MAY 26–JUNE 1
MIYAMBO 15
Nyimbo Na. 102 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Muzithandiza Ena Kukhala Osangalala
(10 min.)
Abale athu akakumana ndi mavuto aakulu, amamva ngati masiku awo onse ndi oipa (Miy 15:15)
Muzichereza anthu amene akukumana ndi mavuto (Miy 15:17; w10 11/15 31 ¶16)
“Kuyang’ana munthu ndi nkhope yachimwemwe” komanso kulankhula mawu olimbikitsa kungamuthandize kwambiri (Miy 15:23, 30, mawu a m’munsi; w18.04 23-24 ¶16-18)
DZIFUNSENI KUTI: ‘Kodi ndi ndani mumpingo wathu amene angafunike kulimbikitsidwa? Nanga ineyo ndingamuthandize bwanji?’
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Miy 15:22—Kodi mfundo ya palembali ingatithandize bwanji kusankha mwanzeru thandizo lachipatala? (ijwbq nkhani na. 39 ¶3)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Miy 15:1-21 (th phunziro 2)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. (lmd phunziro 1 mfundo 5)
5. Ulendo Woyamba
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. M’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 2 mfundo 4)
6. Kuphunzitsa Anthu
(5 min.) Limbikitsani wophunzira wanu amene akutsutsidwa ndi anthu a m’banja lake. (th phunziro 4)
Nyimbo Na. 155
7. Tikhoza Kukhalabe Osangalala Ngakhale Pamene Tikukumana ndi Mavuto
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Onerani VIDIYO yakuti Tikhoza Kumasangalalabe Ngakhale Kuti Tikukumana ndi Zowawa, Tikuvutika ndi Njala Komanso Tikuvutika ndi Usiwa. Kenako funsani funso lotsatirali:
Kodi mwaphunzira chiyani kuchokera pa zimene zinachitikira anthuwa?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 27 ¶1-9