NOVEMBER 24-30
YESAYA 1-2
Nyimbo Na. 44 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Chiyembekezo kwa “Olemedwa Ndi Zolakwa”
(10 min.)
[Onerani VIDIYO yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la Yesaya.]
Anthu a Mulungu anali “olemedwa ndi zolakwa” (Yes 1:4-6; ip-1 14 ¶8)
Yehova anali wofunitsitsa kuwakhululukira ngati akanalapa mochokera pansi pa mtima (Yes 1:18; ip-1 28-29 ¶15-17)
FUNSO LOFUNIKA KULIGANIZIRA: Kodi zimene Yehova anauza mtundu wa Aisiraeli, zingatilimbikitse bwanji ngati tikuda nkhawa kuti machimo athu ndi aakulu kwambiri moti sitingakhululukidwe?
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Yes 2:2—Kodi “phiri la nyumba ya Yehova” limaimira chiyani? (ip-1 39 ¶9)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Yes 2:1-11 (th phunziro 11)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambiranani mfundo imodzi yopezeka mu zakumapeto A, m’kabuku kakuti Muzikonda Anthu. (lmd phunziro 3 mfundo 3)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.)KUNYUMBA NDI NYUMBA. Mwininyumbayo akufuna kuti mukambirane nkhani ina yosiyana ndi imene munagwirizana kuti mudzakambirana. (lmd phunziro 7 mfundo 4)
6. Nkhani
(5 min.) ijwbq nkhani Na. 96—Mutu: Kodi Tchimo N’chiyani? (th phunziro 20)
Nyimbo Na. 38
7. Khalani Bwenzi la Yehova—Yehova Amakhululuka
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Onerani VIDIYO. Kenako ngati n’zotheka, itanani ana amene munawasankhiratu kuti abwere papulatifomu ndipo afunseni mafunso okhudza vidiyoyi komanso zimene aphunzirapo.
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) lfb mutu 38, mawu oyamba a gawo 7, komanso mutu 39