APRIL 28–MAY 4
MIYAMBO 11
Nyimbo Na. 90 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Musamalankhule
(10 min.)
Musamalankhule chilichonse chimene chikhoza kuwononga ‘mnzanu’ (Miy 11:9; w02 5/15 26 ¶4)
Musamalankhule zinthu zimene zingayambanitse anthu, kapena zimene zikunena zoipa za munthu wina, komanso musamangokhalira kudandaula (Miy 11:11; w02 5/15 27 ¶3-4)
Musamalankhule nkhani zachinsinsi za ena (Miy 11:12, 13; w02 5/15 27 ¶6)
FUNSO LOFUNIKA KULIGANIZIRA: Kodi mawu a Yesu opezeka pa Luka 6:45 angatithandize bwanji kuti tizilankhula bwino?
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Miy 11:17—Kodi ifeyo zinthu zimatiyendera bwanji tikakhala okoma mtima? (g20.1 11, bokosi)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Miy 11:1-20 (th phunziro 5)
4. Ulendo Woyamba
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Pezani mwayi woti mumuuze zimene munaphunzira pamisonkhano yampingo yaposachedwapa. (lmd phunziro 2 mfundo 4)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Gwiritsani ntchito vidiyo yopezeka pa Zinthu Zophunzitsira. (lmd phunziro 8 mfundo 3)
6. Kuphunzitsa Anthu
(4 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. M’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo ndipo musonyezeni mmene phunziroli limachitikira. (lmd phunziro 10 mfundo 3)
Nyimbo Na. 157
7. Musalole Kuti Lilime Lanu Lizisokoneza Mtendere
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Chifukwa choti ndife opanda ungwiro, nthawi zina timalankhula zolakwika. (Yak 3:8) Komabe, kuganizira mavuto amene amabwera chifukwa cholankhula zolakwika, kumatithandiza kupewa kulankhula zinthu zimene pamapeto pake tinganong’oneze nazo bondo. Tiyeni tione zinthu zina zofunika kupewa zomwe tikalankhula zingasokoneze mtendere mumpingo.
Kudzitamandira. Munthu akamadzitamandira amadzionetsa kuti ndi wapamwamba kwambiri zomwe zingayambitse mpikisano komanso nsanje.—Miy 27:2
Kusalankhula zoona. Kusalankhula zoona sikutanthauza kunena bodza kokha komanso ngakhale kunena zinthu zomwe zingasocheretse ena. Kusalankhula zoona ngakhale pa nkhani yaing’ono kungachititsenso kuti ena asiye kukukhulupirirani komanso kungawononge mbiri yanu.—Mla 10:1
Miseche. Munthu wamiseche amakamba nkhani zabodza za ena kapena amaulula zinsinsi za ena. (1Ti 5:13) Zimenezi zingayambitse mikangano komanso zingachititse kuti anthu asamagwirizane
Mawu aukali. Munthu amalankhula mawu aukali akalephera kudziletsa pamene wakwiya ndi zimene winawake wachita kapena kulankhula. (Aef 4:26) Mawu aukali amapweteka.—Miy 29:22
Onerani VIDIYO yakuti Muzipewa Zinthu Zomwe Zingasokoneze Mtendere—Kachigawo Kake. Kenako funsani funso lotsatirali:
Kodi mwaphunzira chiyani pa mmene mawu athu angasokonezere mosavuta mtendere mumpingo?
Kuti muone mmene ena anabwezeretsera mtendere, onerani vidiyo yakuti Muzifunafuna “Mtendere ndi Kuusunga.”
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 25 ¶14-21