JUNE 16-22
MIYAMBO 18
Nyimbo Na. 90 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Muzilankhula Mawu Olimbikitsa kwa Anthu Amene Akudwala
(10 min.)
Muzilola kuti nzeru yochokera kwa Mulungu izikuthandizani kudziwa zimene mungalankhule (Miy 18:4; w22.10 22 ¶17)
Muziyesetsa kumvetsa zimene munthuyo akukumana nazo (Miy 18:13; mrt nkhani na. 19 bokosi)
Muzikhala bwenzi lothandiza komanso loleza mtima (Miy 18:24; wp23.1 14 ¶3–15 ¶1)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndingathandize bwanji mkazi kapena mwamuna wanga ngati akudwala matenda enaake kapena ngati ali ndi vuto linalake la mu ubongo?’
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Miy 18:18—N’chifukwa chiyani anthu a m’nthawi za m’Baibulo ankachita maere? (it-2 271-272)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Miy 18:1-17 (th phunziro 11)
4. Ulendo Woyamba
(1 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Munthuyo amalankhula chilankhulo china. (lmd phunziro 2 mfundo 5)
5. Ulendo Wobwereza
(3 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Mwininyumba wakuuzani kuti ali ndi nthawi yochepa. (lmd phunziro 7 mfundo 4)
6. Ulendo Wobwereza
(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. M’phunzitseni mfundo yofunika ya choonadi yokhudza Ufumu wa Mulungu. (lmd phunziro 9 mfundo 5)
7. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira
(4 min.) Chitsanzo. ijwfq nkhani na. 29—Mutu: Kodi Mumakhulupirira Kuti Dzikoli Linalengedwa M’masiku 6 Enieni? (lmd phunziro 5 mfundo 5)
Nyimbo Na. 144
8. Kuthandiza Anthu Amene Mumawakonda Kukhala Anzake a Yehova Popanda Kulankhula
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Ambirife tikudziwa munthu wina amene panopa satumikira Yehova. Mwina mwamuna kapena mkazi wathu, mwana wathu kapena mnzathu amene tinkamukonda koma anasiya kutumikira Yehova. Kodi munazindikira kuti nthawi zina mumachita zinthu mokakamiza mwinanso mwamwano kumene poyesa kumuthandiza kuti ayambirenso kutumikira Yehova? N’zoona kuti tingakhale ndi zolinga zabwino, koma mawu athu akhoza kuwononga zinthu. (Miy 12:18) Ndiye kodi njira yabwino yomuthandizira ingakhale iti?
Lemba la 1 Petulo 3:1 limanena kuti mwamuna wosakhulupirira akhoza kukopeka “osati ndi mawu” okha. Ngakhale mwamuna wa mlongo wa Chikhristu atamakana kukambirana naye mfundo za choonadi cha m’Baibulo, akhozabe kumuthandiza kudziwa Yehova. Zochita za mlongoyo zomwe zimatsogoleredwa ndi makhalidwe abwino monga chikondi, ubwino ndi nzeru zikhoza kufewetsa mtima wa mwamuna wakeyo. (Miy 16:23) Kuchita zinthu mokoma mtima ndi anthu amene timawakonda koma satumikira Yehova kukhoza kukhala ndi zotsatira zabwino.
Onerani VIDIYO yakuti Anthu Omwe Apambana pa Nkhondo Yachikhulupiriro—Amene Ali pa Banja Ndi Munthu Wosakhulupirira. Kenako funsani mafunso otsatirawa:
Kodi mwaphunzira chiyani kuchokera pa zimene zinachitikira Mlongo Sasaki?
Kodi mwaphunzira chiyani kuchokera pa zimene zinachitikira Mlongo Ito?
Kodi mwaphunzira chiyani kuchokera pa zimene zinachitikira Mlongo Okada?
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 27 ¶23-26, bokosi patsamba 214 ndi 217