MAY 19-25
MIYAMBO 14
Nyimbo Na. 89 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Muziganizira Zimene Mungachite Kukachitika Ngozi
(10 min.)
Muzisamala kuti musamangokhulupirira “mawu alionse” amene mungamve (Miy 14:15; w23.02 22-23 ¶10-12)
Musamadalire mmene mukumvera kapena zimene zinakuchitikirani m’mbuyomu (Miy 14:12)
Musamamvere zonena za anthu amene amakana malangizo ochokera ku gulu la Yehova (Miy 14:7)
FUNSO LOFUNIKA KULIGANIZIRA: Akulu, kodi ndinu okonzeka kutsatira malangizo komanso kudalira Yehova pa nthawi ya ngozi?—w24.07 5 ¶11.
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Miy 14:1-21 (th phunziro 11)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Kambiranani mfundo inayake ya m’Baibulo ndi munthu amene wakuuzani kuti akuda nkhawa ndi mavuto azachuma. (lmd phunziro 3 mfundo 3)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. M’patseni magazini imene ili ndi nkhani imene anachita nayo chidwi pa ulendo wapita. (lmd phunziro 9 mfundo 4)
6. Kuphunzitsa Anthu
(5 min.) Limbikitsani wophunzira wanu kuti aziwerenga Baibulo tsiku lililonse ndipo musonyezeni zimene angachite kuti akwaniritse cholinga chimenechi. (th phunziro 19)
Nyimbo Na. 126
7. Pitirizani Kukonzekera Zimene Mudzachite pa Nthawi ya Ngozi
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Ikambidwe ndi mkulu. Tchulani zilengezo zochokera ku ofesi ya nthambi kapena ku bungwe la akulu ngati zilipo.
Popeza tikukhala ‘m’masiku otsiriza,’ tikudziwa kuti tizikumanabe ndi mavuto ambiri. (2Ti 3:1) Kukachitika ngozi, anthu a Yehova nthawi zambiri amalandira malangizo a pa nthawi yake komanso amene amawathandiza kuti apulumuke. Choncho kuti tidzapulumuke pa nthawi imeneyo, zikudalira ngati panopa timamvera malangizo oti tizikhala okonzeka, omwe ndi kuchita zinthu zomwe zingatithandize kukhala ndi chikhulupiriro cholimba komanso kukonzeratu zinthu zimene tingadzafunikire ngoziyo ikadzachitika.—Miy 14:6, 8.
Muzikonzekera mwauzimu: Muziwerenga komanso kuphunzira Baibulo panokha nthawi zonse. Muzikulitsa luso lanu logwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana zolalikirira. Musamade nkhawa ngati kwa kanthawi mukufunika kusiya kaye kuchita zinthu limodzi ndi anthu a mumpingo wanu chifukwa cha ngozi zadzidzidzi. (Miy 14:30) Palibe amene angakulekanitseni ndi Yehova Mulungu komanso Khristu Yesu.—od 176 ¶15-17
Muzikonzekera mwakuthupi: Kuwonjezera pa kukhala ndi chikwama cha pangozi, banja lililonse lizisunga chakudya chokwanira, madzi, mankhwala komanso zinthu zina zofunika zomwe angadzagwiritse ntchito ngati angadzafunike kuti asachoke panyumba kwa kanthawi ndithu.—Miy 22:3; g17.5 4
Onerani VIDIYO yakuti Kodi Mwakonzeka Kukumana ndi Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi? Kenako funsani mafunso otsatirawa:
Kodi Yehova angatithandize bwanji pa nthawi ya ngozi?
Kodi tingakonzekere bwanji?
Kodi tingathandize bwanji anthu amene akhudzidwa ndi ngozizi?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 26 ¶18-22, bokosi patsamba 209