JUNE 9-15
MIYAMBO 17
Nyimbo Na. 157 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
Banja la Chiisiraeli lomwe limakhala mwamtendere likudya chakudya mosangalala
1. Muzikhala Mwamtendere M’banja Lanu
(10 min.)
Kuti m’banja mukhale mtendere pamafunika khama, ndipo khama limenelo silipita pachabe (Miy 17:1; onani chithunzi)
Muzipewa kumangokangana pa nkhani zing’onozing’ono (Miy 17:9; g 9/14 11 ¶2)
Muzilamulira mkwiyo wanu (Miy 17:14; w08 5/1 10 ¶6–11 ¶1)
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Miy 17:24—Kodi “maso a munthu wopusa amangoyendayenda mpaka kumalekezero a dziko lapansi” m’njira yotani? (it-1 790 ¶2)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Miy 17:1-17 (th phunziro 10)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. (lmd phunziro 3 mfundo 5)
5. Ulendo Woyamba
(4 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. M’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 6 mfundo 4)
6. Nkhani
(5 min.) ijwbv nkhani na. 60—Mutu: Kodi Lemba la Miyambo 17:17 Limatanthauza Chiyani? (th phunziro 13)
Nyimbo Na. 113
7. Muzikulitsa Makhalidwe Amene Angakuthandizeni Kuti Muzilankhulana Bwino
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Kulankhulana bwino ndi kumene kumathandiza kuti banja lizikhala losangalala. Ngati anthu amalankhulana momasuka m’banja, akhoza kukwaniritsa zolinga zawo komanso akhoza kuthandizana mosavuta akakumana ndi mavuto. (Miy 15:22) Kodi mungatani kuti muzilankhulana momasuka m’banja lanu?
Muzikhala ndi nthawi yochitira zinthu limodzi. (De 6:6, 7) Mabanja akamachitira limodzi zinthu zokhudza kulambira, zosangalatsa komanso zinthu zina, ubwenzi wawo umalimba ndipo amakondana komanso kukhulupirirana kwambiri. Zimenezi zimawapatsanso mwayi woti azikambirana zinthu zina momasuka. Nthawi zina mungafunike kusintha zinthu zimene mumakonda n’cholinga choti muchite zinthu zimene anthu a m’banja lanu akufuna ndipo zotsatira zake zimakhala zabwino kwambiri. (Afi 2:3, 4) Kodi mungatani kuti muzigwiritsa ntchito bwino nthawi imene mumakhala muli limodzi?—Aef 5:15, 16.
Onerani VIDIYO yakuti Zimene Zingathandize Kuti M’banja Muzikhala Mtendere—Muzilankhulana Nthawi Zonse. Kenako funsani mafunso otsatirawa:
Kodi kugwiritsa ntchito molakwika zipangizo zamakono kungalepheretse bwanji kulankhulana m’banja?
Kodi mwaphunziranso chiyani muvidiyoyi pa nkhani ya kulankhulana bwino?
Muzimvetsera bwino. (Yak 1:19) Ana savutika kufotokoza mmene akumvera ngati akudziwa kuti simuwaweruza kapena kuwamva molakwika. Choncho muziyesetsa kuti musamapse mtima msanga mwana wanu akamakufotokozerani zinazake. (Miy 17:27) M’malomwake muzimvetsera mwachifundo. Muziyesetsa kumvetsa mmene akuganizira komanso mmene akumvera mumtima n’cholinga choti mumuthandize mwachikondi.
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 27 ¶19-22, bokosi patsamba 212