CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | YEREMIYA 35-38
Ebedi-meleki Ndi Chitsanzo Chabwino pa Nkhani ya Kulimba Mtima Komanso Kukoma Mtima
Ebedi-meleki, yemwe anali nduna m’nyumba ya Mfumu Zedekiya, anasonyeza makhalidwe abwino
Iye anachita zinthu molimba mtima komanso mosazengereza pokafotokozera Mfumu Zedekiya zimene zinachitikira Yeremiya ndipo kenako anakamutulutsa m’chitsime
Anasonyeza kukoma mtima pomupatsa Yeremiya nsanza zoti aike m’khwapa kuti zingwe zisamuvulaze