo tikuphunzirapo chiyani? (Ower. 6:23, 24) [Jan. 26, w14 2/15 tsa. 22-23 ndime 9]
Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zimene Gidiyoni anachita pamene anthu a fuko la Efuraimu ankafuna kukangana naye? (Ower. 8:1-3) [Feb. 2, w05 7/15 tsa. 16 ndime 4]
Kodi Yefita ankaganiza zopereka nsembe ya munthu pamene ankanena lonjezo lake? (Ower. 11:30, 31) [Feb. 9, w05 1/15 tsa. 26 ndime 1]
Mogwirizana ndi zimene zili pa Oweruza 11:35-37, n’chiyani chinathandiza mwana wamkazi wa Yefita kukwaniritsa zimene bambo ake analonjeza Mulungu? [Feb. 9, w11 12/15 tsa. 20-21 ndime 15-16]
Pa nthawi yomwe ku Isiraeli kunalibe mfumu “aliyense anali kuchita zimene anali kuona kuti n’zoyenera.” Kodi zimenezi zinachititsa kuti kukhale chisokonezo? Fotokozani. (Ower. 17:6) [Feb. 16, w05 1/15 tsa. 27 ndime 8]
Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani yopitirizabe kupemphera kuchokera kwa Aisiraeli omwe anagonjetsedwa kawiri ndi fuko la Benjamini? (Ower. 20:14-25) [Feb. 23, w11 9/15 tsa. 32 ndime 1-4]