Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • mwb25 September tsamba 2
  • September 1-7

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • September 1-7
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2025
Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Kabuku ka Msonkhano—2025
mwb25 September tsamba 2

SEPTEMBER 1-7

MIYAMBO 29

Nyimbo Na. 28 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Muzikana Miyambo Kapena Zikhulupiriro Zomwe Sizisangalatsa Mulungu

(10 min.)

Mukamamvera Yehova, mumasangalaladi (Miy 29:18; wp16.6 6, bokosi)

Muzidalira nzeru za Mulungu kuti mudziwe ngati mwambo winawake umamusangalatsa kapena ayi (Miy 29:3a; w19.04 17 ¶13)

Musamalole kuti anthu ena akukakamizeni kuchita miyambo yomwe sisangalatsa Mulungu (Miy 29:25; w18.11 11 ¶12)

1. M’bale akulemba notsi pamene akufufuza pogwiritsa ntchito Baibulo komanso buku lakuti “Malemba Othandiza pa Moyo wa Chikhristu.” 2. M’bale yemwe uja akufotokoza zimene amakhulupirira kwa achibale ake omwe si a Mboni. Achibale ena akumvetsera mwachidwi, pomwe ena akuoneka kuti sakumvetsa zimene m’baleyo akunena.

Kufufuza mfundo za m’Baibulo mosamala kwambiri komanso kukambirana ndi achibale omwe si a Mboni, kungakuthandizeni kupewa miyambo imene sisangalatsa Mulungu

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Miy 29:5—Kodi kuyamikira mwachiphamaso n’kutani, nanga munthu amene amachita zimenezi amayalira bwanji ukonde mapazi ake? (it “Kuyamikira Mwachiphamaso” ¶1)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

(4 min.) Miy 29:1-18 (th phunziro 5)

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Muitanireni kuti adzamvetsere nkhani yapadera. (lmd phunziro 2 mfundo 3)

5. Ulendo Woyamba

(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Gwiritsani ntchito Nsanja ya Olonda Na. 1 2025 kuti muyambe kukambirana ndi munthu. Sinthani nkhani yomwe mukukambirana kuti igwirizane ndi nkhani yomwe munthuyo ali nayo chidwi. (lmd phunziro 3 mfundo 3)

6. Ulendo Woyamba

(5 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Perekani magazini ya Nsanja ya Olonda Na. 1 2025 kwa munthu amene akudera nkhawa zokhudza nkhondo. (lmd phunziro 3 mfundo 4)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 159

7. Zofunika Pampingo

(15 min.)

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) lfb mawu oyamba gawo 4 komanso mutu 14-15

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 31 ndi Pemphero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena