OCTOBER 13-19
MLALIKI 7-8
Nyimbo Na. 39 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. ‘Muzipita Kunyumba Yamaliro’
(10 min.)
Muzipeza nthawi yotonthoza anthu amene akulira (Mla 7:2; it “Kulira” ¶9)
Muzitonthoza anthu amene aferedwa powauza zinthu zabwino zimene womwalirayo ankachita (Mla 7:1; w19.06 23 ¶15)
Muzipemphera ndi anthu amene akulira (w17.07 16 ¶16)
KUMBUKIRANI: Anthu amene okondedwa awo amwalira, nthawi zambiri amafunikabe kuthandizidwa ndi Akhristu anzawo kwa nthawi ndithu pambuyo pa imfayo.—w17.07 16 ¶17-19.
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Mla 7:20-22—Kodi mavesiwa angatithandize bwanji kudziwa ngati tikuyenera kufunsa munthu amene watinenera zoipa? (w23.03 31 ¶18)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Mla 8:1-13 (th phunziro 10)
4. Ulendo Woyamba
(2 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Pezani nkhani yomwe ingasangalatse munthuyo ndipo konzani zoti mudzakumanenso. (lmd phunziro 2 mfundo 4)
5. Ulendo Woyamba
(2 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. (lmd phunziro 2 mfundo 3)
6. Ulendo Wobwereza
(2 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Muonetseni chimodzi mwa zinthu zopezeka pa webusaiti yathu ya jw.org. (lmd phunziro 9 mfundo 4)
7. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira
(5 min.) Chitsanzo. ijwfq nkhani na. 50—Mutu: Kodi N’chiyani Chimachitika pa Maliro a Mboni za Yehova? (th phunziro 17)
Nyimbo Na. 151
8. Muzilimbitsa Chikhulupiriro Chanu Choti Akufa Adzauka
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Lonjezo la Yehova lakuti akufa adzauka ndi limodzi mwa malonjezo a mtengo wapatali kwambiri kwa ife. Limatiphunzitsa za makhalidwe ake abwino monga, mphamvu, nzeru, chifundo komanso chikondi chimene amasonyeza aliyense payekha.—Yoh 3:16.
Tikamakhulupirira kwambiri kuti akufa adzauka, sitimadera nkhawa kwambiri za mavuto amene tikukumana nawo. (2Ak 4:16-18) Chiyembekezo chimenechi chingatipatsenso mtendere komanso kutilimbikitsa pamene tikuzunzidwa, tikudwala kapena pamene wokondedwa wathu wamwalira. (1At 4:13) Sitingamasangalale ngati sitikhulupirira kuti akufa adzauka. (1Ak 15:19) Ndiye nthawi zonse muziyesetsa kulimbitsa chikhulupiriro chanu chimenechi.
Werengani Yohane 11:21-24. Kenako funsani mafunso awa:
Kodi Marita anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira kwambiri kuti akufa adzauka?
Kodi anadalitsidwa bwanji chifukwa cha chikhulupiriro chakechi?—Yoh 11:38-44
Onerani VIDIYO yakuti Tsanzirani Akazi a Chikhulupiriro Cholimba—Marita. Kenako funsani mafunso awa:
N’chifukwa chiyani chiyembekezo chakuti akufa adzauka n’chofunika kwambiri kwa inu?
Kodi mungatani kuti chikhulupiriro chanu chakuti akufa adzauka chikhalebe cholimba kwambiri?
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 26-27