NOVEMBER 3-9
NYIMBO YA SOLOMO 1-2
Nyimbo Na. 132 ndi Pempher | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Nkhani ya Chikondi Chenicheni
(10 min.)
[Onerani VIDIYO yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Nyimbo ya Solomo.]
Solomo anayamikira kwambiri Msulami ndipo anamulonjeza kuti amupatsa zinthu zamtengo wapatali (Nym 1:9-11)
Chifukwa chakuti Msulami ankakonda kwambiri m’busa, iye anakhalabe wokhulupirika kwa m’busayo (Nym 2:16, 17; w15 1/15 30 ¶9-10)
ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI: Kuti mudziwe amene akulankhula mukamawerenga buku la Nyimbo ya Solomo, muzigwiritsa ntchito gawo la mu Baibulo la Dziko Latsopano lakuti “Zimene Zili M’bukuli.”
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Nym 2:7-N’chifukwa chiyani Msulami ndi chitsanzo chabwino kwa Akhristu omwe sali pabanja? (w15 1/15 31 ¶11)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Nym 2:1-17 (th phunziro 12)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambiranani mfundo imodzi ya choonadi mu zakumapeto A, m’kabuku kakuti Muzikonda Anthu. (lmd phunziro 1 mfundo 3)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambiranani mfundo imodzi ya choonadi mu zakumapeto A, m’kabuku kakuti Muzikonda Anthu. (lmd phunziro 9 mfundo 3)
6. Kuphunzitsa Anthu
Nyimbo Na. 46
7. “Munthu Wowolowa Manja Adzadalitsidwa”
(15 min.) Nkhani yokambirana. Ikambidwe ndi mkulu.
Tikamagwiritsa ntchito nthawi, mphamvu komanso zinthu zathu pothandiza ena, timadalitsidwa kwambiri. N’zoona kuti munthu akalandira mphatso amaiona kuti ndi dalitso, koma amene waperekayo nayenso amadalitsidwa. (Miy 22:9) Munthu amene amachita zimenezi amakhala wosangalala chifukwa chakuti akutsanzira Yehova ndipo Yehovayo amasangalala naye.—Miy 19:17; Yak 1:17.
Onerani VIDIYO yakuti Kuwolowa Manja Kumatithandiza Kukhala Osangalala. Kenako funsani mafunso awa:
Kodi anthu a muvidiyoyi anasangalala bwanji chifukwa cha kuwolowa manja kwa abale ndi alongo padziko lonse lapansi?
Kodi anthuwa anamva bwanji chifukwa chakuti nawonso anathandiza ena mowolowa manja?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 32-33