Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb25 January tsamba 6-7
  • January 27–February 2

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • January 27–February 2
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2025
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2025
mwb25 January tsamba 6-7

JANUARY 27–FEBRUARY 2

MASALIMO 140-143

Nyimbo Na. 44 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Muzichita Zinthu Mogwirizana ndi Mapemphero Anu Opempha Thandizo

(10 min.)

Muzikhala okonzeka kulandira malangizo kapena uphungu (Sl 141:5; w22.02 12 ¶13-14)

Muziganizira zimene Yehova anachita populumutsa anthu ake m’mbuyomu (Sl 143:5; w10 3/15 32 ¶4)

Muziyesetsa kuona zinthu mmene Yehova amazionera (Sl 143:10; w15 3/15 32 ¶2)

Zithunzi zosonyeza m’bale wachinyamata akuphunzira Baibulo payekha. 1. Akupemphera. 2. Akumvetsera malangizo a m’bale wachikulire amene akuyenda naye mu utumiki.

Mu Masalimo 140-143, muli mapemphero a Davide opempha thandizo komanso muli mawu osonyeza kuti iye ankachita zinthu mogwirizana ndi zimene ankapemphazo.

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 140:3—N’chifukwa chiyani Davide anayerekezera lilime la anthu oipa ndi lilime la njoka? (it-2 1151)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

(4 min.) Sl 141:1-10 (th phunziro 12)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Sinthani nkhani n’kuyamba kukambirana zokhudza Baibulo pambuyo pothandiza munthuyo m’njira inayake. (lmd phunziro 3 mfundo 5)

5. Ulendo Wobwereza

(3 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Munthuyo wakuuzani kuti ali bize. (lmd phunziro 7 mfundo 3)

6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

(5 min.) Chitsanzo. ijwfq 21—Mutu: N’chifukwa Chiyani Mumakana Kuikidwa Magazi? (th phunziro 7)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 141

7. Muzikonzekereratu Zimene Mudzachite Mukadzadwala Kapena Mukadzafunika Kuchitidwa Opaleshoni

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Yehova amalonjeza kuti iye ndi “thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya mavuto.” (Sl 46:1) Zimene zimachitika munthu akadwala kapena akafunika kuchitidwa opaleshoni zimayambitsa nkhawa. Komabe, Yehova anatipatsa zonse zomwe timafunikira pa zochitika ngati zimenezi. Mwachitsanzo, gulu lake linatipatsa khadi lopatsa munthu mphamvu zotiimira pa thandizo lakuchipatala (DPA), Khadi la Mwana,a mafomu ena a zachipatalab kuphatikizapo Makomiti Olankhulana ndi Achipatala (HLC). Zinthu zimenezi zimatithandiza kuti tizimvera lamulo la Mulungu lokhudza magazi.—Mac 15:28, 29.

Mlongo akulemba khadi la DPA.

Onerani VIDIYO yakuti Kodi Mwakonzekera Zimene Mudzachite Mukadzafunikira Thandizo la Chipatala? Kenako funsani mafunso otsatirawa:

  • Kodi kulemba fomu ya DPA kwathandiza bwanji anthu ena?

  • Kodi fomu yakuti Malangizo Othandiza Amayi Oyembekezera (S-401) inathandiza bwanji ena?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kuuza a HLC mwamsanga ngati taona kuti tikhoza kugonekedwa m’chipatala, kuchitidwa opaleshoni, kapena kulandira thandizo la matenda monga a khansa ngakhale zitaoneka kuti sizikhudzana ndi magazi?

KODI MWAKONZEKA?

  • Lembani zimene mwasankha pa khadi lanu la DPA

  • Muziuza a HLC mwamsanga

  • Muzikhala okonzeka kuuza adokotala anu zimene munasankha pa nkhani ya kuikidwa magazi, kugwiritsa ntchito tizigawo tina tamagazi kapena kugwiritsa ntchito magazi anu omwe pa nthawi imene akukuchitani opaleshoni.—onani buku la lff phunziro 39

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 21 ¶14-22

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 103 ndi Pemphero

a Ofalitsa obatizidwa angatenge khadi lawo la DPA kapena Khadi la Mwana kwa mtumiki wa mabuku.

b Mungapemphe kwa akulu ngati mukufuna fomu ya Malangizo Othandiza Amayi Oyembekezera (S-401), fomu ya Mfundo Zofunika Kukumbukira Tikafunika Thandizo la Opaleshoni Kapena la Matenda a Khansa (S-407), komanso fomu ya Mmene Makolo Angatetezere Ana Awo Kuti Asapatsidwe Magazi (S-55).

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena