OCTOBER 20-26
MLALIKI 9-10
Nyimbo Na. 30 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Muziona Mavuto Anu Moyenera
(10 min.)
Timadziwa kuti mavuto si chizindikiro choti Yehova sakusangalala nafe (Mla 9:11; w13 8/15 14 ¶20-21)
Sitiyembekezera kuti tizikhala moyo wopanda mavuto m’dziko la Satanali (Mla 10:7; w19.09 5 ¶10)
Tizipeza nthawi yosangalala ndi mphatso zimene Yehova amatipatsa ngakhale pamene tikukumana ndi mavuto (Mla 9:7, 10; w11 10/15 8 ¶1-2)
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Mla 10:12-14—Kodi mavesiwa akutichenjeza chiyani pa nkhani ya miseche? (it “Miseche, Kunenera Ena Zoipa” ¶4, 8)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Mla 10:1-20 (th phunziro 11)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Yambani kukambirana ndi munthu amene akuoneka kuti wakhumudwa. (lmd phunziro 3 mfundo 4)
5. Ulendo Woyamba
(4 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Kambiranani nkhani imodzi yopezeka pagawo lakuti “Choonadi Chomwe Timakonda Kuphunzitsa Anthu” mu zakumapeto A, m’kabuku ka lmd ndi munthu amene wakuuzani kuti akuda nkhawa chifukwa cha mavuto a zachuma. (lmd phunziro 4 mfundo 4)
6. Kuphunzitsa Anthu
Nyimbo Na. 47
7. Kukhalabe Olimba pa Nthawi ya Mavuto
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Tsiku lililonse timakumana ndi mavuto komanso mayesero. Komabe, mayesero ena amabwera mosayembekezereka moti timasowa mtendere, timasokonezeka maganizo komanso timafooka mwauzimu. Kodi tingatani kuti tikhalebe olimba pamene takumana ndi mavuto?
Kaya tikumane ndi mavuto otani, nthawi zonse Yehova ‘amachititsa kuti tizimva kuti ndife otetezeka.’ (Yes 33:6) Kuti tizidalira Yehova, timafunika kumaona zinthu moyenera komanso kukhala odzichepetsa. (Miy 11:2) Ngati takumana ndi mavuto aakulu, tingafunike kudzipatsa nthawi kuti tisankhe zinthu mwanzeru, tidzisamalire kapena kusamalira okondedwa athu komanso tingafunike kudzipatsa nthawi kuti tilire. (Mla 4:6)
Chifukwa choti Yehova amagwiritsa ntchito atumiki ake kuti alimbikitsane, tizikhala okonzeka kupempha kapena kulandira thandizo. Muzikumbukira kuti Akhristu anzanu amakukondani kwambiri ndipo amasangalala kwambiri akakuthandizani.
Werengani 2 Akorinto 4:7-9. Kenako funsani funso ili:
N’chifukwa chiyani tiyenera kupitiriza kuchita zinthu zokhudza kulambira mokhazikika ngakhale pamene kuchita zimenezi kungakhale kovuta?
Onerani VIDIYO yakuti Yehova Ali Pafupi ndi Anthu a Mtima Wosweka. Kenako funsani mafunso awa:
Kodi Yehova anathandiza bwanji M’bale ndi Mlongo Septer?
Kodi Akhristu anzawo anawathandiza bwanji?
Kodi mwaphunziranso chiyani kuchokera pa chitsanzo chawo?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 28, mawu oyamba gawo 6 komanso mutu 29