NOVEMBER 10-16
NYIMBO YA SOLOMO 3-5
Nyimbo Na. 31 ndi Pemphero Mawu Oyamba (1 min.)
1. Kukongola kwa Mumtima Ndi Kofunika
(10 min.)
Kukongola kwa mumtima kwa Msulami kunkaonekera mu zolankhula zake (Nym 4:3, 11; w15 1/15 30 ¶8)
Makhalidwe ake abwino, ankayerekezeredwa ndi munda wa maluwa wokongola kwambiri (Nym 4:12; w00 11/1 11 ¶17)
Aliyense akhoza kukhala wokongola mumtima, zomwe ndi zofunika kwambiri kuposa kukongola kwa kunja (g05 1/8 25 ¶2-5)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndi makhalidwe auzimu ati amene ndimachita nawo chidwi mwa anthu ena?’
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Nym 3:5—N’chifukwa chiyani “ana aakazi a ku Yerusalemu” analumbiritsidwa “pali insa ndiponso pali mphoyo zakutchire”? (w06 11/15 18 ¶4)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Nym 4:1-16 (th phunziro 2)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. M’pempheni mwachindunji kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 6 mfundo 4)
5. Ulendo Woyamba
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Muonetseni mmene angapezere zinthu m’chilankhulo chake pa jw.org. (lmd phunziro 4 mfundo 3)
6. Nkhani
(5 min.) ijwbq nkhani Na. 131—Mutu: Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani ya Kudziphoda Komanso Kuvala Zodzikongoletsera? (th phunziro 1)
Nyimbo Na. 36
7.Kwatirani mwa Ambuye (Ge 28:2)
(8 min.)
8. Kodi Mudzakhala Mwamuna Kapena Mkazi Wabwino kwa Munthu Amene Mudzakwatirane Naye?
(7 min.) Nkhani yokambirana.
Kodi mukufunafuna mkazi kapena mwamuna woti mukwatirane naye? Kodi inuyo muli ndi makhalidwe auzimu omwe Akhristu ena amene akufuna wokwatirana naye angasangalale nawo? Ngakhale kuti poyamba munthu akhoza kumachita zinthu ngati wauzimu, koma m’kupita kwa nthawi makhalidwe ake enieni amaonekera.
M’munsimu, lembani vesi la m’Baibulo logwirizana ndi makhalidwe amene munthu wauzimu amasonyeza.
Kukonda Yehova ndi kumukhulupirira
Kukhala mutu wabanja wabwino, kapena mkazi amene angamalemekeze mwamuna wake
Kusadzikonda ndi kukhala ndi chikondi chovutikira ena
Kuganiza bwino, kudziwa malire komanso kulolera
Khama ndiponso kulimbikira ntchito
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 34-35